Nyimbo 67
Kundikani Chuma Mmwamba
1. Timukondetu Yehova,
Tate wa mauniko!
Mphatso zonse zabwinozi,
Zichokera kwa iye.
Zovala, chakudya, mbewu,
Nthaka, dzuŵa ndi mvula.
Tiyamikire Mgaŵiri;
Asunga moyo wathu.
2. Ndikupusa kumataya
Nthaŵi yathu mudyera,
Kuunjika chuma chino,
Chosatipatsa moyo!
Tikhale okhutira ndi
Zinthu zofunikadi,
Mwantchito zathu zabwino
Tigwirire moyodi.
3. Tigwiritse nthaŵi yathu
Kuwadyetsa “amphaŵi,”
Kupatsa “anjala” mbiri
Yabwino ya Ufumu.
Mwautumiki tikhala
Abwenzi a Mulungu;
Kusonkhanitsira m’mwamba
Chuma cha umuyaya.