Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
Dziko limafuna kuti ife tizikhulupirira kuti dongosolo la zinthu lilipoli silidzatha. Komabe, Mawu a Mulungu amatiuza zosiyana ndi zimenezi. (1 Yoh. 2:15-17) Amatithandiza kuzindikira kuti ‘kudzikundikira chuma padziko lapansi’ n’kungodzivutitsa chabe. Pofuna kulimbikitsa anthu a Mulungu, pulogalamu ya msonkhano wadera ya chaka chautumiki cha 2007 ili ndi mutu wakuti “Kundikani Chuma . . . Kumwamba.”—Mat. 6:19, 20.
Mtima woganizira kwambiri chuma uli m’gulu la zinthu zotchulidwa pa Aefeso 2:2 kuti “mphamvu ya mumpweya, mzimu umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” Mpweya weniweni umapezeka paliponse, moti aliyense angaupume mosavuta, moteronso “mzimu wa dziko” uli paliponse m’dongosolo lino. (1 Akor. 2:12) Popeza kuti umatha kusocheretsa munthu mosavuta, Baibulo limati uli ndi “mphamvu.” Pulogalamu ya msonkhano wadera udzatithandiza kupewa mtima wa dzikoli wokonda chuma ndi kutithandiza kuika maganizo athu pa zinthu zofunikira kwambiri. (Mat. 6:33) Kuphatikiza pa zimenezo, pulogalamuyi idzatithandiza kudalira Yehova pochita utumiki wathu ngakhale tikamakumana ndi mavuto ndi mayesero osiyanasiyana.
Yesetsani kupezeka pa msonkhanowu masiku onse awiri ndi ‘kusamalira mwapadera, koposa mwa nthawi zonse.’ (Aheb. 2:1) Lembani notsi zachidule za mfundo zimene mungagwiritsire ntchito panokha m’moyo wanu ndi muutumiki. Mukadzapezeka pa msonkhano wolimbikitsa mwauzimuwu kuchokera kumayambiriro mpaka kumapeto, mudzalimbikitsidwa ndi ‘kupitiriza kukundika chuma m’mwamba’!