Nyimbo 89
Chitsanzo cha Umulungu cha Chikondi
1. Mulungu wathu mwanzeru wakonza
Za ife,
Tonsefe,
Chitsanzo chake, chakutitsogoza,
Kuti ife,
Tisagwetu.
Njira yoposa iyo akhalamo,
Aitanira
kuyesayesatu,
Kumene ndithu, sitingachokeko,
Njachikondi,
Njira ya M’lungu.
2. Poyenda m’njira chikondi kwa mnzathu
Chikhale
Chowona,
Chidzatidzutsa kumathandizana
Muzonsezo,
Timachita.
Tisonyezetu chikondi chowona,
Kuwathandiza ena asakhote,
Kuti kapena angakanidwetu,
Kusonyeza
Chikondi chathu.
3. M’lungu nchikondi. Gulu lakonzeka
Indedi,
Ndithudi,
Mopanda dyera kumulemekeza,
Kumutama,
Kumutama.
Tilibukitse dzinalo kwa “nkhosa,”
Kuwathandiza kuwona cho’nadi,
Ntchito ikule mokoma komabe;
Pakutitu
Ndicho chikondi.