Nyimbo 71
Gwiritsitsani Mbiri Yabwino!
1. Tikhazikike muntchito,
Pofika mapeto.
Monga abale tichite,
Modalira M’lungu.
Kuŵala kwa chowonadi,
Tichita zambiri.
Ntchito yathu siri chabe
—Ikondweretsadi.
2. Chiukiriro cha anthu
Chidzutsa mitima,
Chiwathandiza kulimba.
Chiwakondweretsa.
Tifuna kukhulupira
Malonjezo a Ya.
Tiimetu molimbika;
Kuti tipambane.
3. Pogwira ntchito mwamphamvu
Kufika mapeto,
Tifunetu atsamwali
Otilimbikitsa.
“Mbiri” ya chiyembekezo
Cha Paradaiso.
Tiyamikira Mulungu
Mwa Mwana’ke Kristu.