Mutu 17
“Mukhale Nacho Chikondano Chenicheni mwa Inu Nokha”
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene kawirikawiri chimachititsa chidwi ofika chatsopano pamisonkhano ya Mboni za Yehova? (b) Kodi ndiumboni wina wotani wa khalidwe iri umene iwo amawona pamisonkhano yathu yaikulu?
PAMENE anthu kwanthawi yoyamba afika kumisonkhano yampingo ya Mboni za Yehova kawirikawiri amachita chidwi kwambiri ndi chikondi chosonyezedwa kumeneko. Amachiwona m’mayanjano aubwenzi ndi m’kulonjeredwa kwawo.
2 Pamisonkhano yathu yaikulu alendo amawonanso kuti unyinji wa ofikawo uli wodzisungira bwino kwambiri. Mtola nkhani wa nyuzipepala analemba ponena za msonkhano waukulu wotero kuti: ‘Panalibe aliyense woledzera ndi mankhwala kapena zakumwa zoledzeretsa. Panalibe kukalipa ndi kudandaula. Panalibe kukankhana. Panalibe kupanikizana panalibe munthu wotukwana ndi kulalata. Panalibe njerengo zotonzana kapena kulankhula konyansa. Panalibe mpweya wodzala utsi. Panalibe kuba. Panalibe munthu woponya zitini pakapinga. Unalidi mkhalidwe wachilendo.’ Zonsezi ziri umboni wachikondi chimene ‘sichimachita zosayenera, ndi kusatsata zamwini yekha.’—1 Akor. 13:4-8.
3. (a) M’nthawi yokwanira kodi nchiyani chiyenera kuwoneka ponena za kusonyeza kwathu chikondi? (b) Motsanzira Kristu, kodi nchikondi chamtundu wanji chimene tifunikira kukulitsa?
3 Chikondi ndicho mkhalidwe umene umadziwikitsa Mkristu aliyense wowona. (Yoh. 13:35) Pamene tikula mwauzimu, tiyenera kuchisonyeza pamlingo waukulu kotheratu. Mtumwi Paulo anapemphera kuti chikondi cha abale ake “chisefukire chiwonjezere.” (Afil. 1:9; 1 Ates. 3:12) Ndiponso Petro anachirikiza Akristu anzake kulola chikondi chawo kuphatikizapo “gulu lonse la abale.” (1 Pet. 2:17, NW) Chikondi chathu chiyenera kutisonkhezera kuchita zowonjereka koposa kufika kokha pamisonkhano ndi anthu amene timapanga zoyesayesa zochepa kuti tidziwane nawo. Chiyenera kuphatikizapo zambiri koposa kungopereka “moni” wachifundo nthawi ndi nthawi. Mtumwi Yohane anasonyeza kuti chiyenera kukhala cha kudzimana. Iye analemba: “Umo tizindikira chikondi, popeza iyeyu [Mwana wa Mulungu] anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.” (1 Yoh. 3:16; Yoh. 15:12, 13) Sitinachite kale zimenezo. Koma kodi ife tikaperekadi moyo wathu kaamba ka abale athu? Eya, kodi nkumlingo wotani kumene timadzigwiritsira ntchito kuwathandiza tsopano, ngakhale pamene kungakhale kosayenerera?
4. (a) Kodi ndim’njira ina yotani mu imene tingapeze kuti tingakhoze kusonyeza chikondi mokwanira? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukhala ndi chikondano?
4 Limodzi ndi ntchito zimene zimasonyeza mzimu wa kudzimana, kulinso kofunika kukhala ndi malingaliro achifundo owona kulinga kwa abale athu. Mawu a Mulungu amatichirikiza kuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni.” (Aroma 12:10) Tonsefe timalingalira mwanjirayo kulinga kwa anthu ena. Kodi tingaphatikizepo kuwonjezereka m’kagulu ka amene tikulingalira kukhala okondedwa motero? Pamene mapeto a dongosolo lakale ayandikira, kuli kofunika kwa ife kuyandikana kwambiridi ndi abale athu Achikristu. Baibulo limatichenjeza pamfundoyi, kumati: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chiri pafupi; . . . koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; kuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.”—1 Pet. 4:7, 8.
5. Kodi nchifukwa ninji kuli kulakwa kuyembekezera kuti palibe mavuto amene angabuke pakati pa ziwalo zampingo?
5 Ndithudi, malinga ngati tiri opanda ungwiro, padzakhala nthawi pamene tidzachita zinthu zimene zimakhumudwitsa ena. Nawonso, mwanjira zosiyanasiyana adzatichimwira. (1 Yoh. 1:8) Ngati inu mudzipeza mu mkhalidwe wotero, kodi muyenera kuchitanji?
Chochita Pamene Mavuto Abuka
6. (a) Kodi nchifukwa ninji uphungu wa Baibulo nthawi zonse sumavomerezana ndi zikhoterero zathu? (b) Koma kodi nchiyani chikakhala chotulukapo ngati tichigwiritsira ntchito?
6 Malemba amapereka chitsogozo chofunika. Koma pamene atipatsa uphungu uwo ungakhale wosayenerana ndi zimene ife monga anthu opanda ungwiro tiri okhoterera kuchita. (Aroma 7:21-23) Komabe, kuyesayesa kwathu kwaphamphu kuugwiritsira ntchito kudzasonyeza chikhumbo chathu chowona mtima cha kukondweretsa Yehova, ndiponso kudzalemereretsa khalidwe lachikondi chathu kulinga kwa ena.
7. (a) Ngati munthu wina ativulaza, kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulipsira? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kungopewa mbale amene watikhumudwitsa?
7 Nthawi zina pamene anthu avulazidwa amafunafuna njira za kulipsilira kwa wokhumudwitsayo. Koma zimenezo zimangochititsa kokha mkhalidwewo kuipa kwambiri. Ngati kubwezera kuli kofunika, tiyenera kukusiyira kwa Mulungu. (Miy. 24:29; Aroma 12:17-21) Ena angayeseyese kusafuna kuwona wokhumudwitsayo m’moyo wawo, kupewa kuwonana ndi kulankhulana naye. Koma ife sitingatero ndi olambira anzathu. Mwapang’ono, kuvomerezeka kwa kulambira kwathu kumadalira, pa kukonda kwathu abale athu. (1 Yoh. 4:20) Kodi tinganene mowona mtima kuti timakonda munthu amene sitidzalankhula naye kapena amene kukhalapo kwake kumatidetsa kukhosi? Tifunikira kulamulira vutolo ndi kulithetsa. Motani?
8, 9. (a) Ngati tiri ndi chifukwa chodandaula motsutsana ndi mbale, kodi nchiyani chimene chiri chinthu cholungama cha kuchita? (b) Koma bwanji ngati iye watichimwira mobwerezabwereza? (c) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita ndinkhaniyi mwanjira iyi, ndipo kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kutero?
8 Pankhani iyi mtumwi Paulo analemba za “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pamnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akol. 3:13) Kodi inu mungachite zimenezo? Kodi bwanji ngati munthuyo mobwerezabwereza akuchimwirani m’njira zosiyanasiyana?
9 Mtumwi Petro anali ndi funso lofananalo, ndipo anapereka lingaliro lakuti mwinamwake ayenera kuyesa kukhululukira mbaleyo kufikira nthawi zisanu ndi ziwiri. Yesu anayankha: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.” Koma chifukwa ninji? Yesu analongosola mwa kupereka fanizo limene linagogomezera ukulu wa mangawa athu kwa Mulungu poyerekezera ndi alionse amene munthu angakhale nafe mangawa. (Mat. 18:21-35) Mwanjira zambiri timachimwira Mulungu tsiku lirilonse—nthawi zina mwa machitachita adyera, kawirikawiri mwa zimene timanena kapena kuganiza, kuphatikizapo mwa kulephera kuchita zimene tiyenera kuchita. M’kupulukira kwathu tingakhale tisakuzindikira kuti zina za zinthu zimene tinachita zinali zolakwa, kapena m’kuchita mofulumira tingalephere kuganiza mwamphamvu mokwanira za nkhaniyo. Mulungu akanafunsira kuti tilipe ndi moyo wathu kaamba ka machimo athuwo. (Aroma 6:23) Koma iye wapitirizabe kusonyeza chifundo kwa ife (Sal. 103:10-14) Chifukwa chake, sikuli konse kosayenera, kuti atifune ife kuchitirana wina ndi mnzake mofananamo. (Mat. 6:14, 15; Aef. 4:1-3) Pamene tichita zimenezo, m’malo mwa kusonkhezera mkwiyo, nkwachiwonekere kuti tapeza mtundu wa chikondi chimene “sichilingilira zoipa.”—1 Akor. 13:4, 5; 1 Pet. 3:8, 9.
10. Kodi tiyenera kuchitanji ngati mbale ali ndi kanthu kena motsutsana nafe?
10 Pangakhale nthawi pamene timazindikira kuti, ngakhale kuti tiribe malingaliro oipa kulinga kwa mbale wathu, wachita kanthu kena motsutsana nafe. Kodi tiyenera kuchitanji? Mosazengereza tifunikira kulankhula naye ndi kuyesayesa kubwezeretsa maunansi amtendere. Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyambe ndife kuchitapo kanthu. (Mat. 5:23, 24) Kuchita zimenezo sikungakhale kosavuta. Kumafunikira chikondi ndi kudzichepetsa. Kodi mikhalidwe imeneyo iri yamphamvu mokwanira kwa inu kotero kuti mukanachita zimene Baibulo limalangiza? Ichi chiri chonulirapo chofunika cha kuchikalimira.
11. Ngati mbale achita zinthu zotikhumudwitsa, kodi tiyenera kuchitanji?
11 Kumbali ina, kungakhale kwakuti munthu wina akuchita zinthu zimene zikukukhumudwitsani—mwinamwake ena. Kodi sikukanakhala kwabwino kuti munthu wina alankhule naye? Mwinamwake. Ngati inu mwininu mudzalongosola vutolo kwa iye mwanjira yachifundo, izi zingabweretse zotulukapo zabwino. Koma choyamba muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi zinthu zimene amachita ziridi zosemphana ndi malemba? Kapena kodi vutolo liri kwakukulukulu chifukwa cha magwero anga ndi kuti kuphunzitsidwa nzosiya ndi zake?’ Ngati ziri choncho, samalani kusadzikhazikitsira miyezo yanu ndiyeno kuweruza mogwirizana ndi imeneyi. (Yak. 4:11, 12) Mopanda tsankho Yehova amalandira anthu ochokera kumagwero amitundu yonse ndipo ali woleza mtima nawo pamene akukula mwauzimu.
12. (a) Ngati pali chochitika cha kulakwa kwakukulu mu mpingo, kodi ndani amasamalira zimenezo? (b) Koma kodi ndipansi pamikhaldwe yotani pamene thayo la wochimwiridwa liri lakuchitapo kanthu choyamba? Ncholinga chotani?
12 Komabe, ngati munthu wina mu mpingo achita tchimo lalikulu, izi zifunikira chisamaliro chamwamsanga. Koma ndi yani? Kawirikawiri ndi akulu. Komabe, ngati chikuphatikizapo nkhani ya bizinesi pakati pa abale, kapena mwinamwake kugwiritsira ntchito molakwa lirime mwanjira imene munthu wina wavulazidwa kwambiri, pamenepo wochimwiridwayo ayenera choyamba kuyesayesa kuthandiza wolakwa mwachindunji. Izi zingawonekere kukhala zovuta kwa ena. Koma ndizo zimene Yesu analangiza pa Mateyu 18:15-17. Kukonda mbale wake ndi chikhumbo chowona mtima cha kumsunga monga mbale chidzathandiza munthu kuchita mumkhalidwe umene ngati nkotheka, udzafika mtima wa munthu wochimwayo.—Miy. 16:23.
13. Ngati vuto labuka pakati pathu ndi mbale wina, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kuwona nkhaniyo moyenerera?
13 Pamene vuto libuka, kaya likhale lalikulu kapena laling’ono, timathandizidwa ngati tiyesayesa kuzindikira mmene Yehova amaliwonera. Iye samavomereza tchimo mu mpangidwe uliwonse, komabe amawuwona mwa ife tonse. M’nthawi yake yokwanira ozolowera kuchita uchimo osalapa amachotsedwa m’gulu lake. Koma bwanji ponena za ena tonsefe? Ife tonse tasonyezedwa kuleza mtima kwake ndi chifundo. Akupereka chitsanzo choti chitsanziridwe ndi ife. Pamene titero, tikusonyeza chikondi chake.—Aef. 5:1, 2.
Funafunani Njira “za Kuchikulitsira”
14. (a) Kodi nchifukwa ninji Paulo analimbikitsa Akorinto “kuchikulitsa”? (b) Kodi ndimotani mmene malemba olembedwa pano amasonyezera kuti tonsefe timachita bwino kulingalira zamfundoyi?
14 Mtumwi Paulo anatha miyezi yambimbiri kumanga mpingo m’Korinto, Grisi. Iye anagwira ntchito zolimba kuthandiza abale kumeneko ndipo anawakonda. Koma ena a iwo analibe malingaliro achikondi kwa iye. Anali osuliza kwambiri. Iye anawalimbikitsa “kukulitsidwa” kusonyeza chikondi. (2 Akor. 6:11-13; 12:15) Tonsefe tikuchita bwino kulingalira mmene tikusonyezera chikondi kwa ena ndi kufunafuna njira za “kuchikulitsira.”—1 Yoh. 3:14; 1 Akor. 13:3.
15. Kodi nchiyani chingatithandize kukula m’chikondi pamunthu amene ife enife sitimakondweretsedwa naye?
15 Kodi pali ena mu mpingo kwa amene timakupeza kukhala kovuta kukondana nawo? Ngati tiyesayesa ife enife kukwirira zophophonya zawo zazing’ono zirizonse zimene atichitira, monga momwe tikanawafuna kuti atichitire, izi zingathandize unansi wachikondi pakati pathu. (Miy. 17:9; 19:11) Malingaliro athu kulinga kwa iwo nawonso angawongoleredwe ngati tifunafuna mikhalidwe yawo yabwino ndi kusumika pa imeneyi. Kodi ife tawonadi njira m’zimene Yehova akugwiritsirira ntchito abale awa? Kutereku ndithudi kudzachititsa chikondi chathu pa iwo kukula.—Luka 6:32, 33, 36.
16. Kwenikweni, kodi ndimotani mmene ‘tingakulitsire’ kusonyeza chikondi kwa awo a mu mpingo wathu?
16 Ndithudi, tiri ndi polekezera ponena za zimene tingachitire ena. Tingakhale osakhoza kulonjera aliyense pamsonkhano. Kungakhale kosatheka kuphatikiza aliyense pamene tiitana mabwenzi ku chakudya. Ife tonse tiri ndi mabwenzi apafupi amene timatha nawo nthawi yochuluka koposa mmene timachitira ndi ena. Koma kodi tinagakhoze “kukulitsa”? Kodi tingawonongere mphindi zochepa chabe mlungu uliwonse kudziwana bwino kwambiri ndi munthu wina mu mpingo amene sanakhale konse bwenzi lathu lapafupi? Kodi panthawi ndi nthawi tingaitane mmodzi wa amenewa kugwira nafe ntchito mu uminisitala wakumunda? Ngati tiridi ndi chikondano chenicheni, tidzapezadi njira zochisonyezera.
17. Pamene tiri pakati pa abale amene ndi kale lonse sitinakumane nawo, kodi nchiyani chimene chidzasonyeza kuti kaya tiri ndi chikondano chachikulu kaamba ka iwonso?
17 Misonkhano yaikulu Yachikristu imapereka mipata yabwino kwambiri ya ‘kukulitsa’ chikondi chathu. Zikwi zambiri zingafikepo. Sitingakhoze kulonjera iwo onse. Koma tingakhoze kudzisungira mwanjira imene imasonyeza kuti timaika ubwino wawo patsogolo pa ubwino wathu, ngakhale ngati sitinakumane nawo ndi kalelonse. Ndipo tingasonyeze chikondwerero chathu pakati pamisonkhano mwa kuyamba kulonjera ena okhala moyandikana nafe. Tsiku lina onse okhala padziko lapansi adzakhala abale ndi alongo, ogwirizanitsidwa m’kulambiridwa kwa Mulungu ndi Atate wa onse. Ha chidzakhala chisangalalo chotani nanga kudziwa iwo onsewo, limodzi ndi mikhalidwe yawo yosiyanasiyana yambiriyo! Chikondano chenicheni kwa iwo chidzatisonkhezera kufuna kuchita zimenezo. Kodi mulekeranji kuyamba tsopano?
Makambitsirano Openda
● Pamene mavuto abuka pakati pa abale kapena alongo, kodi amenewa ayenera kuthetsedwa motani? Chifukwa ninji?
● Pamene tikula mwauzimu, kodi chikondi chathu chiyeneranso kukula m’njira zotani?
● Kodi ndimotani mmene kuliri kotheka kusonyeza chikondano chenicheni kwa oposa kokha mabwenzi apafupi chabe?