Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kukhulupirira Choikidwiratu?
UGOGODI! KUNENEZA! Pamene munthu wolemekezeka wa m’chitaganya akhulupirira kuti dzina lake kapena mbiri yake yaipitsidwa ndi lipoti lonama, amaumirizika kulungamitsa nkhaniyo. Mwina angapite ku khoti kukasumira mlandu awo amene ali ndi thayo la ugogodiwo.
Aha, kukhulupirira choikidwiratu ndikodi kuneneza Mulungu Wamphamvuyonse. Chiphunzitsocho chimati Mulungu ndiye amene ali ndi mlandu wa masoka onse ndi ngozi zimene zimagwera anthu. Ngati mumakhulupirira choikidwiratu, mungaganize kuti Mfumu Yachilengedwe Chonse yalinganiza mpambo wa zochitika umene uli ndi mawu otere: ‘Lero, John adzavulala mu ngozi ya galimoto, Fatou adzagwidwa ndi malungo, nyumba ya Mamadou idzawonongedwa ndi mkuntho’! Kodi mungasonkhezerekedi kutumikira Mulungu wotero?
‘Komano ngati Mulungu alibe mlandu wa masoka athu, ndiyeno angakhale yani?’ angafunse motero okhulupirira choikidwiratu. Ousmane, mnyamata wotchulidwa mu nkhani yapitayo, anadzifunsa zimenezi. Komano sanafunikire kulota kapena kuganizira kuti afike pa choonadi. Anaphunzira kuti Mulungu wadzichotsera chinenezo chimenechi mwa ziphunzitso zake zopezeka m’Mawu Ake ouziridwa, Baibulo. (2 Timoteo 3:16) Pamenepa, tiyeni tilingalire zimene Baibulo limanena pankhaniyi.
Kodi Ndani Amene Ali ndi Mlandu?
Kusefukira kwa madzi, mikuntho, zivomezi—masoka oterowo kaŵirikaŵiri amatchedwa zochita za Mulungu. Komabe Baibulo silimasonyeza kuti Mulungu amachititsa masoka amenewo. Lingalirani za tsoka limene linachitika zaka mazana ambiri zapita ku Middle East. Baibulo limatiuza kuti munthu mmodzi yekha amene anapulumuka tsokalo anasimba kuti: “Wagwa moto wa Mulungu [mawu achihebri amene kaŵirikaŵiri amatanthauza mphezi] wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa.”—Yobu 1:16.
Pamene kuli kwakuti munthu wowopsedwa ameneyu mwina anaganiza kuti Mulungu ndiye anali ndi mlandu wa motowo, Baibulo limasonyeza kuti Iyeyo analibe mlandu. Dziŵerengereni nokha Yobu 1:7-12, ndipo mudzaona kuti anachititsa mpheziyo sanali Mulungu, koma Mdani wake—Satana Mdyerekezi! Uku sikunena kuti Satana ndiye amachititsa masoka onse. Koma mwachionekere, palibe chifukwa choimbira mlandu Mulungu.
Kwenikweni, anthu kaŵirikaŵiri ndiwo ayenera kuimbidwa mlandu pamene zinthu zilakwika. Kulephera sukulu, ntchito, kapena kulephereka kwa maunansi a anthu kungachitike chifukwa cha kusayesayesa ndi kusaphunzira bwino kapena mwinamwake kusalingalira za ena. Mofananamo, matenda, ngozi, ndi imfa zingachitike chifukwa cha kusasamala. Eetu, kudzimangirira lamba wa m’galimoto pamene mukuyendetsa kumachepetsa kwambiri imfa ya munthu m’ngozi ya galimoto. Lamba wa m’galimoto sakanachita chilichonse ngati “choikidwiratu” chosasinthikacho chikanakhalakodi. Kusamalira umoyo ndi mankhwala ndiponso ukhondo zimachepetsanso kwambiri imfa zamwamsanga. Ngakhale masoka ena amene anthu ambiri amawatcha kuti “zochita za Mulungu” kwenikweni ndiwo zochita za munthu—chotulukapo chochititsa chisoni cha kusasamalira bwino kwa munthu dziko lapansi.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 11:18.
“Nthaŵi ndi Zochitika Zosadziŵika”
Zoonadi, pali zochitika zambiri zachisoni zimene zochititsa zake sizimadziŵika bwino. Komabe, onani zimene Baibulo limanena pa Mlaliki 9:11, NW: “Ndinabweranso kuona pansi pano kuti amene athamanga kwambiri sapambana liŵiro, ngakhale amphamvu sapambana nkhondo, ngakhalenso anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira sapeza chuma, ndipo ngakhale aja amene ali ndi chidziŵitso sapeza chiyanjo; chifukwa nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimawagwera iwo onse.” Motero palibe chifukwa chokhulupirira kuti Mlengi ndiye amachititsa ngozi kapena kuti anthu a m’ngozi amakhala akulangidwa m’njira ina.
Yesu Kristu mwini anatsutsa malingaliro okhulupirira choikidwiratu. Potchula za tsoka lina limene linali lodziŵika kwa omvetsera ake, Yesu anafunsa kuti: “Iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m’Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu? Ndinena kwa inu, Iyayitu.” (Luka 13:4, 5) Mwachionekere Yesu anagwirizanitsa tsokalo, osati ndi kuloŵererapo kwa Mulungu, koma ndi “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika.”
Zosakaza za Kupanda Ungwiro
Bwanji nanga za imfa ndi matenda osatheka kufotokozedwa? Baibulo limalongosola mkhalidwe wa munthu mosapita m’mbali motere: “Mwa Adamu onse amwalira.” (1 Akorinto 15:22) Imfa yavutitsa anthu kuyambira pamene kholo lathu Adamu anayenda m’njira ya kusamvera. Monga momwe Mulungu anachenjezera, Adamu anasiyira mbadwa zake choloŵa cha imfa. (Genesis 2:17; Aroma 5:12) Motero, pamenepa, nthenda zonse zinachokera kwa kholo lathu tonse Adamu. Zofooka zathu za choloŵa nazonso zimachirikiza kwambiri zogwiritsa mwala ndi kulephera kumene timakhala nako m’moyo.—Salmo 51:5.
Lingalirani za vuto la umphaŵi. Kukhulupirira choikidwiratu kaŵirikaŵiri kwalimbikitsa ovutika kukhala m’mavuto awo modzinyanyala. ‘Izi nzimene anatiikira’ amakhulupirira choncho. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti kupanda ungwiro kwa munthu, osati choikidwiratu, nkumene kuli ndi mlandu. Ena amakhala amphaŵi pamene ‘atuta zimene anafesa’ chifukwa cha ulesi kapena kusasamalira bwino chuma. (Agalatiya 6:7; Miyambo 6:10, 11) Anthu miyandamiyanda amakhala mu umphaŵi chifukwa chakuti anthu aumbombo olamulira amawalima pamsana. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:6.) “Wina apweteka mnzake pomlamulira,” limatero Baibulo. (Mlaliki 8:9) Palibe umboni wakuimbira mlandu wonse wa umphaŵi pa Mulungu kapena choikidwiratu.
Kukhulupirira Choikidwiratu—Ziyambukiro Zake Zovulaza
Chikhalirechobe chigomeko chinanso champhamvu chotsutsa kukhulupirira choikidwiratu ndicho chiyambukiro chimene kukhulupirira choikidwiratuko kungakhale nacho pa ochikhulupirira. Yesu Kristu anati: “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.” (Mateyu 7:17) Tiyeni tilingalire za ‘chipatso’ chimodzi cha kukhulupirira choikidwiratu—mmene kumayambukirira thayo la anthu.
Lingaliro labwino lakuti munthu ali ndi thayo nlofunika. Ndilo chimodzi cha zinthu zimene zimasonkhezera makolo kusamalira mabanja awo, antchito kuchita ntchito zawo ndi mtima wonse, opanga zinthu kutulutsa zinthu zolimba. Kukhulupirira choikidwiratu kungawononge lingalirolo. Mwachitsanzo, yerekezerani kuti galimoto la munthu wina lili ndi vuto la chiwongolero. Ngati iyeyo amazindikira kuti ali ndi thayo lalikulu, amakalikonzetsa chifukwa chodera nkhaŵa moyo wake ndi miyoyo ya mapasinjala ake. Komanso, wokhulupirira choikidwiratu anganyalanyaze ngozi imeneyi, akumalingalira kuti galimotolo lidzafa kokha ngati chili ‘chifuniro cha Mulungu’!
Inde, kukhulupirira choikidwiratu kungachirikize mosavuta kusasamala, ulesi, kulephera kuvomereza thayo la zochita za munthu, ndi mikhalidwe ina yambirimbiri yosakondweretsa.
Chopinga pa Unansi Wathu ndi Mulungu?
Changozi koposa zonse nchakuti, kukhulupirira choikidwiratu kungapondereze lingaliro la thayo la munthu kulinga kwa Mulungu. (Mlaliki 12:13) Wamasalmo akulimbikitsa anthu onse ‘kulaŵa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino.’ (Salmo 34:8) Mulungu amaika zofunika zina kwa awo ofuna kulandira ubwino wake.—Salmo 15:1-5.
Chimodzi cha zofunika zimenezo ndicho kulapa. (Machitidwe 3:19; 17:30) Zimenezo zimaphatikizapo kuvomereza zophophonya zathu ndi kupanga masinthidwe ofunika. Monga anthu opanda ungwiro, tonsefe tili ndi zambiri zofunikira kulapa. Koma ngati munthu akhulupirira kuti iyeyo ndi kapolo wa choikidwiratu amene sangachite chilichonse, nkovuta kuti aone kufunika kwa kulapa kapena kusenza thayo la machimo ake.
Ponena za Mulungu, wamasalmo anati: “Chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake.” (Salmo 63:3) Komabe, kukhulupirira choikidwiratu kwakhutiritsa mamiliyoni ambiri kuti Mulungu ndiye woyambitsa nsautso. Motero, zimenezi zachititsa ambiri kumpsera mtima, akumatsekereza mwaŵi wa kukhala kwawo paunansi weniweni ndi Mlengi. Ndi iko komwe, kodi mungakonde bwanji munthu amene munamlingalira kukhala akuchititsa mavuto anu onse ndi ziyeso? Motero kukhulupirira choikidwiratu kumaika chopinga pakati pa Mulungu ndi munthu.
Kumasulidwa ku Ukapolo wa Choikidwiratu
Ousmane wachichepere, wotchulidwa pachiyambi, panthaŵi ina anagwidwa ukapolo ndi kukhulupirira choikidwiratu. Komabe, pamene Mboni za Yehova zinamthandiza kupenda malingaliro ake mogwiritsira ntchito Baibulo, Ousmane anasonkhezereka kusiya kukhulupirira kwake choikidwiratu. Zotulukapo zake zinali mpumulo waukulu ndi kaonedwe katsopano kabwino pa moyo. Chofunika koposa nchakuti wafikira pa kudziŵa Yehova monga Mulungu amene ali “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.”—Eksodo 34:6.
Ousmane wazindikiranso kuti Mulungu, ngakhale kuti samalinganiza kanthu kalikonse m’moyo wathu, ali ndi chifuno kaamba ka mtsogolo.a “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo,” amatero 2 Petro 3:13. Mboni za Yehova zathandiza mamiliyoni ambiri kukulitsa chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha monga mbali ya “dziko latsopano” lolonjezedwa limeneli. Zikufuna kuthandiza inunso.
Pamene mukukula m’chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo, mudzazindikira kuti mtsogolo mwanu simumadalira pa choikidwiratu chinachake chimene simungachilamulire. Mawu a Mose kwa Aisrayeli akale amagwiranso ntchito pamenepa: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kummamatira iye.” (Deuteronomo 30:19, 20) Inde, mungathe kusankha ponena za mtsogolo mwanu. Muli mosalamuliridwa ndi choikidwiratu.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka mafotokozedwe atsatanetsatane a kudziŵiratu zinthu kwa Mulungu, onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1985, masamba 3-7.
[Zithunzi pamasamba 6, 7]
Masoka awa sanali ‘zochita za Mulungu’
[Mawu a Chithunzi]
Chinthunzi cha U.S. Coast Guard
WHO
CHITHUNZI CHA UN 186208/M. Grafman