Mutu 18
Tifunikira Kugwiritsira Ntchito Kudzipereka Kwaumulungu pa Nyumba
1. (a) Pambuyo pa kuphunzira miyezo ya Yehova ya ukwati, kodi ndimasinthidwe otani amene anthu ambiri apanga? (b) Kodi nzowonjezereka zotani zimene zikuphatikizidwa m’moyo wabanja Lachikristu?
PAKATI pa chowonadi chokondweretsa chimene tinaphunzira mkati mwa maphunziro athu Abaibulo oyambirira panali chija chophatikizapo ukwati ndi moyo wabanja. Tinafikira pa kuzindikira Yehova monga Woyambitsa wa ukwati ndipo tinawona kuti m’Baibulo anapereka chitsogozo chabwino koposa cha mabanja. Chifukwa cha chitsogozo chimenecho, mokondweretsa anthu ambiri asiya moyo wachisembwere ndipo anachititsa ukwati wawo kulembetsedwa bwino lomwe. Koma pali zina zambiri ku moyo wabanja Lachikristu koposa zimenezo. Kumaphatikizaponso kaimidwe kathu ka maganizo ponena za kukhalitsa kwa mgwirizano waukwati, kukwaniritsidwa kwa mathayo athu m’banja, ndi mmene tingachitire ndi ziwalo zina zabanja.—Aef. 5:33–6:4.
2. (a) Kodi munthu aliyense amagwiritsira ntchito chimene amadziwa kuchokera m’Baibulo pabanja? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu ndi Paulo akugogomezerera kufunika kwa kutero?
2 Anthu mamiliyoni ambiri amadziwa zimene Baibulo limanena za nkhanizi. Koma pamene ayang’anizana ndi mavuto m’banja la iwo eni, samaligwiritsira ntchito. Bwanji ponena za ife? Ndithudi palibe aliyense wa ife amafuna kufanana ndi awo amene Yesu anatsutsa chifukwa chakuti ananyalanyaza lamulo la Mulungu limene linafunikiritsa ana kulemekeza makolo awo mwa kulingalira kuti kupembedza kwachiphamaso kunali kokwanira. (Mat. 15:4-9) Ife sitifuna kukhala anthu okhala ndi mpangidwe wa kudzipereka kwaumulungu koma amene amalephera kuugwiritsira ntchito “m’banja la iwo eni.” M’malo mwake, tiyenera kufuna kusonyeza kudzipereka kwaumulungu kowona, kumene kuli “njira yaphindu lalikulu.”—1 Tim. 5:4; 6:6, NW; 2 Tim. 3:5.
Kodi Ukwati Udzakhala Kwautali Wotani?
3. (a) Kodi nchiyani chikuchitikira maukwati ambiri, koma kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chitsimikizo chathu? (b) Gwiritsirani ntchito Baibulo lanu kuyankha mafunso ondandalikidwa pamwamba apa onena za kukhalitsa kwa ukwati.
3 Zomangira zaukwati zikutsimikizira kukhala zosachedwa kusweka kwambiri, mwakawiri kawiri kwambiri. Okwatirana ena amene akhalira limodzi kwa zaka 20, 30 kapena 40 tsopano akusankha kuyamba “moyo watsopano” ndi munthu winawake. Ndiponso sikulinso kwachilendo kumva kuti okwatirana achichepere alekana pambuyo pamiyezi yowerengeka chabe yaukwati. Mosasamala kanthu za zimene ena akuchita, monga olambira Yehova tiyenera kukhala ndi chikhumbo cha kukondweretsa Mulungu. Kodi Mawu ake amanenanji za izi?
Pamene mwamuna ndi mkazi akwatirana, kodi ayenera kuyembekezera kukhalira limodzi kwa utali wotani? (Aroma 7:2, 3; Marko 10:6-9)
Kodi ndiati amene ali maziko okha achisudzulo chovomerezedwa pamaso pa Mulungu? (Mat. 19:3-9; 5:31, 32)
Kodi Yehova amalingalira mwamphamvu motani ponena za zisudzulo zimene siziri zovomerezedwa ndi Mawu ake? (Mal. 2:13-16)
Kodi Baibulo limachirikiza kulekana monga njira ya kuthetsera mavuto a ukwati? (1 Akor. 7:10-13)
4. Mosasamala kanthu ndi mkhalidwe wamakono, kodi nchifukwa ninji maukwati ena ali okhalitsa?
4 Kodi nchifukwa ninji maukwati ena amakhalitsa, pamene ena—ngakhale pakati pa odzitcha Akristu—akusweka? Kuyembekezera kukwatira kufikira pamene awiri onsewo ali okhwima ndicho chimene kawirikawiri chiri chochititsa chachikulu. Kupeza wokwatirana naye wokhala ndi zikhumbo zofanana ndi munthuwe ndi amene munthuwe ungakambitsirane naye nkhani momasuka kulinso kofunika. Koma chofunika kwambiri ndicho kukhala kwa munthuyo wogwiritsira ntchito mowona mtima kudzipereka kwaumulungu. Ngati munthu amakondadi Yehova ndipo ali wokhutira kuti njira Zake ziri zolungama, pamenepo padzakhala maziko abwino osamalirira mavuto amene amabuka. (Sal. 119:97, 104; Miy. 22:19) Ukwati wa munthu wotero sudzafooketsedwa ndi kaimidwe ka maganizo kakuti, ngati sudzagwira ntchito, iye nthawi zonse angathe kupeza chilekaniro kapena chisudzulo. Iye sadzagwiritsira ntchito zophophonya za mnzake wa mu ukwati monga chodzikhululukira nacho chonyalanyazira mathayo a iyemwini. M’malo mwake, adzaphunzira kuyang’anizana ndi mavuto a moyo ndi kupeza njira zogwira ntchito zothetsera.
5. (a) Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kwa Yehova kumaphatikizidwira? (b) Ngakhale pamene mukomana ndi vuto lalikulu, kodi ndimapindu otani amene angachokere m’kugwiritsitsa miyezo ya Yehova?
5 Tikuzindikira bwino kuti Mdyerekezi akunenabe kuti pamene tikumana ndi mavuto aumwini tidzanyalanyaza njira za Yehova ndipo tidzasankha kuti kulibwino kwambiri kudzisankhira tokha chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa. Koma anthu amene ali okhulupirika kwa Yehova saali otero. (Yobu 2:4, 5; Miy 27:11) Unyinji wa Mboni za Yehova zimene zakumana ndi chizunzo kuchokera kwa anzawo a mu ukwati sananyanyale zowinda zawo zaukwati. (Mat. 5:37) Ena, pambuyo pa nyengo ya zaka, akhaladi ndi chisangalalo cha kuwona anzawo a mu ukwati akugwirizana nawo m’kutumikira Yehova. (1 Akor. 7:16; 1 Pet. 3:1, 2) Ponena za ena, amene anzawo a mu ukwati sakusonyeza zizindikiro za kusintha kapena amene anzawo a mu ukwati awasiya chifukwa chakuti agwiririra zolimba ku chikhulupiriro chawo—awanso amadziwa kuti adalitsidwa kwambiri mwa kumamatira ku miyezo ya Yehova. Mwanjira yotani? Mikhalidwe yawo yawaphunzitsa kuyandikira kwa Yehova koposerapo. Aphunzira kusonyeza mikhalidwe yaumulungu ngakhale akudedwa. Iwo ali anthu amene miyoyo yawo imapereka umboni wamphamvu ya kudzipereka kwaumulungu.—Sal. 55:22; Yak. 1:2-4; 2 Pet. 1:5, 6.
Aliyense Kuchita Mbali Yake
6. Kuti pakhale ukwati wachipambano, kodi ndimakonzedwe otani amene ayenera kulemekezedwa?
6 Ndithudi, koposa kungokhalira limodzi kuli kofunika kuti pakhale ukwati wachipambanodi. Chofunika cha maziko ndicho kulemekeza kwa chiwalo chirichonse chabanja makonzedwe a Yehova a umutu. Uku kumathandizira kukhalapo kwa dongosolo labwino ndi lingaliro la chisungiko m’banja.—Akor. 11:3; Tito 2:4, 5; Miy. 1:8, 9; 31:10, 28.
7. Kodi ndimotani mmene umutu m’banja uyenera kugwiritsiridwa ntchito?
7 Kodi ndimotani mmene umutu umenewu uyenera kugwiritsiridwa ntchito? Mumkhalidwe umene umasonyeza mikhalidwe ya Yesu Kristu. Yesu ali wamphamvu m’kuchirikiza njira za Yehova; amakonda chilungamo ndipo amada kusayeruzika. (Aheb. 1:8, 9) Iye amakondanso kwambiri mpingo wake, amawupatsa chitsogozo chofunika nawusamalira. Iye saali wonyada ndi wadyera koma, m’malo mwake ali, “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima,” ndipo awo okhala pansi pa umutu wake ‘amapeza mpumulo wa miyoyo yawo.’ (Mat. 11:28, 29; Aef. 5:25-33) Pamene mwamuna amenenso ali atate asamalira banja lake mwanjirayo, kuli kwachiwonekere kuti akudzigonjetsera kwa Kristu, amene anapereka chitsanzo changwiro m’kudzipereka kwaumulungu. Ndithudi, anakubala Achikristu ayenera, kusonyeza mikhalidwe imodzimodziyo pochita ndi ana awo.
8. (a) M’mabanja ena, kodi nchifukwa ninji kumawonekera ngati kuti njira Zachikristu sizikupeza zotulukapo zokhumbidwa? (b) Kodi tiyenera kuchitanji ngati tayang’anizana ndi mkhalidwe wotero?
8 Komabe, chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu, mavuto angabuke. Mlingo wakutiwakuti wa chitsutso kulinga ku malangizo ochokera kwa ena kungakhale kutazika mizu kwambiri kale mwa ena aliyense m’banjalo asanayambe kugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino Abaibulo. Mapempho achifundo ndi mkhalidwe wachikondi zingawonekere kukhala zosaphula kanthu. Tidziwa kuti Baibulo limanena za kutaya “kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa.” (Aef. 4:31) Koma ngati anthu ena sakuwonekera kukhala ozindikira kanthu kalikonse, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa? Eya, kodi Yesu anachita motani pamene anali atapanikizika kwambiri? Sanatsanzire awo amene anamthupsa ndi kusautsidwa. M’malo mwake, anadziika kwa Atate wake, akumadalira pa iye. (1 Pet. 2:22, 23) Mofananamo, ngati mikhalidwe yopereka chiyeso ibuka m’banja, timasonyeza kudzipereka kwaumulungu ngati titembenukira kwa Yehova, kupempherera chithandizo chake, m’malo mwa kugwiritsira ntchito njira zadziko.—Miy. 3:5-7.
9. M’malo mwa kupezera zifukwa, kodi ndinjira zotani zimene amuna Achikristu ambiri aphunzira kugwiritsira ntchito?
9 Nthawi zonse masinthidwe samadza mofulumira, koma uphungu wa Baibulo umagwiradi ntchito. Amuna a banja ambiri amene poyamba anadandaula kwambiri ponena za zolakwa za akazi awo anapeza kuti kuwongokera kunayamba pamene iwo eniwo anazindikira mowonjezereka kotheratu zochita za Kristu ndi mpingo wake. Mpingo umenewo sunapangidwe ndi anthu angwiro. Komabe Yesu amakonda mpingowo, amaupatsa chitsanzo chabwino, ngakhale kupereka moyo wake m’malo mwake, ndipo amagwiritsira ntchito Malemba monga njira ya kuthandizira kuwongolera kotero kuti wonse pamodzi ukakhale womkondweretsa. (Aef. 5:25-27; 1 Pet. 2:21) Chitsanzo chake chalimbikitsa amuna a banja ambiri Achikristu kugwirira ntchito pa kupereka chitsanzo chabwino kwambiri ndi kupereka chithandizo chachikondi iwo eni kuti pakhale kuwongokera. Njira zotero zimakhala ndi zotulukapo zabwino koposa mmene kumachitira kupezera cholakwa kupwetekedwa mtima kapena kungokana kulankhula.
10. (a) Kodi ndim’njira zotani m’zimene mwamuna ndi atate—ngakhale wodzitcha kukhala Mkristu—angakhalire akupangira moyo wa ena m’banja lake kukhala wovuta? (b) Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuwongolera mkhalidwewo?
10 Ndithudi, angakhale mwamuna wabanjayo ndi atate amene zophophonya zake zikuchititsa mavuto m’banja. Bwanji ngati iye saali wodera nkhawa ndi zofunika zamaganizo za banja lake kapena ngati sakupereka chitsogozo chenicheni mwa kulinganiza makambitsirano abanja a Baibulo ndi ntchito zina? Mabanja ena apeza zotulukapo zabwino pambuyo pa makambitsirano achindunji, aulemu a vutolo. (Miy. 15:22; 16:23; 31:26) Koma ngakhale ngati zotulukapo siziridi zimene zinayambekezeredwa, aliyense angathandizire kuongokera kwa mkhalidwe wa pa banja mwa kukulitsa iye mwini zipatso zamzimu ndi kusonyeza nkhawa yachikondi ndi chifundo kaamba ka ziwalo zina zabanja. Kupita patsogolo sikudzadza, mwa kuyembekezera munthu wina kuchitapo kanthu, koma mwa kuchita mbali ya ife eni bwino lomwe, motero kusonyeza kuti ife enife tikugwiritsira ntchito kudzipereka kwaumulungu pabanja.—Akol. 3:18-20, 23, 24.
Kopeza Mayankho
11, 12. (a) Kodi ndimakonzedwe otani amene Yehova wapanga kutithandiza pa mavuto amoyo wabanja? (b) Kuti tipindule mokwanira, kodi nchiyani chimene chikuvomerezedwa kuti tichite?
11 Pali magwero ambiri ku amene anthu amatembenukirako kaamba ka uphungu wa zochitika za mabanja awo. Koma timadziwa kuti Mawu a Mulungu ali ndi uphungu wabwino koposa, ndipo tiri ndi chikondwerero kuti kupyolera mwa gulu lake lowoneka akutithandiza kuugwiritsira ntchito. Kodi inu mukupindula mokwanira kuchokera ku thandizo limenelo?—Sal. 119:129, 130; Mika 4:2.
12 Kuphatikiza pa kufika pamisonkhano yampingo, kodi muli ndi nthawi yopatulidwa yokhazikika yaphunziro Labaibulo labanja? Mabanja amene amachita izi mokhazikika mlungu uliwonse akhala ogwirizana m’kulambira kwawo. Moyo wabanja lawo umachititsidwa kukhala wabwino kwambiri pamene akambitsirana kugwira ntchito kwa Mawu a Mulungu kumikhalidwe ya iwo eni.—Yerekezerani Deuteronomo 11:18-21.
13. (a) Ngati tiri ndi mafunso pankhani zenizeni zaukwati kapena zabanja, kodi nkuti kumene kawirikawiri tingapezeko chithandizo chofunikacho? (b) Kodi nchiyani chiyenera kusonyezedwa m’zosankha zonse zimene timapanga?
13 Mwinamwake pali mafunso onena za nkhani zenizeni za ukwati kapena za banja zimene ziri zofunika kwa inu. Mwachitsanzo, bwanji za kupewa kutenga mimba? Kodi kufulidwa nkoyenerera kwa Akristu? Kodi kutaya mimba nkopanda cholakwa ngati kukuwonekera ngati kuti khandalo lidzabadwa lopunduka? Kodi pali malire ali onse ponena za mtundu wa kugonana umene uli woyenerera pakati pa mwamuna ndi mkazi? Ngati wachichepere wa zaka 13 kufika 19 asonyeza chikondwerero chochepa m’nkhani zauzimu, kodi ayenera kukhala ndi phande, limodzi ndi banja m’kulambira kumlingo wotani? Inu mosakaikira muli ndi lingaliro pa iriyonse ya nkhani izi. Koma kodi mungayankhe pamaziko a malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo? Lirilonse lamafunso amenewa linapendewa mu Nsanja ya Olonda. Phunzirani kugwiritsira ntchito zisonyezero zopezeka kupeza chidziwitso chotere. Ngati mulibe mabukhu akale amene zisonyezero zingawasonye, pendani laibrale pa Nyumba Yaufumu. Musayembekezere Inde kapena Ayi ku funso lirilonse. Nthawi zina muyenera kusankha—inumwini kapena monga awiri okwatirana. Koma phunzirani kupanga zosankha zimene zimasonyeza chikondi chanu cha pa Yehova ndi cha paziwalo za banja lanu. Pangani zosankha zimene zimapereka umboni wachikhumbo chanu chaphamphu cha kukhala wokondweretsadi kwa Mulungu. Ngati mutero, kudzapereka umboni kwa Yehova ndi kwa ena amene amakudziwani bwino kuti mumagwiritsiradi ntchito kudzipereka kwaumulungu osati kokha poyera komanso m’banja la inu mwini.—Aef. 5:10; Aroma 14:19.
Makambitsirano Openda
● Kodi kukhulupirika kwa Yehova kumaphatikizidwa bwanji m’kukhulupirika kwa munthuwe ku zowinda zaukwati?
● Pamene tapanikizika ndimavuto abanja, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kuchita chimene chiri chokondweretsa kwa Mulungu?
● Ngakhale ngati ena m’banja alephera, kodi tingachitenji kuwongolera mkhalidwewo?