Nyimbo 189
Kulengeza Tsiku Lakubwezera la Yehova
1. Malipenga amveka;
Chi’tano chamveka.
Tsiku lobwezeralo
La Ya layandika.
Tilengeza molimba,
Nkana anyozera.
Tipereke chenjezo;
Ufumu wabadwa.
2. Nkhondoyo nja Yehova.
Yesu atsogoza.
Mapeto olakika,
Kukweza cho’nadi.
Maluso a Satana
Adzathetsedwadi.
Taphunzitsidwa ndi
Ya Kumenya nkhondoyo.
3. Alonda achenjeza.
Afu’la pamodzi.
Yenseyo m’malo ake
Mwa kufuna kwa Ya.
Yehova ali n’nthaŵi;
Nthaŵiyo ikutha
Kuti tilalikire
Za Ufumu wake.