Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/98 tsamba 3
  • Chenjerani ndi Chifundo Chosayenera!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chenjerani ndi Chifundo Chosayenera!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 1/98 tsamba 3

Chenjerani ndi Chifundo Chosayenera!

1 Anthu a Yehova ngodziŵika chifukwa cha mkhalidwe wawo wachifundo ndi kuoloŵa manja. Kaŵirikaŵiri mzimuwo umaoneka mwanjira yeniyeni pamene titsanzira Msamariya wachifundo amene Yesu analankhula za iye m’fanizo lake lomvetsa chisoni. (Luka 10:29-37) Chikhalirechobe, ena amene ali osayenerera kulandira chithandizo cha zinthu zakuthupi angayeseyese kuti apindule ndi chifundo chathu. Chotero, chikondi chathu cha pa ena chiyenera kusonyezedwa mogwirizana ndi “chidziŵitso, ndi kuzindikira konse.”—Afil. 1:9.

2 Mu Mpingo: Mwachitsanzo, munthu wina anganene kuti ali pa ulova kapena angapereke zifukwa zina kuti apemphe chithandizo. Nthaŵi zina anthu amenewa angakhale asakuchita khama kufunafuna ntchito koma amangofuna kuti ena awapatse zinthu zofunika m’moyo. Ponena za otere mtumwi Paulo analamula kuti: “Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.”—2 Ates. 3:10.

3 ‘Nthaŵi ndi zowagwera zosaonedweratu’ zimagwera tonsefe, chotero ngati tili osoŵa zinthu zakuthupi tilibe “chakudya chathu chalero,” sitiyenera kudera nkhaŵa mopambanitsa, popeza Yehova amagaŵira amene amamkonda ndi amene akuchita chifuniro chake. (Mlal. 9:11; Mat. 6:11, 31, 32) Wosoŵayo angakupeze kukhala kopindulitsa kulankhula ndi mmodzi wa akulu. Akulu angakhale akudziŵa makonzedwe aboma olinganizidwira kupereka chithandizo ndipo angakhoze kuthandiza wosoŵayo kulemba mafomu kapena iwo angadziŵe ziyeneretso za opindula ndi makonzedwe otero. Mulimonse mmene zingakhalire, bungwe la akulu lingakhoze kupenda mkhalidwe wa munthu aliyense wopempha chithandizo ndi kusankha zimene zingachitidwe.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:3-16.

4 Onyenga Oyendayenda: Sosaite ikulandirabe mawu akuti ena m’mipingo alimidwa pamsana mwauphyuta ndalama ndi zinthu zina zakuthupi ndi onyenga oyendayenda. Izi siziyenera kutidabwitsa popeza Malemba amachenjeza kuti “anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Tim. 3:13) Kaŵirikaŵiri onyenga amenewa amanama kuti ndalama zawathera ndi kuti afunikira ndalama kuti apeze choyendera ndi chakudya kubwererera kwawo. Ngakhale kuti angamvekere kukhala oona mtima, m’zochitika zambirimbiri iwo sali konse Mboni za Yehova koma kuti akungoyeserera kukhala.

5 Nthaŵi zonse sikokwanira kungokhulupirira zonena munthuyo kuti amadziŵa dzina la woyang’anira winawake m’tauni inayake. Poyendayenda, oyenga amenewo amadziŵa maina a abale ena ndi mipingo imene amasonkhanako. Ngakhale kuti zonena zawo zingamveke ngati zoona, zipendeni.

6 Ngati mlendo akupempha chithandizo, kukakhala kwanzeru kufunsa mmodzi wa akulu mumpingo, amene angatsogoze m’kutsimikizira kuti munthuyo ali mbale wathu. Kaŵirikaŵiri kuchitira telefoni mmodzi wa akulu mumpingo wa munthuyo nkoyenera kuti mbiri ya munthuyo itsimikiziridwe. Abale oona ndi alongo amene mosayembekezereka agwera mumkhalidwe wosoŵa adzamvetsetsa kuti kufufuza kwa mtundu umenewu kukuchitidwira kutetezera ophatikizidwa onse. Ku mbali ina, onyengawo adzaululika mwa kufufuza kotere. Sikuli kofunika kukhala okayikira anthu onse osadziŵika kwa ife, koma tiyenera kuchenjerera onyenga oipawo.

7 Mfumu yanzeru Solomo inalangiza kuti: ‘Oyenera kulandira zabwino usaŵamane; pokhoza dzanja lako kuŵachitira zabwino.’ (Miy. 3:27) Mwa luntha lathu, tingathe kupitirizabe kukhala achifundo pamene tikuchenjerera kuti tisasonyeze chifundo chosayenera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena