Yehova Amapereka Mphamvu Yoposa Yaumunthu
1 Mwaŵi wamtengo wapatali wa utumiki wopatulika—utumiki wachikristu—waikiziridwa kwa ophunzira onse a Yesu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Koma nthaŵi zina kupanda ungwiro kwathu, ndi mavuto tili nawo m’dongosolo la zinthu lino zimatipangitsa kudziona ngati osakwanira kwenikweni.
2 Ngati zimenezo zachitika, kalata ya mtumwi Paulo yomwe analembera Akristu odzozedwa a ku Korinto ingatitonthoze. Analemba kuti: “Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi.” (2 Akor. 4:7) Paulo anali ndi chidaliro, chifukwa anati: “Popeza tili nawo utumiki umene . . . , sitifooka.” (2 Akor. 4:1) Nzoona, tonsefe timafunikiradi kulimbikira, kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” kuti tipitirizebe kulengeza uthenga wabwino ‘osafooka.’ Timafunikira nyonga yochokera kwa Mulungu, yemwe amapereka “mphamvu yoposa yaumunthu.”—Yoh. 10:16; 2 Akor. 4:7b, NW.
3 Nzolimbikitsa kuona kuti Mboni zambiri zili zachangu mosasamala kanthu zoti amayang’anizana ndi chitsutso champhamvu, matenda aakulu, kapena umphaŵi. Tonsefe tiyenera kuzindikira kuti Yehova amachirikiza ntchito yathu yolalikira. M’malo mwakuti tilole zokhumudwitsa kapena mantha kutifooketsa pakulalikira, tiyeni ‘tilimbikebe mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.’—Aef. 6:10; Miy. 24:10.
4 Mmene Tingapezere Mphamvu ya Mulungu: Osaleka kupemphera, mukumapempha thandizo ndi nyonga ya Mulungu. (Aroma 12:12; Afil. 4:6, 7) Ndiyeno, khulupirirani Yehova ndi mtima wanu wonse kuti adzakupatsani mphamvu yoposa yaumunthu. (Miy. 3:5) Ŵerengani zokumana nazo zamakono m’magazini athu, pakuti zimapereka umboni wakuti Yehova akuthandiza atumiki ake lerolino kupirira ziyeso. Gwirizanani kwambiri ndi abale mumpingo, ndipo musamanyalanyaze misonkhano yampingo.—Aroma 1:11, 12; Aheb. 10:24, 25.
5 Tiyenitu tonsefe tichite zimene tingathe kuti tilandire mphamvu ya Yehova—yoposa yaumunthu, imene idzatithandiza kuti tisafooke pantchito yofunika kwambiri imeneyi yolalikira Ufumu.