Nyimbo 81
Kuyamikira Kudekha kwa Mulungu
1. Yehova mphamvu yanuyo
Inapanga zokongola.
Ponseponse chilengedwe
Chimalengeza za ichi.
Ngakhale kukongolako
Kusangalatsa abwino,
Adzawona kukongola
M’chilakiko cha ufumu.
2. Chilungamo chanu M’lungu
Chingathe kuipa konse;
Kutitu tipulumuke,
Simunawonongeretu.
Otchedwa ndi dzina lanu,
Aimba moyamikira
Nafunitsitsa kuwona
Chilakiko cha ufumu.
3. M’chipiliro chanu M’lungu
Tilalikira mbiriyo,
Kusonyeza ’nthu ubwino,
Wopezeka m’Mawu anu.
Mutithandize kunena
Kutinso apulumuke
Pamodzi nafe awone
Ufumu wolakikawo.