Nyimbo 1
‘Lemekeza Yehova, O Moyo Wanga’
1. N’dzalemekeza Yehova—
Milomo yanga imyimbire—
Iye amakhululuka,
Nachotsadi chisoni chonse.
Sakwiya msanga, ngwachifundo,
Zonse zimtsimikizira.
Onse owopa Yehova,
Adzaŵakomera mtima.
2. Yehova ngwachifundodi,
Adziŵa kuti ndife fumbi
Monga duŵa la kuthengo,
Ndimo mmene timafotera.
Iye ndimfumu pazonse;
Ntchito zake ziri zamphamvu.
Tika sunga malangizo,
Adzatichirimikitsa.
3. Yehova anakhazika
Mpando wachifumu kumwamba.
Koma ukoma wa Yehova
Ngwa onse omamumvera.
Mdalitse Yehova angelo;
Mkwezeni ndi mtima wonse.
M’dalitse Yehova nonse.
Dalitsa M’lungu mtimanga.