Nyimbo 122
Kudzisungira Ife Eni Monga “Wamng’ono”
1. Oyanjidwadi ndi awo
Omvera malangizo.
Ntchito ya odalira Ya
Imadalitsidwadi.
Popeza tivutika ndi
Kusalungama kwathu,
Tifune kudzichepetsa
Tigonjere Mulungu.
2. ‘Dzichepetsenitu nokha,’
Kristu anaterodi.
Kumachititsa mtendere,
Umenewu ngwabwino.
Anakhazika chitsanzo.
Anakondwa nakodi
Kugonjera kwa Mulungu
Ndi kumutumikira.
3. Mwanzeru titsogolere
Mu kulemekezana
Ndi kudziŵa kuti Yesu
Anafera abale.
Abalewo nga Mulungu;
Awapatsa maluso.
Tiyeni tidzichepetse
Tikhale auzimu.
4. Lamulo la umutulo
Lithandiza kudziŵa
Kudzichepetsadi tokha
Ndi kusonya chikondi.
Mzimu wa Ya ngopezeka
Kuti utithandize.
Unansi wabwino ndi Ya
Udzatichepetsabe.