Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od mutu 15 tsamba 157-161
  • Ubwino Wogonjera Anthu Amene Akutitsogolera M’gulu la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ubwino Wogonjera Anthu Amene Akutitsogolera M’gulu la Mulungu
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI TIYENERA KUGONJERA NDANI?
  • Zimene Kugonjera Kwaumulungu Kumafuna kwa Ife
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kugonjera Kwaumulungu—Chifukwa Ninji Ndipo ndi Yani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Kukhala Mutu wa Banja Kumatanthauzanji?
    Galamukani!—2004
  • Kodi kugonjera mu Ukwati Kumatanthauzanji?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od mutu 15 tsamba 157-161

MUTU 15

Ubwino Wogonjera Anthu Amene Akutitsogolera M’gulu la Mulungu

TIYENERA kugonjera Yehova yemwe ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse kuti tikhale m’gulu la anthu amene akuchita chifuniro chake. Timalemekeza Mwana wake yemwe ndi Mutu wa mpingo wachikhristu ndiponso timalemekeza anthu amene amatitsogolera pa zinthu zosiyanasiyana. Kugonjera koteroko kumapindulitsa aliyense.

2 Mfundo yakuti anthu azigonjera ulamuliro, inayambira m’munda wa Edeni ndipo imaonekera bwino m’malamulo a Mulungu opezeka pa Genesis 1:28 ndi pa Genesis 2:16, 17. Nyama zinayenera kugonjera anthu ndipo Adamu ndi Hava anayenera kuchita zimene Mulungu amafuna ndi kugonjera ulamuliro wake. Kugonjera ulamuliro wa Mulungu kukanachititsa kuti anthu azikhala mwamtendere ndiponso kuti zinthu ziziwayendera bwino. Mawu amene ali pa 1 Akorinto 11:3, amasonyeza bwino zoti Yehova amafuna kuti tizigonjera winawake. Pamenepa mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” Zimenezi zikusonyeza kuti aliyense kupatulapo Yehova yekha, ali ndi winawake wofunika kumugonjera ngati mutu wake.

3 Anthu ambiri masiku ano samalemekeza anthu amene akuwatsogolera. Chifukwa chiyani? Vutoli linayambira m’munda wa Edeni pamene makolo athu anakana kugonjera Mulungu ngati mutu wawo. (Gen. 3:4, 5) Koma zimene anachitazi sizinawathandize kukhala osangalala. M’malomwake anayamba kulamuliridwa ndi mngelo woipa, Satana Mdyerekezi. Kupanduka kwa anthu oyambirira amenewa, kunachititsa kuti anthu akhale otalikirana ndi Mulungu. (Akol. 1:21) Zotsatira zake n’zakuti anthu ambiri masiku ano akulamulidwa ndi woipayo.​—1 Yoh. 5:19.

4 Kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kugwiritsira ntchito zimene timaphunzirazo, kumatithandiza kuti tisamalamulidwe ndi Satana. Tikadzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa, timakhala titavomereza kuti iye ndi Wolamulira Wamkulu wa moyo wathu. Timagwirizana ndi Mfumu Davide yemwe anavomereza kuti Yehova ndi “mutu pa onse.” (1 Mbiri 29:11) Modzichepetsa timavomereza kuti: “Yehova ndi Mulungu. Iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha. Ndife anthu ake ndi nkhosa zimene akuweta.” (Sal. 100:3) Timadziwa kuti Yehova ndi wamkulu ndiponso kuti ndi woyenera kumugonjera chifukwa ndi amene analenga zinthu zonse. (Chiv. 4:11) Popeza ndife atumiki a Mulungu woona, timatsanzira Yesu Khristu yemwe anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yogonjera Mulungu.

5 Kodi Yesu anaphunzira chiyani pa mavuto amene anakumana nawo ali padziko lapansi? Lemba la Aheberi 5:8 limayankha kuti: “Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.” Yesu anakhalabe wokhulupirika ndi wogonjera kwa Atate wake wakumwamba ngakhale pamene anakumana ndi mavuto. Ndiponso Yesu sanachite kanthu kalikonse mwa iye yekha, sanalankhule za m’maganizo mwake komanso sanadzifunire ulemerero. (Yoh. 5:19, 30; 6:38; 7:16-18) Pochita utumiki, ankasangalala ndi kuchita chifuniro cha Atate wake ngakhale kuti zimenezo zinachititsa kuti anthu azim’tsutsa komanso kumuzunza. (Yoh. 15:20) Ngakhale zinali choncho, Yesu anakhalabe wogonjera kwa Mulungu ndipo “anadzichepetsa” mpaka “imfa ya pamtengo wozunzikirapo.” Kugonjera kwa Yesu kunabweretsa madalitso ambiri. Kunatheketsa kuti anthu adzapulumutsidwe ndi kudzapeza moyo wosatha. Kunachititsanso kuti Yesuyo akwezedwe komanso kunapereka ulemerero kwa Atate wake.​—Afil. 2:5-11; Aheb. 5:9.

KODI TIYENERA KUGONJERA NDANI?

6 Tikamagonjera Mulungu pochita chifuniro chake, timapewa nkhawa ndi mavuto amene anthu omwe sakufuna kugonjera ulamuliro wa Yehova amakumana nawo. Mdani wathu Mdyerekezi, nthawi zonse amayesetsa kuti atiwononge. Tingatetezeke kwa woipayu ngati tikupitirizabe kumutsutsa komanso kukhala odzichepetsa pogonjera Yehova ndi mtima wonse.​—Mat. 6:10, 13; 1 Pet. 5:6-9.

7 Mu mpingo, tikamamvera ndi kugonjera “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene anapatsidwa ulamuliro, timalemekeza Khristu yemwe ndi Mutu wa mpingo. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tizigwirizana. Kugonjera ulamuliro wa Mulungu mu mpingo kudzatithandiza kuti tizitsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu pochita zinthu zokhudza kulambira. Zimenezi zikuphatikizapo mmene timachitira utumiki wathu, kupezeka ndi kuyankha pamisonkhano, kugwirizana ndi akulu komanso kutsatira malangizo onse a gulu la Mulungu.​—Mat. 24:45-47; 28:19, 20; Aheb. 10:24, 25; 13:7, 17.

8 Kugonjera Mulungu kumachititsa kuti mu mpingo wachikhristu mukhale mtendere komanso kuti zonse zizichitika mwadongosolo. Makhalidwe abwino a Yehova amaonekeranso mwa anthu ake. (1 Akor. 14:33, 40) Zimene timaona m’gulu la Yehova, zimatipangitsa kulankhula ngati mmene Mfumu Davide ananenera. Iye ataona kusiyana kwa pakati pa atumiki a Yehova ndi anthu oipa, ananena mosangalala kuti: “Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”​—Sal. 144:15.

9 M’banja, “mutu wa mkazi ndi mwamuna.” Komanso mwamuna amayenera kugonjera Khristu, pamene mutu wa Khristu ndi Mulungu. (1 Akor. 11:3) Akazi ayenera kugonjera amuna awo, ndipo ana ayenera kugonjera makolo awo. (Aef. 5:22-24; 6:1) M’banja mumakhala mtendere aliyense akamatsatira mfundo yogonjera mutu wake.

10 Mwamuna ayenera kukhala mutu wachikondi potsanzira Khristu. (Aef. 5:25-29) Mwamuna akakhala mutu wabwino, mkazi ndi ana ake amamugonjera mosangalala. Udindo wa mkazi ndi kukhala wothandiza kapena mnzake womuyenerera wa mwamuna. (Gen. 2:18) Mkazi akamathandiza ndi kulemekeza mwamuna wake, mwamunayo amamukonda ndipo zimenezi zimachititsa kuti Mulungu alemekezedwe. (1 Pet. 3:1-4) M’banja, amuna ndi akazi akamatsatira malangizo a m’Baibulo ogonjera mutu, amaperekanso chitsanzo chabwino kwa ana awo pa nkhani yogonjera Mulungu.

Munthu amene amagonjera dongosolo la Mulungu lolemekeza mutu amakhala womvera pa zinthu zonse

11 Kugonjera Mulungu kumakhudzanso mmene timaonera “olamulira akuluakulu,” omwe “ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.” (Aroma 13:1-7) Monga nzika zomvera malamulo, Akhristu amakhoma misonkho ndiponso amapereka “zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” (Mat. 22:21) Kuwonjezera pamenepo, akamakonza dongosolo lolalikira m’gawo lawo, amachita zinthu mogwirizana ndi zimene malamulo a m’dziko lawo amanena pa nkhani yosunga chinsinsi. Chifukwa choti timagonjera ndi kumvera olamulira pa zinthu zomwe sizisemphana ndi malamulo olungama a Yehova, timagwiritsa ntchito bwino mphamvu zathu pogwira ntchito yolalikira.​—Maliko 13:10; Mac. 5:29.

12 Munthu amene amagonjera dongosolo la Mulungu lolemekeza mutu amakhala womvera pa zinthu zonse. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene anthu onse azidzagonjera Yehova Mulungu. (1 Akor. 15:27, 28) Anthu amene amagonjera ulamuliro wa Yehova mosangalala adzadalitsidwa kwambiri ndipo adzapitirizabe kumugonjera mpaka kalekale.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena