Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 2/1 tsamba 9-14
  • Kugonjera Kwaumulungu—Chifukwa Ninji Ndipo ndi Yani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugonjera Kwaumulungu—Chifukwa Ninji Ndipo ndi Yani?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Tifunikira Kugonjera Yehova Mulungu
  • Yesu Kristu, Chitsanzo Changwiro cha Kugonjera Kwaumulungu
  • Zitsanzo Zakale za Kugonjera Kwaumulungu
  • Chitsanzo cha Paulo cha Kugonjera
  • Zimene Kugonjera Kwaumulungu Kumafuna kwa Ife
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Ubwino Wogonjera Anthu Amene Akutitsogolera M’gulu la Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kugonjera kwa Mkazi Kodi Kumatanthauzanji?
    Galamukani!—1996
  • Kodi kugonjera mu Ukwati Kumatanthauzanji?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 2/1 tsamba 9-14

Kugonjera Kwaumulungu​—Chifukwa Ninji Ndipo ndi Yani?

‘Ndidziŵa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’​—YEREMIYA 10:23.

1. Kodi ndimitundu yotani ya kudziimira pawekha imene yakhala yofunika mofala?

PAKATI pa zikalata za anthu zotchuka koposa pali chotchedwa Kulengezedwa kwa Kudziimira Pawekha, mwa chimene maiko 13 a ku North America olamuliridwa ndi Briteni m’zaka za zana la 18 analengeza kudziimira kwawo paokha kuchoka ku dziko lowalamulira, Briteni. Iwo anafuna ufulu, ndipo kudziimira paokha kuchoka ku ulamuliro wakunja ndi ufulu zinayendera limodzi. Kudziimira pawekha kwandale zadziko ndi kwachuma kungakhale kwabwino kwambiri. M’nthaŵi zaposachedwapa maiko ena a Kummawa kwa Yuropu anasinthira ku kukudziimira paokha kwandale zadziko. Komabe, kuyenera kuvomerezedwa kuti m’maiko amenewo kudziimira paokha koteroko kwadzetsa mavuto aakulu.

2, 3. (a) Kodi ndimtundu uti wa kudziimira pawekha umene suli wabwino? (b) Kodi chenicheni chimenechi chinagogomezeredwa motani poyambirira?

2 Pamene kuli kwakuti mitundu yosiyanasiyana ya kudziimira pawekha ingakhale yabwino, pali mtundu wina wa kudziimira pawekha umene suli wabwino. Kodi ndiuti umenewo? Ndiwo kudziimira pawekha osadalira Mpangi wa munthu, Yehova Mulungu. Kumeneko sikuli dalitso koma temberero. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti munthu sanalinganizidwe kuti adzichitire zinthu mosadalira Mpangi wake, monga momwe mawu a mneneri Yeremiya ogwidwa pamwambapa akusonyezera molondola. M’kunena kwina, munthu analinganizidwa kuti agonjere kwa Mpangi wake. Kukhala wogonjera kwa Mlengi wathu kumatanthauza kukhala omvera kwa iye.

3 Chenicheni chimenecho chinagogomezeredwa kwa anthu akuthupi aŵiri oyambirira ndi lamulo la Yehova kwa iwo, monga momwe lalembedwera pa Genesis 2:16, 17: ‘Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo, chifukwa tsiku limene udzadya umenewo udzafa ndithu.’ Kukana kugonjera Mlengi wake kunadzetsa uchimo, kuvutika ndi imfa pa Adamu ndi mbadwa zake.​—Genesis 3:19; Aroma 5:12.

4, 5. (a) Kodi nchiyani chimene chakhala chotsatirapo cha kukana kwa anthu kugonjera Mulungu? (b) Kodi ndilamulo lotani limene liri losapeŵeka?

4 Anthu okana kugonjera kwa Mulungu ngopanda nzeru ndipo ali olakwa. M’dziko kwachititsa kusaweruzika, upandu, chiwawa, ndi chisembwere limodzi ndi zotulukapo zake za matenda opatsirana mwakugonana. Ndiponso, kodi mliri wa upandu wa achichepere simachititsidwa kwakukulukulu ndi kukana kwa achichepere kugonjera Yehova, kuphatikizapo makolo awo ndi malamulo a dziko? Mzimu wakudziimira pawekha umenewu ukuwoneka m’njira yachilendo ndi yodzilekerera imene anthu ambiri amavalira ndi m’kalankhulidwe konyansa kamene iwo amagwiritsira ntchito.

5 Koma palibedi kupeŵa lamulo losapeŵeka la Mlengiyo: ‘Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi.’​—Agalatiya 6:7, 8.

6, 7. Kodi nchiyani chimene chiri nakatande wakukana kukhala wogonjera, monga momwe kwawonedwera m’zitsanzo ziti?

6 Kodi nakatande wa kukana kugonjera konseku nchiyani? Kunena mwachidule, ndizo dyera ndi kunyada. Ndicho chifukwa chake Hava, mkazi woyambayo, analola kunyengedwa ndi njoka nadya chipatso choletsedwa. Ngati akanakhala wodekha ndi wodzichepetsa, chiyeso chakufuna kufanana ndi Mulungu​—kudzisankhira chabwino ndi choipa​—sichikanamkopa mtima. Ndipo ngati akanakhala wopanda dyera, sakanafuna chinthu chimene chinaletsedwa mwamphamvu ndi Mpangi wake, Yehova Mulungu.​—Genesis 2:16, 17.

7 Pasanapite nthaŵi yaitali Adamu ndi Hava atachimwa, kunyada ndi dyera zinachititsa Kaini kupha mphwake Abele mwambanda. Ndiponso, dyera linachititsa angelo ena kuchita modziimira paokha, akumasiya malo awo oyamba navala mathupi aumunthu kuti akasangalale ndi zosangalatsa zathupi. Kunyada ndi dyera zinasonkhezera Nimrode ndipo zawoneka kukhala mikhalidwe yaikulu ya olamulira adziko ochuluka chiyambire m’nthaŵi yake.​—1 Yohane 3:12; Yuda 6.

Chifukwa Chake Tifunikira Kugonjera Yehova Mulungu

8-11. Kodi nzifukwa zamphamvu zinayi zotani zosonyezera kugonjera kwathu kwaumulungu?

8 Kodi nchifukwa ninji tifunikira kugonjera Mpangi wathu, Yehova Mulungu? Choyamba, chifukwa chakuti iye ndi Mfumu Yachilengedwechonse. Moyenerera, ulamuliro wonse uli m’manja mwake. Iye ndi Woweruza, Wopereka Malamulo, ndi Mfumu yathu. (Yesaya 33:22) Kunalembedwadi za iye kuti: ‘Zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.’​—Ahebri 4:13.

9 Ndiponso, popeza kuti Mpangi wathu ngwamphamvuyonse, palibe amene angapambane m’kumutsutsa; palibe amene anganyalanyaze kufunikira kwawo kwakukhala ogonjera kwa Iye. Mwamsanga kapena pambuyo pake, awo amene akukana adzawonongedwa monga momwe anachitira Farao wakale ndi mmene adzachitira Satana Mdyerekezi panthaŵi ya Mulungu yokwanira.​—Salmo 136:1, 11-15; Chivumbulutso 11:17; 20:10, 14.

10 Kugonjera ndiko chofunika cha zolengedwa zonse zaluntha chifukwa chakuti izo zikukhalapo kaamba ka chifuno chotumikira Mpangi wawo. Chivumbulutso 4:11 chimalengeza kuti: ‘Muyenera inu, [Yehova, NW] Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwachifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.’ Iye ali Woumba Wamkulu, ndipo amaumba ziŵiya zaumunthu kuti zichite chifuno chake.​—Yesaya 29:16; 64:8.

11 Sitiyenera kunyalanyaza chenicheni chakuti Mpangi wathu ngwanzeruzonse, motero amadziŵa chimene chiri chabwino koposa kwa ife. (Aroma 11:33) Malamulo ake ali ‘kaamba ka ubwino wathu.’ (Deuteronomo 10:12, 13) Choposa zonse, ‘Mulungu ndiye chikondi,’ chotero iye amangofuna chimene chiri chabwino koposa kwa ife. Tiri ndi zifukwa zotisonkhezera zochuluka chotani nanga zokhalira ogonjera kwa Mpangi wathu, Yehova Mulungu!​—1 Yohane 4:8.

Yesu Kristu, Chitsanzo Changwiro cha Kugonjera Kwaumulungu

12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu anasonyezera kugonjera kwaumulungu? (b) Kodi ndimawu a Yesu ati amene amasonyeza mkhalidwe wake wa maganizo wakugonjera?

12 Mosakaikira konse, Mwana wobadwa yekha wa Yehova, Yesu Kristu, amatipatsa chitsanzo changwiro cha kugonjera kwaumulungu. Mtumwi Paulo akutchula zimenezi pa Afilipi 2:6-8: ‘[Yesu], pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, [anadzichepetsanso] yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya [pamtengo wozunzirapo, NW].’ Pamene anali padziko lapansi, Yesu ananena mobwerezabwereza kuti sanachite kanthu kalikonse kodziyambira yekha; sanachite modziimira payekha, koma nthaŵi zonse anakhalabe wogonjera kwa Atate wake wakumwamba.

13 Timaŵerenga pa Yohane 5:19, 30 kuti: ‘Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kuchita kanthu payekha, koma chimene awona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo. Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.’ Mofananamo, iye anapemphera mobwerezabwereza pausiku umene anaperekedwa: “Simonga ndifuna ine, koma inu.”​—Mateyu 26:39, 42, 44; wonaninso Yohane 7:28; 8:28, 42.

Zitsanzo Zakale za Kugonjera Kwaumulungu

14. Kodi Nowa anasonyeza kugonjera kwaumulungu mwanjira zotani?

14 Pakati pa zitsanzo zaumunthu zakale za kugonjera kwaumulungu panali Nowa. Iye anasonyeza kugonjera kwake mwanjira zitatu. Yoyamba, mwakukhala munthu wolungama, wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’tsiku lake, woyenda ndi Mulungu wowona. (Genesis 6:9) Yachiŵiri, mwakumanga chingalawa. ‘Anachita . . . , monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.’ (Genesis 6:22) Yachitatu, mwakulengeza chenjezo la Chigumula chinalinkudza monga ‘mlaliki wa chilungamo.’​—2 Petro 2:5.

15, 16. (a) Kodi Abrahamu anatiikira chitsanzo chabwino chotani cha kugonjera kwaumulungu? (b) Kodi Sara anasonyeza motani kugonjera?

15 Abrahamu anali chitsanzo china chapadera cha kugonjera kwaumulungu. Iye anasonyeza kugonjera mwakumvera lamulo la Mulungu: ‘Tuluka iwe m’dziko lako.’ (Genesis 12:1) Zimenezo zinatanthauza kusiya malo abwino a Uri (mzinda wotchuka, monga momwe kwasonyezedwera ndi zofukulidwa m’mabwinja) kukapupulikapupulika monga wosamukasamuka m’dziko lachilendo kwa zaka zana limodzi. Abrahamu anasonyeza kugonjera kwaumulungu makamaka mwakupambana chiyeso chachikulu chakukhala wofunitsitsa kupereka nsembe mwana wake Isake.​—Genesis 22:1-12.

16 Sara mkazi wa Abrahamu akutipatsa chitsanzo china chabwino cha kugonjera kwaumulungu. Ndithudi, kupupulikapupulika m’dziko lachilendo kunali ndi mavuto ambiri, koma palibe pamene timaŵerenga za kudandaula kwake. Iye anapereka chitsanzo chabwino cha kugonjera kwaumulungu pazochitika ziŵiri pamene Abrahamu anamsonyeza kukhala mlongo wake pamaso pa olamulira achikunja. Pantaŵi zonse ziŵirizo iye sanatsutse, ngakhale kuti anatsala pang’ono kukhala mmodzi wa akazi aang’ono a olamulira achikunja monga chotulukapo. Chochitira umboni kugonjera kwake kwaumulungu ndicho njira imene anatchera mwamuna wake Abrahamu kuti ‘mbuyanga,’ kusonyeza kuti ndiwo unali mkhalidwe wake wamtima.​—Genesis 12:11-20; 18:12; 20:2-18; 1 Petro 3:6.

17. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Isake anasonyeza kugonjera kwaumulungu?

17 Tisaiŵaletu chitsanzo cha kugonjera kwaumulungu choperekedwa ndi Isake mwana wa Abrahamu. Mwambo Wachiyuda umasonyeza kuti Isake anali wazaka pafupifupi 25 pamene Yehova analamula atate wake, Abrahamu, kumpereka nsembe. Ngati Isake akadafuna, akadawatsutsa atate wake mosavuta, amene anali ndi zaka zana limodzi kuposa iye. Koma sanatero. Ngakhale kuti Isake anazizwa ndi kusakhalapo kwa nyama ya nsembe, analolera mofatsa atate wake kumuika pa guwa lansembe ndiyeno kummanga manja ndi miyendo kuti asapalapate pamene mpeni wophera ukagwiritsiridwa ntchito.​—Genesis 22:7-9.

18. Kodi ndimotani mmene Mose anasonyezera kugonjera kwaumulungu kwachitsanzo chabwino?

18 Zaka zambiri pambuyo pake, Mose anatiikira chitsanzo chabwino m’kugonjera kwaumulungu. Zimenezo zikusonyezedwadi ndi kulongosoledwa kwake kukhala “wofatsa woposa anthu onse padziko lapansi.” (Numeri 12:3) Kutsatira kwake momvera malamulo a Yehova kwazaka 40 m’chipululu, ngakhale kuti anali kuyang’anira anthu opanduka okwanira mamiliyoni aŵiri kapena atatu, kumachitira umboni mowonjezereka kugonjera kwake kwaumulungu. Motero cholembedwacho chimati ‘Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.’​—Eksodo 40:16.

19. Kodi ndimawu ati amene Yobu anasonyezera kugonjera kwake kwa Yehova?

19 Yobu ndimunthu winanso amene anatiikira chitsanzo chabwino koposa m’kugonjera kwaumulungu. Pamene Yehova analola Satana kuchotsa chuma chonse cha Yobu, kupha ana ake, ndiyeno kumkantha ndi ‘zironda zoŵaŵa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pa mutu pake,’ mkazi wa Yobu anati kwa iye: ‘Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano kuti ufe.’ Komabe, Yobu anasonyeza kugonjera kwake kwaumulungu mwakunena kwa iye: ‘Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha, tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa?’ (Yobu 2:7-10) Osonyeza mkhalidwe wamaganizo umodzimodziwo ndiwo mawu ake olembedwa pa Yobu 13:15: ‘Angakhale andipha koma ndidzamlindira.’ Ndipo, ngakhale kuti Yobu kwakukulukulu anadera nkhaŵa ndi kudzilungamitsa kwake, sitiyenera kuiŵala kuti potsirizira pake Yehova anati kwa mmodzi wa owonekera kukhala omtonthoza: ‘Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako aŵiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.’ Mosakaikira, Yobu akutipatsa chitsanzo chabwino cha kugonjera kwaumulungu.​—Yobu 42:7.

20. Kodi Davide anasonyeza kugonjera kwaumulungu mwanjira zotani?

20 Kutchula chitsanzo china chimodzi chabe cha m’Malemba Achihebri, pali Davide. Pamene Mfumu Sauli analondalonda Davide ngati nyama, Davide anakhala ndi mipata iŵiri yothetsera mavuto ake mwakupha Sauli. Komabe, kugonjera kwaumulungu kwa Davide kunamletsa kuchita chimenecho. Mawu ake ngolembedwa pa 1 Samueli 24:6 kuti: ‘Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumtsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.’ (Wonaninso 1 Samueli 26:9-11.) Anasonyezanso kugonjera kwake kwaumulungu mwakulandira chidzudzulo pamene analakwa kapena kuchimwa.​—2 Samueli 12:13; 24:17; 1 Mbiri 15:13.

Chitsanzo cha Paulo cha Kugonjera

21-23. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza kugonjera kwaumulungu m’zochitika zosiyanasiyana zotani?

21 M’Malemba Achikristu Achigiriki, tiri ndi chitsanzo chapadera cha kugonjera kwaumulungu mwa mtumwi Paulo. Iye anatsanzira Mbuye wake, Yesu Kristu, m’zimenezi monga momwe anachitira m’mbali zina zonse za uminisitala wake wautumwi. (1 Akorinto 11:1) Ngakhale kuti Yehova Mulungu anamgwiritsira ntchito kwambiri koposa aliyense wa atumwi enawo, Paulo sanachite konse modziimira payekha. Luka akutiuza kuti pamene nkhani inabuka yakuti kaya otembenuka Achikunja anafunikira kudulidwa, ‘abale [a ku Antiokeya] anapatula Paulo ndi Barnaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kumka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.’​—Machitidwe 15:2.

22 Ponena za ntchito ya Paulo yaumishonale, tikuuzidwa pa Agalatiya 2:9 kuti: ‘Pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnaba dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndipo iwo kwa amdulidwe.’ Mmalo mwakuchita modziimira payekha, Paulo anafunafuna chitsogozo.

23 Mofananamo, panthaŵi yotsirizira imene Paulo anali m’Yerusalemu, analandira uphungu woperekedwa ndi akulu kumeneko wonena zakupita kukachisi ndi zakutsatira njira ya Chilamulo kotero kuti onse akathe kuwona kuti iye sanali wopatuka pa Chilamulo cha Mose. Popeza kuti kuchita motero kunawonekera kuchititsa kuti gulu la anthu limuukire, kodi kugonjera kwake akuluwo kunali kulakwa? Kutalitali, monga momwe zikuwonekera m’zimene tikuŵerenga pa Machitidwe 23:11 kuti: ‘Usiku wake Ambuye anaimira pa iye, nati, limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.’

24. Kodi ndimbali zinanso zotani zakugonjera zimene tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira?

24 Ndithudi, Malemba amatipatsa zifukwa zamphamvu zokhalira ogonjera ndi zitsanzo zamphamvu za awo amene anasonyeza kugonjera koteroko. M’nkhani yotsatira, tidzakambitsirana mbali zosiyanasiyana m’zimene tingakhale ogonjera kwa Yehova Mulungu, njira zotithandiza kukhala otero, ndi madalitso amene amatsatirapo.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ndimtundu wotani wa kudziimira pawekha umene suli wabwino?

◻ Kodi nchiyani chimene chiri nakatande wa kukana kukhala wogonjera?

◻ Kodi nzifukwa zotani zimene tifunikira kukhalira ogonjera Yehova?

◻ Kodi nzitsanzo zabwino zotani zimene Malemba amatipatsa za kugonjera kwaumulungu?

[Chithunzi patsamba 10]

Nimrode, wolamulira woyamba kupandukira kugonjera kwaumulungu m’nyengo yokhalako chigumula chisanachitike

[Chithunzi patsamba 13]

Nowa, chitsanzo cholungama cha kugonjera kwaumulungu​—Genesis 6:14, 22

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena