Nyimbo 197
Imbirani Yehova!
1. Tikuimbira Mulungu,
Ndi kuchita mwanzeru.
Molam’lidwa mwana wake
Akulamula dziko.
Tiimba mwachilakiko.
Ya wachita zambiri!
Tifuula m’chitamando
Mothirira mang’ombe.
Popeza Yesu Ndimfumu,
Anthu amuwope.
Wayamba kulamulira.
Timudziŵikitsa.
2. Tiri munthaŵi zozunza,
zowawa ndi nsautso;
Zonga nthaŵi yachisanu,
Yokhala ngati bwinja.
Zaka chikwi zayandika;
Kuipa kudzachoka.
Kudzakhala Paradaiso.
Onse adzakondwera.
Zinthu zonse zatsopano
Tizidikiratu.
Kudziŵa chiyembekezo
Tsata chilungamo.
3. Ya akuchita zamphamvu.
Anthu achita mantha
Mmene asamalirira
Ntchito yofalitsayo.
Ambuye Mfumu ya dziko,
Apatsa madalitso.
Tiyeni timuimbire.
Kuchokera mumtima.
Abale okondedwanu,
Titametu M’lungu.
Ali pampando woyera;
Ulemu ndiwake.