Nyimbo 201
Kukondwera ndi Mtundu wa Mulungu
1. Mwa kulalika Ufumu
Tikufunafuna anthu:
“Idzani mumve uthenga.
Wa chowonadi cha Baibulo.”
Ya aitanatu,
Athawe tsoka lowopsa,
Kumka kuchisangalalo,
m’Dziko Latsopano loikidwa.
(Korasi)
2. Wonani! ‘Mtundu woyera’
Woikidwa ndi Yehova
Mopatulidwa mukhola,
Kulengezatu chipulumutso.
Ya akondwa nafe
Ngati tichita zabwino,
Kutsanzira Kristu wathu;
Tisachoke m’njira ya Mulungu.
(Korasi)
3. Mudzikotu labwinodi,
Mopanda zinthu zovuta,
Wonani! Khamu lokondwa
Muntchito ya Mulungu ya phindu.
Sausanso mtima.
Akupeza chowonadi,
Nachigwiritsira ntchito,
Alemekeza dzina lakelo.
(KORASI)
Idzani mukondwere!
Ndi “mtundu” wa M’lungu
Nenani mbiri yabwinoyi.
Mgwadireni Mulungu.
M’lambireni ndithu.
Mukhale kumbali Yaufumu.