Nyimbo 88
Pemphero la Mtumiki wa Mulungu
1. Atate wakumwamba,
Titame dzina lanu;
Zifundo zikhalitsa,
Zokhulupirikabe.
Zokhulupirikabe,
Inde, zimakhalitsa.
2. Pochita utumiki,
Tiphunzitseni M’lungu.
Malamulo tisunga,
Pokhalatu ndi “nkhosa.”
Pokhalatu ndi “nkhosa,”
Malamulo tisunga.
3. Tigaŵireni nzeru,
Yodzadza ndi chikondi.
Tikhale achifundo,
Ndipo opanda tsankho.
Monga opanda tsankho,
Tikhale achifundo.
4. Tikhale achimwemwe
Muutumiki wanu.
Kupempha sitileka
Muwonjeze Ufumu.
Muwonjeze Ufumu,
Kupempha sitileka.