Nyimbo 87
Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
1. Yehova Tate wakumwamba,
Usiku wopatulika!
Pa Nisani khumi ndi chinayipo,
Panali ulemelero.
Mwanawankhosa anadyedwa,
Israyeli namasuka.
Mbuye wathu anakhetsa mwazi wake
Kukwaniritsa ulosiwo.
2. Tasonkhana pamaso panu,
Tadza monga nkhosa zanu,
Kutamanda chikondi chachikulu
Chomwe chinadzetsa Kristu.
Patsogolo pathupa pali
Gome la vinyo ndi mkate.
Tidziŵa izo ndizo zizindikiro
Za chakudya chomwe tidzidya.
3. Mkatewo ndi thupi la Kristu
Loperekedwa kwa ife.
Chikho ndi chizindikiro cha mwazi
Woombola anthu ife.
Tisunge Chikumbutso ichi
M’maganizo ndi mitima.
Tikayenda mofanafana ndi Kristu,
Tidzapeza moyo wosatha.