Nyimbo 171
Nyimbo Yachilakiko
1. ‘Imbirani Ya, chifukwa ali wokwezekadi.
Apakavalowo Wawamiza munyanja.
Ya ndimphamvu yangadi, Iye wandipulumutsa.
M’lungu wanga; Ndidzamutamanda.
Magaleta a Farao ndi gululo Wawaponyera m’nyanja.
Dzanja lanu lamanja Yehova Lamphamvudi muluso.’
2. Aisrayeli Anaimba za chilakikocho.
M’nthaŵi yathu ino Tiwona chilakiko.
Yesu alamulira, Dongosolo lidzandira.
Tikondwera, Ndi chipulumutso!
Chinjoka Satana, ndi angelo ake—Aponyedwa padziko.
Mwanawankhosayo alakika. Mdimawo wapitadi.
3. Tamandani Ya. Ulemelero ndi mphamvu nzake.
Ufumu wakhala, Kukantha nkhonya msanga.
Tiimba mofuula. Zikomo M’lungu ndi Yesu.
Achimwemwe Kukhala ndi moyo.
Kwa M’lungu wathu Yehova ndi Mesiya Timawayamikira.
Adzatipatsa chipulumutso. Nyimbo idzaimbidwa!