Kodi Kudandaula Konse Nkoipa?
Kodi palinso zokhumudwitsa zina zopweteka kwambiri kuposa zimene sitimadandaula nazo?—Marquis De Custine, 1790-1857.
KWA zaka ziŵiri, mkazi wina wapantchito anali kumangovutidwa ndi wantchito mnzake. Chifukwa chomakanakana, wantchito mnzakeyo anayamba kumnyoza ndi kumnyalanyaza. Kuvutika kwake maganizo kunawononga thanzi lake, koma nanga akanatani? Mofananamo, wophunzira wina yemwe anali wopambana kwambiri m’kalasi anamchotsa sukulu chifukwa chikumbumtima chake sichinamlole kuseŵera nawo maseŵera a karati omwe ankachitika pasukulupo. Onse aŵiriwo anaona kuti analakwiridwa, koma kodi anafunikira kukadandaula? Ngati anati atero, kodi akanayembekezera kuthandizidwa, kapena akanapangitsa kuti zinthu zifike poipa kwambiri?
Madandaulo otere ndi ena ambiri ngofala lerolino, popeza kuti tikukhala ndi anthu opanda ungwiro m’dziko loipa. Madandaulowo amakhala a chilichonse kungoyambira kusakondwa, chisoni, kupweteka, kapena kukwiya ndi mkhalidwe wina mpaka kusumira munthu wina. Anthu ambiri amaona kuti ndi bwino kungopeŵa kudandaula kuti apeŵe kukangana; komabe, kodi munthu ayenera kungokhaladi chete nthaŵi zonse? Kodi Baibulo limati chiyani?
Zotsatirapo Zopweteka kwa Wodandaulayo ndi kwa Enawo
Nzosakayikitsa kuti mzimu wodandauladandaula umavulaza, ndipo Baibulo limautsutsa. Wodandaula amadzivulaza yekha mwakuthupi ndi mwauzimu ndipo amavutitsa anthu amene amadandaula nawowo. Ponena za mkazi wodandaula, mwambi wa Baibulo umati: “Kudonthadontha tsiku lamvula, ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.” (Miyambo 27:15) Kudandaula ndi Yehova kapena ndi zina mwa zopereka zake nkulakwa kwenikweni. Pamene mtundu wa Aisrayeli unadandaula za mana ozizwitsa amene ankapatsidwa paulendo wawo wa zaka 40 m’chipululu, namawatcha kuti “mkate wachabe,” Yehova anatumiza njoka zaululu [NW], kuti zilange odandaula opanda ulemuwo, ndipo ambiri anafa.—Numeri 21:5, 6.
Ndiponso, Yesu analangiza ophunzira ake kuti tisamadandaula za “kachitsotso” ka zolakwa zimene timaona mwa anthu anzathu, koma tizizindikiranso “mtanda” wa zolakwa zathu. (Mateyu 7:1-5) Mofananamo, Paulo anatsutsa woweruza mnzake mwa kudandaula kuti ali “wopanda mawu oŵiringula, . . . pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.” Machenjezo ameneŵa otiletsa kudandaula ayenera kutithandiza kupeŵa kusuliza mosafunikira ndi kupeŵa kukulitsa mzimu wodandaula.—Aroma 2:1.
Kodi Kudandaula Konse Nkoipa?
Choncho, kodi tinganene kuti mitundu yonse ya kudandaula njoipa? Iyayi, tisatero. Baibulo limasonyeza kuti pali zolakwa zambiri m’dziko lokhotali limene tikukhalamo zomwe zifunikira kukonzedwa. Yesu anatchula mwa fanizo woweruza wina wosalungama, yemwe anakakamizika kuweruza mwachilungamo mlandu wa mkazi wamasiye woponderezedwa; kuti ‘asamlemetse ndi kudzaidza kwake.’ (Luka 18:1-8) Pazinthu zina nafenso tiyenera kupitirizabe kudandaula kufikira zolakwika zitawongoleredwa.
Potilimbikitsa kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti udze, kodi Yesu sanali kutisonkhezera kuzindikira kuti dziko lilipoli lili ndi zolakwa zambiri ndipo tiyenera ‘kulilira’ Mulungu kuti akonze zinthu? (Mateyu 6:10) Pamene “kulira” ponena za kuipa kwa Sodomu ndi Gomora kunafika m’makutu mwake, Yehova anatumiza amithenga ake kuti ‘akaone ngati anachita monse monga kulira kwake’ kuti iye akonze zinthu. (Genesis 18:20, 21) Awo amene anadandaula kwa Yehova anapeza mpumulo pamene iye anawononga mizinda yonse iŵiriyo ndi anthu ake oipa.
Mpingo Wachikristu
Kodi zingakhale zosiyana pakati pa abale a mumpingo wachikristu? Ngakhale kuti ali amuna ndi akazi opanda ungwiro, Akristu amayesetsa kutumikira Mulungu mumtendere ndi mogwirizana. Komabe, pamabuka mavuto amene angachititse ena kudandaula ndi kufuna kuti zinthu ziwongoleredwe. M’zaka za zana loyamba, vuto linabuka mumpingo wa odzozedwa pambuyo pa Pentekoste. Akristu ambiri ongotembenuka kumene anatsala ku Yerusalemu kuti alangizidwe ndi kulimbikitsidwa. Ankagaŵana chakudya chimene anali nacho. Komabe, “kunauka chidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo anaiŵalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.” M’malo mowatsutsa odandaulawo kuti anali kuvutitsa, atumwi anachitapo kanthu kukonza zolakwazo. Inde, anthu akadandaula moyenera, mwaulemu ndi mwa njira yabwino, oyang’anira mpingo amawamvetsera modzichepetsa.—Machitidwe 6:1-6; 1 Petro 5:3.
Kudandaula kwa Anthu Oyenera
Kodi mwaona pazitsanzo zili pamwambazo kuti madandaulo ayenera kuperekedwa mwa njira yabwino ndiponso kwa munthu woyenera? Mwachitsanzo, munthu sangapeze thandizo ngati adandaula kwa apolisi ponena za kukwera kwa msonkho kapena kwa woweruza ponena za matenda ake. Mofananamo, sikungakhale koyenerera kudandaula za nkhani ina yake ya mumpingo kapena kunja kwa mpingo kwa munthu amene alibepo udindo kapena amene sangathandizepo.
M’maiko ambiri lerolino, muli makhoti ndi maulamuliro ena oyenera kumene anthu angakadandauleko ndi chiyembekezo chopezako thandizo. Pamene wophunzira amene watchulidwa kuchiyambi kwa nkhani ino anakadandaula kukhoti, oweruza anaweruza kuti iye sanalakwe, anambwezeretsa kusukulu, ndipo sukuluyo inampepesa. Mofananamo, wantchito wamkazi wovutitsidwa uja, anathandizidwa ndi bungwe loimira akazi ogwira ntchito. Oyang’anira sukuluyo anampepesa. Mabwana ake anachitapo kanthu pofuna kuthetsa mkhalidwe wovutitsa akazi.
Komabe, tisayembekezere kuti madandaulo onse adzayankhidwa mofananamo. Mfumu yanzeru Solomo ananena zoona kuti: “Chokhotakhota sichingawongokenso.” (Mlaliki 1:15) Tingachite bwino kuzindikira kuti nkhani zina zidzangofuna kudikira kuti Mulungu adzaziwongolere panthaŵi yake.
[Chithunzi patsamba 31]
Akulu, amamvetsera madandaulo oyenera ndi kuchitapo kanthu