Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 3/1 tsamba 8-13
  • Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunika kwa Madyerero Aakulu
  • M’Nthaŵi ya Mafumu a Mumzere wa Davide
  • Atabwerako Kuukapolo
  • M’Zaka za Zana Loyamba C.E.
  • “Iwe Uzikhala Wosangalala Basi”
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Zikondwerero Zomwe Zimatikhudza
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Nsanja ya Olonda—1998
w98 3/1 tsamba 8-13

Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli

“Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m’malo amene iye adzasankha, katatu m’chaka . . . ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu.”​—DEUTERONOMO 16:16.

1. Kodi tinganenenji pankhani ya madyerero a m’nthaŵi za Baibulo?

KODI mumaganiza chiyani mukalingalira za madyerero? Pamadyerero ena m’nthaŵi zakale anthu anali kuchita mopambanitsa ndiponso kuchita chisembwere. Ndipo ndi mmene zimakhaliranso pamadyerero ena amakono. Koma madyerero olongosoledwa m’Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli sanali otero. Pamene kuli kwakuti zinali nthaŵi za chisangalalo, anawatchanso “masonkhano opatulika.”​—Levitiko 23:2.

2. (a) Kodi amuna achiisrayeli anafunikira kuchitanji katatu pachaka? (b) Monga momwe Deuteronomo 16:16 imagwiritsirira ntchito liwu lakuti “madyerero,” kodi madyererowo ndiwo chiyani?

2 Amuna okhulupirika achiisrayeli​—nthaŵi zambiri atatsagana ndi mabanja awo​—anali kupeza chisangalalo chotsitsimutsa poyenda ulendo wa ku Yerusalemu, ‘malo amene Yehova anasankha,’ ndipo anali kupanga zopereka mooloŵa manja pochirikiza madyerero atatu aakulu. (Deuteronomo 16:16) Buku lakuti Old Testament Word Studies limafotokoza liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “madyerero” pa Deuteronomo 16:16 kukhala “nthaŵi yachisangalalo chachikulu . . . pamene anali kupereka nsembe ndi kuchita mapwando pokondwerera zinthu zosaiŵalika zimene Mulungu anawachitira.”a

Kufunika kwa Madyerero Aakulu

3. Kodi madyerero atatu apachakawo anali kukumbutsa za madalitso otani?

3 Popeza kuti Aisrayeli anali alimi, iwo anali kudalira Mulungu kuti awadalitse mwa kuwagwetsera mvula. Madyerero atatu aakulu m’Chilamulo cha Mose anali kuchitika panthaŵi yotuta barele kuchiyambi kwa nyengo yangululu, nthaŵi yotuta tirigu chakumapeto kwa ngululu, ndi nthaŵi yotuta zina zonse chakumapeto kwa chilimwe. Zimenezi zinali nthaŵi zachisangalalo ndi chiyamikiro chachikulu kwa Mwini njira ya mvula ndiponso Mpangi wa dziko lotulutsa zakudya limenelo. Koma madyererowo analoŵetsamo zina zambiri.​—Deuteronomo 11:11-14.

4. Kodi madyerero oyamba ankakhalako pokondwerera chochitika chosaiŵalika chotani?

4 Madyerero oyamba anali kuchitika m’mwezi woyamba pakalenda yakale ya m’Baibulo, kuyambira pa Nisani 15 mpaka 21, masiku amene leroli angakhale chakumapeto kwa March kapena kuchiyambi kwa April. Madyererowa anali kutchedwa kuti Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, komanso popeza kuti anali kukhalako tsiku lotsatira Paskha wa Nisani 14, iwo anali kutchedwanso kuti “madyerero a paskha.” (Luka 2:41, NW; Levitiko 23:5, 6) Madyerero ameneŵa anali kukumbutsa Aisrayeli za kulanditsidwa kwawo kuchizunzo cha ku Igupto, ndipo mkate wopanda chotupitsawo unatchedwa kuti “mkate wa chizunziko.” (Deuteronomo 16:3) Unawakumbukutsa za kuti kutuluka kwawo mu Igupto kunali kofulumira moti analibe nthaŵi yoika chotupitsa ku mitanda yawo ndi kuiyembekezera kuti itupe. (Eksodo 12:34) Pamadyerero ameneŵa m’nyumba iliyonse ya Mwisrayeli simunayenera kupezeka mkate wokhala ndi chotupitsa. Aliyense wochita nawo madyererowa, kuphatikizapo mlendo, amene anadya mkate wokhala ndi chotupitsa anayenera kulangidwa mwa kuphedwa.​—Eksodo 12:19.

5. Kodi ndi mwaŵi wotani umene ayenera kuti anaukumbukira pamadyerero achiŵiri, ndipo ndani enanso amene anayenera kusangalala nawo?

5 Madyerero achiŵiri anali kuchitika patapita milungu isanu ndi iŵiri (masiku 49) kuchokera pa Nisani 16 ndipo anali kukhalako patsiku lachisanu ndi chimodzi m’mwezi wachitatu, Sivani, umene lero ndi chakumapeto kwa May. (Levitiko 23:15, 16) Madyererowo anali kutchedwa Madyerero a Masabata (m’nthaŵi ya Yesu, anali kutchedwa Pentekoste, kutanthauza “cha Makumi Asanu” m’Chigiriki), ndipo anali kuchitika chapafupi ndi nthaŵi yapachaka imodzimodziyo imene Israyeli analoŵa m’pangano la Chilamulo paphiri la Sinai. (Eksodo 19:1, 2) Pamadyerero ameneŵa Aisrayeli okhulupirika ayenera kuti anasinkhasinkha ponena za mwaŵi wawo wa kukhala opatulidwa monga mtundu wopatulika wa Mulungu. Kukhala kwawo anthu apadera a Mulungu kunafuna kuti azimvera Chilamulo cha Mulungu, monga lamulo la kusamalira osauka mwachikondi kuti nawonso asangalale pamadyerero ameneŵa.​—Levitiko 23:22; Deuteronomo 16:10-12.

6. Kodi madyerero achitatu anakumbutsa anthu a Mulungu za chochitika chiti?

6 Omaliza mwa madyerero atatu aakulu apachaka anali kutchedwa kuti Madyerero a Kututa, kapena kuti Madyerero a Misasa. Anali kukhalako m’mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Tishri, kapena kuti Etanimu, kuyambira patsiku la 15 mpaka patsiku la 21, masiku amene lero ali kuchiyambi kwa October. (Levitiko 23:34) Panthaŵiyi, anthu a Mulungu anali kukhala panja pa nyumba zawo kapena padenga la nyumba zawo m’misasa yopangidwa ndi nthambi ndi masamba a mitengo. Zimenezi zinali kuwakumbutsa za ulendo wawo wazaka 40 wochokera ku Igupto kupita ku Dziko Lolonjezedwa, pamene mtunduwo unaphunzira kudalira pa Mulungu kuti awapatse zosoŵa zawo zatsiku ndi tsiku.​—Levitiko 23:42, 43; Deuteronomo 8:15, 16.

7. Kodi tikupindula motani mwa kupenda madyerero a m’Israyeli wakale?

7 Tiyeni tionenso madyerero ena amene anali osaiŵalika m’mbiri ya anthu akale a Mulungu. Zimenezi ziyenera kutilimbikitsa lerolino, popeza kuti ifenso tikuuzidwa kuti tizisonkhana pamodzi mokhazikika mlungu uliwonse ndiponso katatu pachaka pamisonkhano ikuluikulu.​—Ahebri 10:24, 25.

M’Nthaŵi ya Mafumu a Mumzere wa Davide

8. (a) Kodi ndi madyerero osaiŵalika otani amene anachitika m’masiku a Mfumu Solomo? (b) Kodi tikuyembekezera chimake chotani cha Madyerero a Misasa ophiphiritsira?

8 Chikondwerero chosaiŵalika panthaŵi ya Madyerero a Misasa chinachitika mu ulamuliro waulemerero wa Mfumu Solomo, mwana wa Davide. “Khamu lalikulu ndithu” linasonkhana kuchokera kumalekezero a Dziko Lolonjezedwa kaamba ka Madyerero a Misasa ndi kupatuliridwa kwa kachisi. (2 Mbiri 7:8) Madyererowo atatha, Mfumu Solomo analola opezekapowo kupita, amene “anadalitsa mfumu, napita kumahema awo osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israyeli anthu ake.” (1 Mafumu 8:66) Amenewotu analidi madyerero osaiŵalika. Lerolino, atumiki a Mulungu akuyembekezera chimake cha Madyerero a Misasa ophiphiritsira pamapeto a Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Solomo Wamkulu, Yesu Kristu. (Chivumbulutso 20:3, 7-10, 14, 15) Panthaŵiyo, anthu okhala kungondya zonse za dziko lapansi, kuphatikizapo oukitsidwa ndiponso opulumuka Armagedo, adzagwirizana polambira Yehova Mulungu mosangalala.​—Zekariya 14:16.

9-11. (a) Kodi nchiyani chinachititsa kuti kukhale madyerero osaiŵalika m’masiku a Mfumu Hezekiya? (b) Kodi nchitsanzo chotani chimene ambiri ochokera ku ufumu wakumpoto wa mafuko khumi anapereka, ndipo kodi chimatikumbutsa chiyani lerolino?

9 Madyerero ena apadera osimbidwa m’Baibulo anachitika utatha ulamuliro wa Mfumu Ahazi woipayo, amene anatseka kachisi naloŵetsa ufumu wa Yuda mumpatuko. Woloŵa m’malo mwa Ahazi anali Mfumu Hezekiya wabwinoyo. M’chaka choyamba cha ulamuliro wake, ali ndi zaka zakubadwa 25, Hezekiya anayambitsa ntchito yaikulu yobwezeretsa zinthu ndi kuwongolera. Nthaŵi yomweyo anatsegula kachisi nalinganiza kuti akonzedwe. Kenako mfumuyo inatumiza makalata kwa Aisrayeli okhala mu ufumu wankhanza wa Israyeli kumpoto, kuwaitana kuti abwere kudzakondwerera Paskha ndi Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa. Ambiri anabwera, ngakhale kuti anzawo anawatonza.​—2 Mbiri 30:1, 10, 11, 18.

10 Kodi madyererowo anayenda bwino? Baibulo limasimba kuti: “Ndipo ana a Israyeli opezeka m’Yerusalemu anachita madyerero a mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi aŵiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa.” (2 Mbiri 30:21) Aisrayeli amenewo anapereka chitsanzo chabwino chotani nanga kwa anthu a Mulungu lerolino, ambiri amene amapirira chitsutso ndi kuyenda maulendo aatali kuti akapezeke pamisonkhano yachigawo!

11 Mwachitsanzo, talingalirani za Misonkhano Yachigawo itatu ya “Kudzipereka Kwaumulungu” imene inachitika ku Poland mu 1989. Ambiri mwa anthu 166,518 amene anapezekapo anachokera ku dziko limene kale linali Soviet Union ndi kumaiko ena a Eastern Europe kumene ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa panthaŵiyo. Buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdomb likuti: “Kwa ena amene anafika pamisonkhanoyo, inali nthaŵi yawo yoyamba kupezeka pamsonkhano waukulu wa anthu a Yehova oposa 15 kapena 20. Mitima yawo inadzala ndi chiyamikiro poona zikwi makumi ambiri m’mabwalo a maseŵero, kupemphera nawo pamodzi, ndi kuimba nawo nyimbo zotamanda Yehova.”​—Tsamba 279.

12. Kodi nchiyani chinachititsa kuti kukhale madyerero osaiŵalika mu ulamuliro wa Mfumu Yosiya?

12 Hezekiya atamwalira, anthu a ku Yuda anayambanso kulambira konyenga mu ulamuliro wa Mfumu Manase ndi Mfumu Amoni. Kenako panabweranso ulamuliro wa mfumu ina yabwino, Yosiya wachinyamatayo, amene anachitapo kanthu molimba mtima kuti abwezeretse kulambira koona. Pamene anali ndi zaka 25 zakubadwa, Yosiya analamula kuti kachisi akonzedwe. (2 Mbiri 34:8) Pochita ntchito yokonza imeneyo, Chilamulo cholembedwa ndi Mose chinapezeka m’kachisimo. Mfumu Yosiya anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anaŵerenga m’Chilamulo cha Mulungu ndipo analamula kuti chiŵerengedwe kwa anthu onse. (2 Mbiri 34:14, 30) Ndiyeno, malinga ndi zimene zinalembedwa, anapanga makonzedwe okondwerera Paskha. Ndiponso mfumuyo inapereka chitsanzo chabwino mwa kupereka chopereka chachikulu kuti madyererowo achitike. Chotero, Baibulo limasimba kuti: “Panalibe Paskha wochitika m’Israyeli wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samueli mneneri.”​—2 Mbiri 35:7, 17, 18.

13. Kodi madyerero a Hezekiya ndi Yosiya amatikumbutsanji lerolino?

13 Ntchito ya kuwongolera yochitidwa ndi Hezekiya ndi Yosiya ikufanana ndi ntchito yobwezeretsa yosangalatsa zedi imene yachitika pakati pa Akristu oona chiyambire nthaŵi imene Yesu Kristu anakhala pampando wachifumu mu 1914. Monga momwe zinalili makamaka pamene Yosiya anali kuwongolera zinthu, kubwezeretsa kwamakono kumeneku kwazikidwa pazolembedwa m’Mawu a Mulungu. Ndiponso, monga m’masiku a Hezekiya ndi Yosiya, kubwezeretsa kwamakono kwachitika ndi misonkhano ikuluikulu imene yafotokoza maulosi osangalatsa kwambiri a m’Baibulo ndi kufotokoza matanthauzo a mapulinsipulo a m’Baibulo panthaŵi yake. Chiŵerengero chachikulu cha amene abatizidwa chawonjezeranso chimwemwe pamisonkhano yolangiza imeneyi. Monga Aisrayeli olapa m’masiku a Hezekiya ndi Yosiya, obatizidwa chatsopano asiya ntchito zoipa za m’Dziko Lachikristu ndi za m’dziko lonse la Satana. Mu 1997 anthu oposa 375,000 anabatizidwa monga chizindikiro cha kudzipatulira kwawo kwa Mulungu woyera, Yehova​—avareji ya anthu oposa 1,000 patsiku.

Atabwerako Kuukapolo

14. Kodi nchiyani chinachititsa kuti madyerero a mu 537 B.C.E. akhale osaiŵalika?

14 Yosiya atamwamlira, mtunduwo unayambanso kulambira konyenga konyansa. M’kupita kwa nthaŵi, m’chaka cha 607 B.C.E., Yehova analanga anthu ake mwa kuchititsa kuti magulu ankhondo achibabulo aukire Yerusalemu. Mzindawo ndi kachisi wake zinasakazidwa, ndipo dzikolo linasanduka bwinja. Ndiyeno panapita zaka 70 Ayuda ali muukapolo ku Babulo. Kenako Mulungu anadzutsanso otsalira a Ayuda olapa, amene anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa kukabwezeretsa kulambira koona. Iwo anafika ku mzinda wosakazidwawo wa Yerusalemu m’mwezi wachisanu ndi chiŵiri m’chaka cha 537 B.C.E. Chinthu choyamba chimene anachita ndicho kumanga guwa loperekerapo nsembe za tsiku ndi tsiku nthaŵi zonse monga momwe pangano la Chilamulo linanenera. Imeneyo inali nthaŵi ya phwando linanso losaiŵalika. ‘Anachita madyerero a misasa monga kwalembedwa.’​—Ezara 3:1-4.

15. Kodi otsalira obwezeretsedwa mu 537 B.C.E. anali ndi ntchito yotani yoti aichite, ndipo mkhalidwe wofananawo unakhalapo motani mu 1919?

15 Anthu ameneŵa amene anabwerako kuukapolo anali ndi ntchito yaikulu kwambiri yoti aichite​—kumanganso kachisi wa Mulungu ndi Yerusalemu pamodzi ndi malinga ake. Anansi awo ansanje anali kuwatsutsa koopsa. Pamene anali kumanga kachisiyo, linali “tsiku la tinthu tating’ono.” (Zekariya 4:10) Mkhalidwewo unafanana ndi wa Akristu okhulupirika odzozedwa mu 1919. M’chaka chosaiŵalika chimenecho, iwo anamasulidwa kuukapolo wauzimu m’Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Iwo anali zikwi zingapo zokha ndipo anayang’anizana ndi dziko lodana nawo. Kodi adani a Mulungu anali kudzalepheretsa kupita patsogolo kwa kulambira koona? Yankho la funso limenelo limatikumbutsa za chikondwerero cha madyerero aŵiri omaliza olembedwa m’Malemba Achihebri.

16. Kodi nchiyani chimene chinali chapadera pamadyerero a mu 515 B.C.E.?

16 M’kupita kwa nthaŵi kachisiyo anamangidwanso m’mwezi wa Adara m’chaka cha 515 B.C.E., nthaŵi ya madyerero a m’ngululu ya Nisani. Baibulo limasimba kuti: “Nasunga madyerero a mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi aŵiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja awo mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.”​—Ezara 6:22.

17, 18. (a) Kodi ndi madyerero ena osaŵalika ati amene anachitika m’chaka cha 455 B.C.E.? (b) Kodi tili motani m’chochitika chofananacho lerolino?

17 Patapita zaka 60, m’chaka cha 455 B.C.E., panachitikanso madyerero osaiŵalika. Madyerero a Misasa a chakacho anakhalako pamapeto a kumangidwanso kwa malinga a Yerusalemu. Baibulo limasimba kuti: “Ndi msonkhano wonse wa iwo otuluka m’ndende anamanga misasa, nakhala m’misasamo; pakuti chiyambire masiku a Yesuwa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israyeli sanatero. Ndipo panali chimwemwe chachikulu.”​—Nehemiya 8:17.

18 Kumenekotu kunali kubwezeretsa kosaiŵalika kwa kulambira koona kwa Mulungu pakati pa chitsutso choopsa! Zilinso chimodzimodzi lerolino. Ngakhale kuti nthaŵi zina kwabuka chizunzo ndi chitsutso, ntchito yaikulu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu yafika kumalekezero a dziko lapansi, ndipo uthenga wachiŵeruzo wa Mulungu walengezedwa ponseponse. (Mateyu 24:14) Kusindikizidwa chizindikiro komaliza kwa otsalira odzozedwa a 144,000 kukuyandikira. Anzawo a “nkhosa zina” oposa mamiliyoni asanu asonkhanitsidwa m’mitundu yonse kukhala “gulu limodzi” ndi otsalira odzozedwa. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:3, 9, 10) Kumenekotu ndi kukwaniritsidwa kwabwino chotani nanga kwa chithunzi chaulosi cha Madyerero a Misasa! Ndipo ntchito yaikulu kwambiri imeneyi yotuta idzapitirizabe mpaka m’dziko latsopano pamene anthu oukitsidwa miyandamiyanda adzaitanidwa kuti iwonso achite nawo Madyerero a Misasa ophiphiritsira.​—Zekariya 14:16-19.

M’Zaka za Zana Loyamba C.E.

19. Kodi nchiyani chinachititsa kuti Madyerero a Misasa a m’chaka cha 32 C.E. akhale apadera?

19 Madyerero amene Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu anapezekapo, mosakayikira ndiwo anali ena mwa madyerero apadera kwambiri olembedwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, talingalirani za nthaŵi imene Yesu anapezeka pa Phwando la Misasa (kapena kuti Madyerero a Misasa) m’chaka cha 32 C.E. Iye anagwiritsira ntchito chochitikacho pophunzitsa choonadi chofunika kwambiri ndipo anachirikiza chiphunzitso chake mwa kugwira mawu m’Malemba Achihebri. (Yohane 7:2, 14, 37-39) Nthaŵi zonse paphwando limeneli panali kukhala mwambo woyatsa nyali pazoikapo nyali zinayi zazikulu kwambiri m’bwalo lamkati la kachisi. Zimenezi zinathandizira kuti apitirize kusangalala ndi phwandolo mpaka usiku. Mwachionekere, Yesu anali kusonya ku nyali zazikulu kwambiri zimenezi pamene anati: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.”​—Yohane 8:12.

20. Kodi nchifukwa ninji Paskha wa m’chaka cha 33 C.E. anali wapadera?

20 Ndiyeno kunali Paskha ndi Phwando la Mkate Wopanda Chotupitsa m’chaka chosaiŵalikacho cha 33 C.E. Pa Tsiku la Paskha limenelo, Yesu anaphedwa ndi adani ake ndipo anakhala Mwanawankhosa wophiphiritsira wa pa Paskha, amene anafa kuti achotse “tchimo lake la dziko lapansi!” (Yohane 1:29; 1 Akorinto 5:7) Patapita masiku atatu, pa Nisani 16, Mulungu anaukitsa Yesu ali ndi thupi lauzimu losakhoza kufa. Zimenezi zinachitika panthaŵi imene anali kupereka zipatso zoundukula potuta barele monga momwe Chilamulo chinanenera. Choncho, Ambuye Yesu Kristu woukitsidwayo anakhala “chipatso choundukula cha iwo akugona.”​—1 Akorinto 15:20.

21. Kodi nchiyani chinachitika pa Pentekoste wa 33 C.E.?

21 Phwando lapadera kwambiri linali la Pentekoste mu 33 C.E. Patsikuli Ayuda ambiri ndi otembenukira kuchiyuda anasonkhana ku Yerusalemu, kuphatikizapo ophunzira a Yesu okwanira ngati 120. Phwandolo lili mkati, Ambuye Yesu Kristu woukitsidwayo anatsanulira mzimu woyera wa Mulungu pa anthu 120 amenewo. (Machitidwe 1:15; 2:1-4, 33) Chotero pomwepo iwo anadzozedwa nakhala mtundu watsopano wosankhidwa wa Mulungu kudzera m’pangano latsopano limene Yesu Kristu anali nkhoswe yake. Paphwando limenelo mkulu wa ansembe wa Ayuda anali kupereka kwa Mulungu nsembe ya mikate iŵiri yokhala ndi chotupitsa yopangidwa ndi zipatso zoundukula za nyengo ya kututa tirigu. (Levitiko 23:15-17) Mikate yokhala ndi chotupitsa imeneyi imaimira anthu opanda ungwiro 144,000 amene Yesu ‘anagulira Mulungu’ kuti atumikire monga ‘ufumu ndi ansembe . . . kuchita ufumu padziko.’ (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3) Zonena kuti olamulira akumwamba ameneŵa achokera kunthambi ziŵiri za mtundu wa anthu wauchimo, Ayuda ndi Akunja, zikusonyezedwanso ndi mikate iŵiri yokhala ndi chotupitsa.

22. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu samakondwerera madyerero a m’pangano la Chilamulo? (b) Kodi tidzakambitsirana chiyani m’nkhani yotsatira?

22 Pangano latsopano litayamba kugwira ntchito pa Pentekoste wa 33 C.E., zimenezo zinatanthauza kuti pangano lakale la Chilamulo linatha ntchito pamaso pa Mulungu. (2 Akorinto 3:14; Ahebri 9:15; 10:16) Zimenezo sizikutanthauza kuti Akristu odzozedwa ngopanda lamulo. Iwo amatsatira malamulo a Mulungu amene Yesu Kristu anaphunzitsa ndipo analembedwa m’mitima mwawo. (Agalatiya 6:2) Choncho, Akristu samachita madyerero atatu apachakawo pokhala anali mbali ya pangano lakale la Chilamulo. (Akolose 2:16, 17) Komabe, tingaphunzirepo zambiri pa mzimu wa atumiki a Mulungu amene analiko Chikristu chisanakhaleko ponena za madyerero awo ndi misonkhano ina ya kulambira. M’nkhani yathu yotsatira, tidzakambitsirana zitsanzo zimene mosakayikira zidzasonkhezera onse kuyamikira kufunika kwa kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse.

[Mawu a M’munsi]

a Onaninso buku la Insight on the Scriptures, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., Voliyumu 1, tsamba 820, danga loyamba, ndime 1 ndi 3, pamutu wakuti “Festival.”

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Mafunso Obwereza

◻ Kodi madyerero atatu aakulu a Aisrayeli anali ndi chifuno chotani?

◻ Kodi pamadyerero a Hezekiya ndi Yosiya panachitikanji?

◻ Kodi ndi madyerero osaiŵalika otani amene anachitika m’chaka cha 455 B.C.E., ndipo nchifukwa ninji ali olimbikitsa kwa ife?

◻ Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kuti Paskha ndi Pentekoste wa 33 C.E. zikhale zapadera?

[Bokosi patsamba 12]

Zimene Madyererowo Akutiphunzitsa Lerolino

Onse amene akufuna kuti apindule kwamuyaya ndi nsembe ya Yesu yowatetezera ku machimo ayenera kutsatira tanthauzo la Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa. Madyerero ophiphiritsira ameneŵa ndiwo chikondwerero cha Akristu odzozedwa chifukwa cha kulanditsidwa kwawo kuchokera ku dziko loipali ndi kumasulidwa kwawo ku choloŵa cha uchimo kudzera mwa dipo la Yesu. (Agalatiya 1:4; Akolose 1:13, 14) Madyerero enieniwo anali kuchitika kwa masiku asanu ndi aŵiri​—nambala imene m’Baibulo imaimira kukwanira kwauzimu. Madyerero ophiphiritsira akuchitika mokwanira nthaŵi yonse imene mpingo wa Akristu odzozedwa udzakhala padziko lapansi ndipo madyererowo ayenera kuchitidwa ndi “kuona mtima, ndi choonadi.” Zimenezi zikutanthauza kuchenjera nthaŵi zonse ndi chotupitsa chophiphiritsira. M’Baibulo, chotupitsa chimagwiritsiridwa ntchito kuimira ziphunzitso zopotoka, chinyengo, ndi kuipa. Alambiri oona a Yehova ayenera kuda chotupitsa chimenechi, osachilola kuipitsa miyoyo yawo ndiponso osachilola kuwononga chiyero cha mpingo wachikristu.​—1 Akorinto 5:6-8; Mateyu 16:6, 12.

[Chithunzi patsamba 9]

Mtolo wa barele watsopano unali kuperekedwa nsembe chaka chilichonse pa Nisani 16, tsiku limene Yesu anaukitsidwa

[Chithunzi patsamba 10]

Yesu ayenera kuti anasonya ku nyali za pamadyerero pamene anadzitcha “kuunika kwa dziko”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena