Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 3/15 tsamba 4-7
  • Chifukwa Chake Zozizwitsa Zokha sizimabala Chikhulupiriro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Zozizwitsa Zokha sizimabala Chikhulupiriro
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Zozizwitsa Sizinabale Chikhulupiriro
  • Tanthauzo la Chikhulupiriro Choona
  • Kukhulupirira Popanda Kuona
  • Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Zozizwitsa—Kodi Zinachitikadi?
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Umboni Woti Zozizwitsa Zotchulidwa M’Baibulo Zinachitikadi
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 3/15 tsamba 4-7

Chifukwa Chake Zozizwitsa Zokha sizimabala Chikhulupiriro

KUKHULUPIRIRA nkulinga utaona. Ambiri amaganiza choncho. Ena amati angakhulupirire Mulungu ngati angadzivumbule yekha mwanjira ina yozizwitsa. Mwinamwake zingakhale choncho, koma kodi kukhulupirira koteroko kungakhale chikhulupiriro chenicheni?

Talingalirani Aisrayeliwo, Kora, Datani, ndi Abiramu. Baibulo limasonyeza kuti anali mboni zoona ndi maso za zozizwitsa zoopsa za Mulungu: miliri khumi pa Igupto, kumasuka kwa mtundu wa Israyeli popyola Nyanja Yofiira, ndi kufafanizidwa kwa Farao wa Igupto ndi gulu lake lankhondo. (Eksodo 7:19–11:10; 12:29-32; Salmo 136:15) Kora, Datani, ndi Abiramu anamvanso Yehova akulankhula ali kumwamba ku Phiri la Sinai. (Deuteronomo 4:11, 12) Komabe, pasanapite nthaŵi yaitali zitachitika zozizwitsa zimenezi, amuna atatuwo anasonkhezera kupandukira Yehova ndi atumiki ake amene anawaika.​—Numeri 16:1-35; Salmo 106:16-18.

Pafupifupi zaka 40 pambuyo pake, mneneri wotchedwa Balamu anaonanso chozizwitsa. Ngakhale pamene mngelo analoŵererapo sanaope kukhala kumbali ya adani a Mulungu, Amoabu. Mosasamala kanthu za chozizwitsa chimenecho, Balamu anatsutsanabe ndi Yehova Mulungu ndi anthu Ake. (Numeri 22:1-35; 2 Petro 2:15, 16) Komabe, kupanda chikhulupiriro kwa Balamu sikunali kanthu pokuyerekezera ndi kwa Yudasi Isikariote. Ngakhale kuti anali bwenzi lapamtima la Yesu ndi mboni yoona ndi maso zozizwitsa zambiri, Yudasi anampereka Kristu ndi ndalama zasiliva makumi atatu.​— Mateyu 26:14-16, 47-50; 27:3-5.

Atsogoleri achipembedzo achiyuda anazidziŵanso zozizwitsa zambiri za Yesu. Ataukitsa Lazaro, iwo anavomereza kuti: “Munthu uyu achita zizindikiro zambiri.” Koma kodi kumuona Lazaro ali moyo kunafeŵetsa mitima yawo ndi kuwapatsa chikhulupiriro? Ayi ndithu. M’malo mwake, anapangana kuti aphe Yesu ndi Lazaro yemwe!​—Yohane 11:47-53; 12:10.

Ngakhale pamene Mulungu analoŵereramo mwachindunji anthu oipa amenewo sanakhulupirire. Nthaŵi ina pamene Yesu anali m’bwalo la kachisi, anapemphera mofuula kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.” Yehova anayankha ndi mawu ochokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.” Komabe, chochitika chozizwitsa chimenechi sichinabale chikhulupiriro m’mitima ya omwe analipowo. Baibulo limati: “Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pawo iwo sanakhulupirira Iye.”​—Yohane 12:28-30, 37; yerekezerani ndi Aefeso 3:17.

Chifukwa Chake Zozizwitsa Sizinabale Chikhulupiriro

Kodi nchifukwa ninji anthuwo sanakhulupirire ngakhale anaona zozizwitsa zambiri choncho? Nzodabwitsa kwambiri kuona kuti atsogoleri achipembedzo achiyuda anamkana Yesu makamaka mutalingalira kuti panthaŵi yeniyeni imene anayamba utumiki wake, Ayuda onse anali “kuyembekezera  . . . Kristu,” kapena Mesiya. (Luka 3:15) Komabe, vuto kwenikweni linali m’zimene iwo anayembekezera. Wolemba dikishonale W. E. Vine akugwira mawu katswiri wa Baibulo wodziŵika bwino kuti anati Ayuda anangotengeka ndi lingaliro la Mesiya yemwe “anali kudzatukula umoyo wawo wakuthupi” ndi “wachuma.” Chotero, sanakonzekere za Yesu wodzichepetsa, wosaloŵerera m’zandale wa ku Nazarete, yemwe anaonekera pakati pawo monga Mesiya weniweni mu 29 C.E. Atsogoleri achipembedzowo anaopanso kuti ziphunzitso za Yesu zikanadodometsa mkhalidwe wa zochitika za m’dzikomo ndi kuika pangozi malo awo apamwamba. (Yohane 11:48) Malingaliro awo olakwika ndi dyera linawaphimba kuti asaone tanthauzo la zozizwitsa za Yesu.

Pambuyo pake atsogoleri achipembedzo achiyuda ndi enanso anakana umboni wa zozizwitsa wakuti Mulungu anayanja atsatiri a Yesu. Mwachitsanzo, pamene atumwi ake anachiritsa munthu wopunduka chibadwire, ziŵalo zokwiya za bwalo lalikulu lamilandu lachiyuda zinafunsa kuti: “Tidzawachitira chiyani anthu awa? pakutitu chaoneka kwa onse akukhala m’Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana. Komatu tiwaopse asalankhulenso m’dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu.” (Machitidwe 3:1-8; 4:13-17) Mwachionekere, chozizwitsa chimenechi sichinabale kapena kuyambitsa chikhulupiriro m’mitima ya anthu amenewo.

Kukhumba malo apamwamba, kunyada, ndi dyera nzimene zapangitsa anthu kuumitsa mitima yawo. Kukuoneka kuti ndi mmene zinaliri kwa Kora, Datani, ndi Abiramu, otchulidwa poyamba paja. Nsanje, mantha, ndi maganizo ena akupwetekedwa mtima ndi zimene zalepheretsa ena. Akutikumbutsanso za angelo osamvera, ziŵanda, zimene poyamba zinali ndi ufulu wakuona nkhope ya Mulungu. (Mateyu 18:10) Sizimakayikira kuti Mulungu aliko. Ndithudi, “ziŵanda zikhulupiranso, ndipo zinthunthumira.” (Yakobo 2:19) Komabe, zilibe chikhulupiriro mwa Mulungu.

Tanthauzo la Chikhulupiriro Choona

Chikhulupiriro si kungokhulupirira chabe. Sichilinso kungotengeka maganizo kwa kanthaŵi mutaona chozizwitsa iyayi. Ahebri 11:1 amati: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” Munthu wachikhulupiriro amatsimikiza mumtima mwake kuti chilichonse chimene Yehova Mulungu amalonjeza chili ngati kuti chakwaniritsidwa kale. Ndiponso, umboni wosakanika wa zenizeni zosaoneka ngwamphamvu kwambiri kwakuti chikhulupiriro chenichenicho nchofanana ndi umboni umenewo. Inde, chikhulupiriro nchozikidwa pa umboni. Ndipo m’nthaŵi zapitazo, zozizwitsa zinagwiritsiridwa ntchito kukulitsa chikhulupiriro kapena kuchimangirira. Zizindikiro zimene Yesu anachita zinali zoti ena atsimikize kuti iye anali Mesiya wolonjezedwayo. (Mateyu 8:16, 17; Ahebri 2:2-4) Mofananamo, mphatso zotero za mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, zonga kuchiritsa mwa chozizwitsa ndi kulankhula m’malilime zinasonyeza kuti tsopano Yehova anawakana Ayuda koma kuti anayanja mpingo wachikristu, umene Mwana wake Yesu Kristu anakhazikitsa.​—1 Akorinto 12:7-11.

Imodzi ya mphatso zozizwitsa za mzimu inali mphatso yakunenera. Pamene osakhulupirira anaona chozizwitsa chimenechi, ena anasonkhezeredwa kulambira Yehova, nati: “Mulungu ali ndithu mwa inu.” (1 Akorinto 14:22-25) Komabe, Yehova Mulungu sanafune kuti zozizwitsa zikhale zinthu zachikhalire pakulambira kwachikristu. Nchifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka.” (1 Akorinto 13:8) Mwachionekere mphatso zimenezi zinalekeka pamene atumwi anamwalira ndi ajanso amene anazilandira kwa iwo.

Kodi ndiye kuti anthu akanangosiyidwa opanda maziko a chikhulupiriro? Ayi, pakuti Paulo anati: “[Mulungu] sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.” (Machitidwe 14:17) Ndithudi, kwa anthu oona mtima amene akufuna kukhulupirira ndi maganizo ndi mitima yawo umboni wotizingawu, “zaoneka bwino zosaoneka zake [za Yehova Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi Umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo [okana Mulungu] adzakhale opanda mawu akuŵiringula.”​—Aroma 1:20.

Kungokhulupirira kuti Mulungu aliko sikokwanira. Paulo analangiza kuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Mungachite zimenezi mwa kuphunzira Malemba mwakhama mothandizidwa ndi zofalitsa zachikristu, zonga magazini ano. Chikhulupiriro chozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu, Baibulo, sichili chofooka, kapena chachabechabe. Awo amene azindikira chifuniro cha Mulungu nkumachichita mwa chikhulupiriro akuchitira Mulungu utumiki wopatulika.​—Aroma 12:1.

Kukhulupirira Popanda Kuona

Mtumwi Tomasi kunamvuta kukhulupirira kuti Yesu waukitsidwa kwa akufa. “Ndikapanda kuona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yake; sindidzakhulupira,” anatero Tomasi. Kenaka pamene Yesu anavala thupi la mabala a kupachikidwa kwake, Tomasi anakhulupirira chozizwitsacho. Komabe, Yesu anati: “Odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.”​—Yohane 20:25-29.

Lero, Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri ‘zikuyenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.’ (2 Akorinto 5:7) Ngakhale kuti sizinaone zozizwitsa zolembedwa m’Baibulo, zimakhulupirira kuti zimenezi zinachitika. Mbonizo zimakhulupirira Mulungu ndi Mawu ake. Mwa chithandizo cha mzimu wake, zimamvetsetsa ziphunzitso za Baibulo ndi mutu wake waukulu​—kukweza uchifumu wa Yehova Mulungu mwa njira ya Ufumu wake wakumwamba. (Mateyu 6:9, 10; 2 Timoteo 3:16, 17) Akristu oona ameneŵa amagwiritsira ntchito uphungu wanzeru wa Baibulo m’moyo wawo napindula nawo kwambiri. (Salmo 119:105; Yesaya 48:17, 18) Amavomereza umboni wosatsutsika wakuti maulosi a Baibulo amasonyeza kuti nthaŵi yathuyi ndiyo “masiku otsiriza,” ndipo amakhulupirira kuti dziko latsopano limene Mulungu walonjeza lili pafupi. (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-14; 2 Petro 3:13) Kwa iwo nzowasangalatsa kugaŵana ndi ena chidziŵitso cha Mulungu. (Miyambo 2:1-5) Amadziŵa kuti njira yokha imene awo ofunafuna Mulungu angampezere ndiyo mwa kuphunzira Malemba.​—Machitidwe 17:26, 27.

Kodi mukumkumbukira Albert, yemwe watchulidwa m’nkhani yapitayo? Patapita masiku oŵerengeka kuchokera pamene pemphero lake lofunsira chozizwitsa linakhala losayankhidwa, mmodzi wa Mboni za Yehova anamchezera, mkazi wachikulire yemwe anamsiyira mabuku onena za Baibulo. Pambuyo pake Albert anavomereza phunziro la Baibulo laulere lapanyumba. Mmene anayamba kumvetsetsa uthenga wa Baibulo, chisoni chake chinasanduka chimwemwe. Anayamba kuzindikira kuti basi wampeza Mulungu.

Malemba amalangiza kuti: “Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi.” (Yesaya 55:6) Mungatero mwa kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ake, koma osati mwa kudikira chozizwitsa chamakono chochokera kwa Mulungu. Zimenezo nzofunika, chifukwa zozizwitsa zokha sizimabala chikhulupiriro.

[Chithunzi patsamba 5]

Ngakhale kuuka kozizwitsa kwa Lazaro sikunawapangitse adani a Yesu kukhala ndi chikhulupiriro

[Zithunzi patsamba 7]

Chikhulupiriro chimadalira pa chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena