Pamene Mavuto Sadzakhalakonso
MAVUTO sanali mbali ya chifuno choyamba cha Mulungu kwa banja la munthu. Sindiye anawaikapo, ndipo samawafuna ayi. ‘Ngati ndi mmene zilili,’ mungafunse motero, ‘kodi anayamba motani, ndipo nchifukwa ninji Mulungu wawalola mpaka lero?’—Yerekezerani ndi Yakobo 1:13.
Yankho lake likupezeka m’nkhani yoyambirira ya mbiri ya munthu—Baibulo, makamaka m’buku la Genesis. Limanena kuti makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anatsatira Satana Mdyerekezi pakupandukira kwake Mulungu. Zochita zawo zinabutsa nkhani zazikulu zimene zinasokoneza maziko ake a bata ndi mtendere wa chilengedwe chonse. Pamene anafuna ufulu wodzisankhira chabwino ndi choipa, anatsutsa uchifumu wa Mulungu. Anakayikira kuyenera kwake kulamulira ndi kukhala kwake yekhayo wakuwauza “zabwino ndi zoipa.”—Genesis 2:15-17; 3:1-5.
Bwanji Sanangoumiriza Chifuniro Chake Pomwepo?
‘Nanga bwanji Mulungu sanangoumiriza chifuniro chake pomwepo?’ mungafunse zimenezo. Ambiri aganiza kuti nkhaniyi njapafupi kwambiri. ‘Mulungu anali nazo mphamvu. Akanazigwiritsira ntchito kuwonongera apanduwo,’ iwo amatero. (Salmo 147:5) Koma tadzifunsani nokha kuti, ‘Kodi ine ndimafulumira kutama onse amene amagwiritsira ntchito mphamvu zawo zazikulu kuti aumirize chifuniro chawo? Kodi mwachibadwa sindimanyansidwa pamene wolamulira wotsendereza agwiritsira ntchito magulu opha anthu kuti awononge adani ake?’ Anthu ochuluka oganiza bwino amanyansidwa nazo zoterozo.
‘A-aa,’ mukutero, ‘koma ngati Mulungu anagwiritsira ntchito mphamvuzo, kulibe amene akanakayikira zochita zake.’ Mukunenetsa? Kodi si zoona kuti anthu amakayikiradi njira imene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake? Amakayikira chifukwa chake iye sanazigwiritsire ntchito nthaŵi zina, monga pakulola kwake kuipa. Ndipo amakayikira chifukwa chake wazigwiritsira ntchito nthaŵi zina. Ngakhale Abrahamu wokhulupirikayo anavutika maganizo ndi njira imene Mulungu anagwiritsira ntchito mphamvu zake pa adani Ake. Mukukumbukira pamene Mulungu anafuna kuwononga Sodomu. Abrahamu mosadziŵa anaopa kuti anthu abwino adzafera pamodzi ndi oipa. Anadandaula nati: “Musamatero ayi, kupha olungama pamodzi ndi oipa.” (Genesis 18:25) Ngakhale anthu oganiza bwino ngati Abrahamu amafuna chitsimikizo chakuti mphamvu zopanda malirezo sadzazigwiritsira ntchito molakwa.
Inde, Mulungu akanawononga Adamu, Hava, ndi Satana nthaŵi yomweyo. Koma taganizirani mmene zimenezo zikanakhudzira angelo kapena zolengedwa zamtsogolo, zimene mwina zikanadziŵa pambuyo pake zimene iye anachita. Kodi zimenezi sizikanawasiya ndi mafunso osautsa ponena za kulungama kwa ulamuliro wa Mulungu? Kodi sizikanangotsimikiza kuti Mulungu analidi wopondereza wankhalwe, malinga ndi kufotokoza kwa Nietzsche, Mulungu amene mwankhanza amawononga aliyense womtsutsa?
Bwanji Sanangowapangitsa Anthu Kuchita Chabwino?
‘Kodi Mulungu sakanangowapangitsa anthu kuchita chabwino?’ ena angafunse zimenezo. Eya, talingaliraninso izi. M’mbiri yonse, maboma ayesa kuchititsa anthu kutsatira kaganizidwe kawo. Maboma ena kapena olamulira ena agwiritsira ntchito njira zamitundumitundu zosinthira anthu maganizo, mwina mankhwala kapena opaleshoni, nalanda anthuwo mphatso yabwino kwambiri ya ufulu wakudzisankhira. Kodi sitimakonda kukhala anthu aufulu wodzisankhira, ngakhale kuti mphatso imeneyo nthaŵi zina timaigwiritsira ntchito molakwa? Kodi timalilola boma kapena wolamulira aliyense kutilanda mphatsoyo?
Nanga ndi njira ina iti imene inalipo yomwe Mulungu anasankha m’malo mogwiritsira ntchito mphamvu pomwepo kuti asungitse lamulo? Yehova Mulungu anaona kuti chipandukocho chingathetsedwe bwino mwa kulola nyengo yokhala ndi malire yakuti aja okana malamulo ake adzilamulire popanda ulamuliro wake. Zimenezi zinadzapatsa banja la munthu, lochokera kwa Adamu ndi Hava, nthaŵi yaifupi yodzilamulira okha popanda kumvera lamulo la Mulungu. Anachitiranji zimenezo? Chifukwa anadziŵa kuti, m’kupita kwa nthaŵi, padzakhala umboni wochuluka wosatsutsika, wotsimikiza kuti njira yake yolamulira njabwino ndi yolungama nthaŵi zonse, ngakhale pamene agwiritsira ntchito mphamvu zake zopanda malirezo kusungitsa chifuniro chake, ndi kuti kumpandukira kwamtundu uliwonse kumadzetsabe tsoka pambuyo pake.—Deuteronomo 32:4; Yobu 34:10-12; Yeremiya 10:23.
Nanga Bwanji za Oferamo Onse Opanda Chifukwa?
‘Nanga pali pano, bwanji za anthu onse opanda chifukwa?’ mungafunse zimenezo. ‘Kodi zili bwino iwo kuvutika kuti kugwira ntchito kwa lamulo kuoneke?’ Mulungu sanalole kuti kuipa kukhaleko kungoti asonyeze kugwira ntchito kwa mfundo ya lamulo yosamveka bwino. M’malo mwake anati akhazikitsiretu choonadi chofunika chakuti iye yekha ndiye mfumu ndi kuti zolengedwa zake zonse zimafunika kumvera malamulo ake kuti zikhale ndi mtendere ndi chimwemwe chachikhalire.
Chinthu chofunika kwambiri kukumbukira nchakuti Mulungu adziŵa kuti angathetseretu zopweteka zilizonse zomwe kuipa kungadzetse pabanja la munthu. Adziŵa kuti m’kupita kwa nthaŵi, nyengo yaifupi ya zopweteka ndi mavuto idzakhala ndi mapindu ake. Talingalirani za mayi amene amagwiritsa mwana wake pamene dokotala akumbaya jekeseni yoŵaŵa ya katemera kuti amteteze ku matenda akutiakuti amene angaphe mwanayo. Kulibe mayi amene amafuna kuti mwana wake amve kupweteka. Kulibe dokotala amene amafuna kusautsa wodwala. Panthaŵiyo, mwana satha kumvetsa chifukwa chake akumpweteka, koma pambuyo pake adzamvetsa chimene iwo analolera zimenezo.
Kodi Kumatonthozadi Ovutika?
Ena angaganize kuti kungodziŵa zinthu zimenezi kwenikweni sikungatonthoze aja ovutika. Hans Küng akunena kuti kufotokoza momveka chifukwa chake mavuto akhalako mwa iko kokha “sikumthandiza wovutikayo mpang’ono pomwe monga momwe nkhani ya zakudya simamthandizira munthu amene ali kufa ndi njala.” Akufunsa kuti: “Kodi zifukwa zomveka zingamlimbikitsedi munthu amene afuna kufa ndi mavuto?” Zoona, “zifukwa zomveka” zonse zimene anthu onyalanyaza Mawu a Mulungu, Baibulo, apereka sizinawalimbikitse aja ovutika. Zifukwa za anthu zoterozo zangowonjezera mavuto pa mavuto mwa kusonyeza kuti Mulungu anafuna kuti munthu azivutika ndi kuti analenga dziko lapansi likhale chigwa cha misozi kapena malo oyesera aja amene potsiriza pake adzakhala ndi moyo kumwamba. Mwano wake kukula!
Komabe, Baibulo lomwe limapatsa chitonthozo chenicheni. Silimangopereka chifukwa chomveka chimene mavuto akhalirako komanso limakulitsa chidaliro palonjezo lotsimikizika la Mulungu lakuti adzathetsa zovuta zonse zomwe kulola kwake mavuto kwadzetsa.
“Nthaŵi Zakukonzanso Zinthu Zonse”
Posachedwa Mulungu adzakonzanso zinthu zonse kuti zikhale monga momwe anafunira zisanapanduke zolengedwa zake zaumunthu. Nthaŵi yake yoikika ya ulamuliro wodziimira pawokha wa munthu ili pafupi kutha. Tikukhala panthaŵi imene adzatuma “Yesu; amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthaŵi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.”—Machitidwe 3:20, 21.
Kodi Yesu Kristu adzachita chiyani? Adzachotsa adani onse a Mulungu padziko lapansi. (2 Atesalonika 1:6-10) Chimenechi sichidzakhala chiweruzo chamsangamsanga, chonga chomwe amapereka olamulira aumunthu otsendereza. Umboni wochuluka wosonyeza zotsatira zake zatsoka za ulamuliro wosalongosoka wa munthu udzasonyeza kuti Mulungu ali wolungama pamene posachedwa agwiritsira ntchito mphamvu zake zopanda malirezo kusungitsa chifuniro chake. (Chivumbulutso 11:17, 18) Poyamba, zimenezi zidzakhala “masauko [“chisautso chachikulu,” NW]” onga sipadakhale otero padziko lapansi, onga Chigumula cha tsiku la Nowa koma choposapo. (Mateyu 24:21, 29-31, 36-39) Awo amene adzapulumuka “chisautso chachikulu” chimenechi adzakhala ndi “nyengo zakutsitsimutsa” pamene adzaona malonjezo a Mulungu akukwaniritsidwa operekedwa “m’kamwa mwa aneneri ake oyera.” (Machitidwe 3:19; Chivumbulutso 7:14-17) Kodi Mulungu walonjeza chiyani?
Eya, aneneri a Mulungu akale akunena kuti mavuto amene nkhondo ndi kukhetsa mwazi zimachititsa adzatha. Mwachitsanzo, Salmo 46:9 limatiuza kuti: “Aletsa nkhondo kumalekezero adziko lapansi.” Sikudzakhalanso oferamo popanda chifukwa ndi othaŵa kwawo omvetsa chisoni, ochitidwa mizambi, opunduka, ndi ophedwa m’nkhondo zankhanza! Mneneri Yesaya akuti: “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.
Aneneri akuloseranso kuti mavuto amene upandu ndi chisalungamo zimachititsa adzatha. Miyambo 2:21, 22 ikulonjeza kuti “oongoka mtima adzakhala m’dziko” ndi kuti amene amachititsa zopweteka ndi mavuto “adzazulidwamo.” ‘Wina sadzapwetekanso mnzake pomlamulira.’ (Mlaliki 8:9) Oipa onse adzachotsedwapo ku nthaŵi yonse. (Salmo 37:10, 38) Yense adzakhala pamtendere ndi chisungiko, osavutika ayi.—Mika 4:4.
Ndiponso, aneneri akulonjezanso kuti mavuto amene matenda ndi kupsinjika mtima zimachititsa adzatha. (Yesaya 33:24) Yesaya akulonjeza kuti akhungu, ogontha, opunduka, ndi onse odwala matenda osiyanasiyana adzachira. (Yesaya 35:5, 6) Mulungu adzachotsapo ngakhale zoŵaŵitsa za imfa. Yesu analosera kuti “onse ali m’manda adzamva mawu ake nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) M’masomphenya ake a “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano,” mtumwi Yohane anauzidwa kuti “Mulungu yekha . . . adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” (Chivumbulutso 21:1-4) Taganizirani zimenezo! Kulibe choŵaŵitsa, kulibe misozi, kulibe kulira, kulibe imfa—kulibenso mavuto!
Masoka alionse omwe angakhale atachitika pakulola kwakanthaŵi kuipa kumeneku adzatha. Ngakhale zopweteka ndi mavuto a munthu—zimene sizinali chifuno cha Mulungu—sizidzakumbukika konse ayi. ‘Zovuta zoyamba zidzaiŵalika . . . Zinthu zakale sizidzakumbukika.’ (Yesaya 65:16, 17) Chifuno choyamba cha Mulungu cha banja langwiro la munthu lokhala pamtendere wokwana ndi chimwemwe padziko lapansi la paradaiso chidzachitika chonse. (Yesaya 45:18) Anthu adzadalira uchifumu wake kotheratu. Udzakhala mwaŵi wotani nanga kukhala panthaŵi imene Mulungu adzathetsa mavuto onse a munthu, nthaŵi imene adzaonetsa kuti saali “wopondereza, wonyenga, waukathyali, wakupha,” monga mwa kuneneza kwa Nietzsche, koma kuti nthaŵi zonse ali wachikondi, wanzeru, ndi wolungama pakugwiritsira ntchito mphamvu zake zazikulukuluzo!
[Chithunzi patsamba 5]
Olamulira Ena Asintha Anthu Maganizo, Nawalanda Ufulu Wawo Wakudzisankhira
[Mawu a Chithunzi]
UPI/Bettmann
[Chithunzi patsamba 7]
Mavuto atatha, onse adzasangalala ndi moyo wokhutiritsa