Mutu 14
Kukalambirana
1, 2. (a) Kodi ndi masinthidwe otani amene amakhalapo pamene ukalamba ufika? (b) Kodi amuna aumulungu a m’nthaŵi za Baibulo anapeza motani chikhutiro mu ukalamba?
ZAMBIRI zimasintha pamene tikukalamba. Kufooka kwa thupi kumatilanda nyonga yathu. Tikayang’ana m’kalirole timaona makwinya atsopano ndi imvi zimene zikuyambika—ngakhale dazi. Tingayambe kuiŵala zinthu kaŵirikaŵiri. Pamakhala maunansi atsopano pamene ana akwatira kapena kukwatiŵa, ndiponso pamene adzukulu abadwa. Kwa ena, kupuma pantchito kumadzetsa mkhalidwe wosiyana wa moyo.
2 Kunena zoona, zaka zaukalamba zingakhaledi zovuta. (Mlaliki 12:1-8) Komabe, talingalirani za atumiki a Mulungu a m’nthaŵi za Baibulo. Ngakhale kuti pomalizira pake anamwalira, anapeza nzeru ndi luntha, zimene zinawapatsa chikhutiro chachikulu mu ukalamba wawo. (Genesis 25:8; 35:29; Yobu 12:12; 42:17) Kodi iwo anakhoza motani kufika paukalamba ali achimwemwe? Ndithudi, kunali mwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mapulinsipulo amene ife lerolino timawapeza m’Baibulo.—Salmo 119:105; 2 Timoteo 3:16, 17.
3. Kodi Paulo anapereka uphungu wotani kwa amuna ndi akazi okalamba?
3 M’kalata yake kwa Tito, mtumwi Paulo anapereka chitsogozo chabwino kwa aja amene akukalamba. Iye analemba kuti: “Okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro. Momwemonso akazi okalamba akhale nawo makhalidwe oyenera anthu oyera, osadyerekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma.” (Tito 2:2, 3) Kumvera mawu ameneŵa kungakuthandizeni kuyang’anizana ndi zovuta zaukalamba.
ZOLOŴERANI PAMENE ANA AKUKAKHALA PAOKHA
4, 5. Kodi makolo ambiri amamva motani pamene ana awo achoka panyumba, ndipo kodi ena amazoloŵera motani mkhalidwe watsopano?
4 Kusintha kwa mathayo kumafuna kuzoloŵera. Zimenezi nzoona chotani nanga pamene ana achikulire achoka panyumba ndi kukwatira kapena kukwatiwa! Kwa makolo ambiri chimenechi chimakhala chizindikiro choyamba chakuti akukalamba. Ngakhale kuti amakondwera poona kuti ana awo akula, kaŵirikaŵiri makolo amada nkhaŵa kuti kaya anachita zonse zimene akanakhoza kukonzekeretsa ana kukadzikhalira okha. Ndiponso angalakalake kukhala nawo pafupi.
5 Zoona, makolo amapitiriza kudera nkhaŵa za umoyo wa ana awo, ngakhale pambuyo pakuti ana achoka panyumba. Mayi wina anati: “Ndikanakonda kumalandira mauthenga kuchokera kwa iwo kaŵirikaŵiri, kuti ndidziŵe ngati ali bwino—zimenezo zikanandipatsa chimwemwe.” Tate wina akuti: “Pamene mwana wathu wamkazi anachoka panyumba, inali nthaŵi yovuta kwambiri. Panakhala kusoŵeka kwakukulu kwa munthu wina m’banja chifukwa chakuti nthaŵi zonse tinkachitira zinthu pamodzi.” Kodi makolo ameneŵa achita motani ndi kusakhalapo kwa ana awo? Nthaŵi zambiri, mwa kusamalira anthu ena ndi kuwathandiza.
6. Kodi nchiyani chimene chimathandiza kusunga maunansi a banja m’malo ake oyenera?
6 Pamene ana apita ku ukwati, mathayo a makolo amasintha. Genesis 2:24 imati: ‘Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.’ Kulemekeza mapulinsipulo aumulungu a umutu ndi dongosolo labwino kudzathandiza makolo kusunga zinthu m’malo ake oyenera.—1 Akorinto 11:3; 14:33, 40.
7. Kodi tate wina anakulitsa maganizo abwino otani pamene ana ake aakazi anachoka panyumba atakwatiwa?
7 Pamene ana aŵiri aakazi anakwatiwa ndi kuchoka panyumba, makolo awo anamva kutayikidwa m’moyo wawo. Poyamba, tateyo sanali kukondwera nawo akamwini akewo. Koma pamene analingalira pulinsipulo la umutu, anazindikira kuti tsopano amuna a ana ake aakaziwo anali ndi thayo la kusamalira mabanja awo. Motero, pamene ana ake aakaziwo anapempha uphungu kwa iye, anawafunsa zimene amuna awo anaganiza, ndiyeno anawachirikiza kwambiri. Akamwini akewo tsopano amamuona monga bwenzi ndipo amalandira mauphungu ake.
8, 9. Kodi makolo ena achita motani kuti azoloŵere pamene ana awo akula ndi kukadzikhalira okha?
8 Bwanji ngati okwatirana chatsopano alephera kuchita chimene makolo awo akulingalira kuti ndicho chabwino koposa, ngakhale kuti sichili chotsutsana ndi Malemba? Okwatirana ena amene ali ndi ana okwatira anati: “Nthaŵi zonse timawathandiza kuona lingaliro la Yehova, koma ngati sitigwirizana ndi chosankha chawo, timavomereza ndipo timawachirikiza ndi kuwalimbikitsa.”
9 M’maiko ena ku Asia, amayi ena zimawakhalira zovuta kwambiri kuzoloŵera pamene ana awo aamuna akukadzikhalira okha. Komabe, ngati alemekeza dongosolo lachikristu ndi umutu, amaona kuti mikangano ndi azipongozi awo imachepa. Mkazi wina wachikristu amaona kuti kuchoka panyumba kwa ana ake aamuna kwakhala “koyamikirika kwambiri nthaŵi zonse.” Iye ali wokondwa kuona kukhoza kwawo kusamalira mabanja awo atsopano. Ndiponso, zimenezi zapeputsanso mtolo wa zakuthupi ndi wa m’maganizo umene iye ndi mwamuna wake ayenera kusenza pamene akukalamba.
KULIMBITSA UKWATI WANU
Pamene mukukalamba, limbitsaninso chikondi chanu kwa wina ndi mnzake
10, 11. Kodi ndi uphungu wotani wa m’Malemba umene ungathandize anthu kupeŵa misampha ina ya msinkhu wapakati?
10 Anthu amachita mosiyanasiyana pamene afika usinkhu wapakati. Amuna ena amavala mosiyana kuti ayese kuoneka achinyamata. Akazi ambiri amada nkhaŵa ndi masinthidwe amene amafika ndi nyengo yoleka kusamba. Mwachisoni, anthu ena amsinkhu wapakati amakwiyitsa anzawo a muukwati ndi kuwachititsa nsanje mwa kuseŵera ndi anyamata kapena atsikana. Komabe, amuna aumulungu okalamba ali “anzeru,” amapeŵa zikhumbo zosayenera. (1 Petro 4:7) Akazinso achikulire amayesa kusunga maukwati awo kaamba kokonda amuna awo ndi kufuna kukondweretsa Yehova.
11 Mwa kuuziridwa, Mfumu Lamueli analemba chitamando cha “mkazi wangwiro” amene achitira mwamuna wake ‘zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.’ Mwamuna wachikristu sadzalephera kuyamikira mmene mkazi wake akuyesayesera kulimbana ndi zovutitsa mtima zilizonse zimene angakumane nazo m’zaka za msinkhu wapakati. Chikondi chake chidzamsonkhezera ‘kumtama.’—Miyambo 31:10, 12, 28.
12. Kodi okwatirana angakalambirane motani mwachikondi?
12 M’kati mwa zaka zakubala ana zotangwanitsa kwambiri, nonse aŵiri mungakhale mutaika pambali zofuna zaumwini kuti musamalire zofunika za ana anu. Pamene iwo achoka, ndi nthaŵi yakuti musumikenso maganizo onse pa moyo wanu wa ukwati. “Pamene ana anga aakazi anachoka panyumba,” akutero mwamuna wina, “tinayambanso kutomerana ndi mkazi wanga.” Mwamuna wina akuti: “Aliyense amasamalira thanzi la mnzake ndipo timakumbutsana kuchita maseŵero olimbitsa thupi.” Kuti asasungulumwe, iye ndi mkazi wake amachereza ena mumpingo. Inde, kusamalira ena kumadzetsa madalitso. Ndiponso, kumakondweretsa Yehova.—Afilipi 2:4; Ahebri 13:2, 16.
13. Kodi kukhala womasuka ndi woona mtima kumathandiza mbali yanji pamene a muukwati akukalamba pamodzi?
13 Musalole kuti kulankhulana kuduke pakati pa inu ndi mnzanu wa muukwati. Kambitsiranani moona mtima. (Miyambo 17:27) Mwamuna wina anati: “Timakulitsa kumvana mwa kusamalirana ndi kulingalirana.” Mkazi wake akuvomerezana naye, akumati: “Pamene takalambirana, timasangalala kumwera pamodzi tiyi, kucheza, ndi kuthandizana.” Kukhala kwanu womasuka ndi woona mtima kungathandize kulimbitsa ukwati wanu, kuupatsa nyonga imene idzalepheretsa ziukiro za Satana, wowononga maukwati.
SANGALALANI NDI ADZUKULU ANU
14. Mwachionekere, kodi ndi mbali yanji imene agogo ake aakazi a Timoteo anathandiza pakukula kwake monga Mkristu?
14 Adzukulu ali “korona” wa okalamba. (Miyambo 17:6) Ubwenzi wa adzukulu ungakhale wosangalatsadi—waumoyo ndi wotsitsimula. Baibulo limatamanda Loisi, amene anali agogo, amene pamodzi ndi mwana wake wamkazi Yunike, anaphunzitsa chikhulupiriro chawo mdzukulu wake wakhanda Timoteo. Wachichepereyu anakula akumadziŵa kuti amake ndi agogo ake analemekeza choonadi cha Baibulo.—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.
15. Ponena za adzukulu, kodi ndi chithandizo chofunika chotani chimene agogo angapereke, koma kodi ayenera kupeŵanji?
15 Iyi ndiyo mbali yofunika imene agogo angathandize kwambiri. Agogo inu, munaphunzitsa kale ana anu chidziŵitso chanu cha zifuno za Yehova. Tsopano mukhoza kuchita chimodzimodzi kwa mbadwo winawo! Ana aang’ono ambiri amakondwera kumvetsera pamene agogo awo akusimba nkhani za m’Baibulo. Simukulanda thayo la atate ayi, la kuphunzitsa choonadi cha Baibulo kwa ana awo. (Deuteronomo 6:7) M’malo mwake, mumathandizira. Pemphero lanu likhale lija la wamasalmo lakuti: “Pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.”—Salmo 71:18; 78:5, 6.
16. Kodi agogo angapeŵe motani kuchititsa kusamvana m’banja mwawo?
16 Mwachisoni, agogo ena amapusika kwambiri adzukulu kwakuti pamakhala kusamvana pakati pa agogo ndi ana awo. Komabe, kukoma mtima kwanu kungachititse adzukulu anu kusapeza vuto kuulula kwa inu nkhani zimene alephera kuulula kwa makolo awo. Nthaŵi zina achichepere amafuna kuti agogo awo amene amamvana nawo akhale kumbali kwawo motsutsana ndi makolo awo. Bwanji pamenepo? Gwiritsirani ntchito nzeru ndi kulimbikitsa adzukulu anu kukhala omasuka kwa makolo awo. Mungafotokoze kuti zimenezi zimakondweretsa Yehova. (Aefeso 6:1-3) Ngati kuli kofunika, mungatsegulire njira achicheperewo mwa kuyamba ndinu kulankhula ndi makolo awo. Khalani woona mtima kwa adzukulu anu pa zimene mwaphunzira kwa zaka zambiri. Kuona mtima kwanu kungawapindulitse.
SINTHANI PAMENE MUKUKALAMBA
17. Kodi Akristu okalamba ayenera kutsanzira kutsimikiza mtima kotani kwa wamasalmo?
17 Pamene zaka zikupita, mudzaona kuti simuthanso kuchita zonse zimene munali kukhoza kapena zimene mungafune kuchita. Kodi munthu ayenera kuchita motani ndi ukalamba? M’maganizo mwanu mungaone monga muli ndi zaka 30 chabe, koma kuyang’ana m’kalirole kumaonetsa zosiyana ndi zimenezo. Musalefulidwe. Wamasalmo anachonderera Yehova kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” Tsanzirani kutsimikiza mtima kwa wamasalmo kwakuti: “Ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzawonjeza kukulemekezani.”—Salmo 71:9, 14.
18. Kodi Mkristu wokalamba angagwiritsire ntchito bwino motani nthaŵi yake atapuma pantchito?
18 Ambiri akonzekera pasadakhale kuwonjezera chitamando chawo kwa Yehova atapuma pantchito. “Ndinakonzekera pasadakhale zimene ndidzachita pamene mwana wanga wamkazi amaliza sukulu,” anafotokoza motero tate wina amene tsopano anapuma pantchito. “Ndinatsimikiza mtima kuti ndidzayamba utumiki wolalikira wa nthaŵi zonse, ndipo ndinagulitsa bizinesi yanga kuti ndimasuke ndi kutumikira Yehova mokwanira. Ndinapempherera chitsogozo cha Mulungu.” Ngati mukuyandikira zaka zakupuma pantchito, pezani chitonthozo pa chilengezo cha Mlengi wathu Wamkulu chakuti: “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, ine ndidzakusenzani inu.”—Yesaya 46:4.
19. Kodi ndi uphungu wotani umene waperekedwa kwa awo amene akukalamba?
19 Kupuma pantchito kungakhale kovuta kukuzoloŵera. Mtumwi Paulo analangiza amuna okalamba kukhala “odzisunga.” Zimenezi zimafuna kudziletsa pa zinthu, osagonja pachikhumbo cha kufuna moyo wofeŵa. Pangakhale kufunika kokulirapo kwa kukhala ndi dongosolo ndi kudziyang’anira pamene mwapuma pantchito kuposa ndi kale lonse. Motero, khalani wokangalika, mwa “kuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Wonjezerani zochita zanu ndi kumathandiza ena. (2 Akorinto 6:13) Akristu ambiri amachita zimenezi mwa kulalikira mokangalika uthenga wabwino malinga ndi nyonga yawo. Pamene mukukalamba, khalani “olama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro.”—Tito 2:2.
MMENE MUNGACHITIRE PAMENE MWATAYA MNZANU WA MUUKWATI
20, 21. (a) M’dongosolo lino la zinthu, kodi nchiyani chimene potsirizira pake chimalekanitsa okwatirana? (b) Kodi Anna akupereka chitsanzo chabwino chotani kwa ofedwa anzawo a muukwati?
20 Nzomvetsa chisoni komanso zoona kuti m’dongosolo lino la zinthu, anthu okwatirana potsirizira pake amalekanitsidwa ndi imfa. Akristu ofedwa mnzawo wa muukwati amadziŵa kuti okondedwa awowo akugona tsopano, ndipo ali ndi chidaliro chakuti adzawaonanso. (Yohane 11:11, 25) Koma kutayikako kumamvetsabe chisoni. Kodi wotsalayo angachite motani?a
21 Kukumbukira zimene munthu wina wotchulidwa m’Baibulo anachita kungakhale kothandiza. Anna anafedwa mwamuna wake patangopita zaka zisanu ndi ziŵiri za ukwati wawo, ndipo pamene tiŵerenga za iye, anali ndi zaka 84 zakubadwa. Ndithudi, iye anagwidwa ndi chisoni pamene anataya mwamuna wake. Kodi anapirira motani? Anapereka utumiki wopatulika kwa Yehova Mulungu pakachisi usana ndi usiku. (Luka 2:36-38) Moyo wa Anna wa utumiki wa mapemphero mosakayikira unali mankhwala amphamvu pa chisoni chake ndi kusungulumwa kwake monga mkazi wamasiye.
22. Kodi akazi amasiye ena ndi amuna ofedwa akazi awo achita motani ndi kusungulumwa?
22 “Vuto lalikulu koposa kwa ine lakhala kusoŵa mnzanga wolankhula naye,” akutero mkazi wina wokalamba wazaka 72 amene anafedwa mwamuna wake zaka khumi zapitazo. “Mwamuna wanga anali mmvetseri wabwino. Tinkakambitsirana za mpingo ndi ntchito yathu ya utumiki wachikristu.” Mkazi wina wamasiye akuti: “Ngakhale kuti nthaŵi imachiritsa, ndaona kukhala kolondola kwambiri kunena kuti zimene munthu amachita nayo nthaŵi ndizo zimathandiza kuchira. Umakhala wokhoza kuthandiza ena.” Mwamuna wina wazaka 67 wofedwa mkazi wake akuvomereza zimenezo, akumati: “Njira yabwino koposa yochitira ndi kufedwa ndiyo kudzipereka pa kutonthoza ena.”
KUŴERENGEREDWA NDI MULUNGU PAUKALAMBA
23, 24. Kodi Baibulo limapereka chitonthozo chachikulu chotani kwa okalamba, makamaka aja ofedwa anzawo a muukwati?
23 Ngakhale kuti imfa imatenga bwenzi la muukwati, Yehova amakhalabe wokhulupirika, wonena zoona nthaŵi zonse. “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,” inaimba motero Mfumu yakaleyo Davide, “ndidzachilondola ichi: Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’kachisi wake.”—Salmo 27:4.
24 “Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu,” akulangiza motero mtumwi Paulo. (1 Timoteo 5:3) Uphungu umene ukutsatira chilangizo chimenechi umasonyeza kuti akazi amasiye oyenerera opanda achibale apafupi angapatsidwe chichirikizo cha zinthu zakuthupi ndi mpingo. Komabe, lingaliro la chilangizo chakuti “chitira ulemu” limaphatikizapo kuwaŵerengera. Nchitonthozo chotani nanga chimene akazi amasiye aumulungu ndi amuna ofedwa akazi awo angachipeze mwa kudziŵa kuti Yehova amawaŵerengera ndi kuti adzawachirikiza!—Yakobo 1:27.
25. Kodi ndi chonulirapo chotani chimene chidakalipo kwa okalamba?
25 “Kukongola kwa nkhalamba ndi imvi,” amatero Mawu ouziridwa a Mulungu. “Ndiyo korona wa ulemu, [pamene, NW] idzapezedwa m’njira ya chilungamo.” (Miyambo 16:31; 20:29) Chotero, pitirizani kuika utumiki wa Yehova patsogolo m’moyo wanu, kaya muli muukwati, kapena mwatsalanso nokha. Mukatero, mudzakhala ndi dzina labwino ndi Mulungu tsopano ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko lopanda zopweteka za ukalamba.—Salmo 37:3-5; Yesaya 65:20.
a Kuti mumve zochuluka pankhaniyi, onani brosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.