Kodi Chimwemwe Chenicheni Chingapezeke Kuti?
ANTHU ambiri amaganiza kuti chimwemwe chingapezeke mwa kukhala ndi chuma. Nanga inuyo? Pamene kuli kwakuti nzoona kuti chuma chingatipatsenso chimwemwe, sichimapereka chimwemwe chotsimikizika; kapenanso chuma chakuthupi sichimakulitsa chikhulupiriro kapena kukhutiritsa zosoŵa zauzimu.
Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu Kristu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo.” (Mateyu 5:3, NW) Yesu anatinso: “Mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.”—Luka 12:15.
Ambiri amafunafuna chimwemwe mwa kuchita chisembwere ndi “ntchito za thupi” zina. (Agalatiya 5:19-21) Komabe, kutsata zilakolako zathupi sikumadzetsa chimwemwe chenicheni chokhalitsa. Ndiponso, ochita zimenezi sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9, 10.
Pofunafuna chimwemwe ena amayesa kusumika maganizo pa umunthu wawo mwa kuyesa kudzikulitsira ulemu wa iwo okha. Malaibulale ndi masitolo a mabuku ngodzaza ndi mabuku odziphunzitsa munthu yekha, koma zofalitsa zimenezi sizinapatse anthu chimwemwe chokhalitsa. Choncho, kodi nkuti kumene tingapeze chimwemwe chenicheni?
Kuti tikhaledi achimwemwe, tiyenera kudziŵa kusoŵa kwathu kwauzimu kwachibadwa. Yesu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” Komanso, sitingapeze phindu lililonse ngati tadziŵa kusoŵa kumeneku kenako nkulephera kuchitapo kanthu. Tinene mwafanizo: Nchiyani chingachitikire wampikisano wothamanga yemwe walephera kukhutiritsa chikhumbo cha madzi cha thupi lake pambuyo pa mpikisanowo? Kodi mwamsanga sangathedwe madzi m’thupi ndi kudwala matenda ena aakulu? Momwemonso, ngati tilephera kukhutiritsa njala yathu ya chakudya chabwino chauzimu, tidzafota mwauzimu m’kupita kwa nthaŵi. Zimenezi zidzatitayitsa chisangalalo ndi chimwemwe.
Yesu anadziŵa bwino lomwe kusoŵa kwake kwauzimu, naphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse ndi kuwasinkhasinkha. Anali kupeza ndi kuŵerenga zigawo za m’Malemba Oyera mosavutika, ndipo anaphunzitsanso ena kuchita chimodzimodzi. (Luka 4:16-21; yerekezerani ndi Aefeso 4:20, 21.) Yesu anafanizanso kuchita chifuniro cha Atate wake wakumwamba ndi chakudya. Kuchita chifuniro cha Mulungu kunamdzetsera chimwemwe chachikulu.—Yohane 4:34.
Inde, chimwemwe chenicheni sichingapezeke mwa kukhala ndi chuma chakuthupi; kapenanso chimwemwe sichimadza mwa kuyesa kukhutiritsa zilakolako za thupi lochimwali. Chimwemwe chenicheni ndicho mkhalidwe wa mtima, wozikidwa pa chikhulupiriro chenicheni ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu. Nchifukwa chake wamasalmo Davide anaimba moyenerera kuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15b.
[Chithunzi patsamba 23]
Chikhulupiriro ndi unansi wabwino ndi Mulungu zidzakupatsani chimwemwe chenicheni