Madalitso Kapena Matemberero—Zitsanzo kwa Ife Lerolino
“Izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.”—1 AKORINTO 10:11.
1. Kodi ndi kupenda kotani kumene tiyenera kupanga, monga momwedi munthu amapendera chiŵiya?
DZIMBIRI lingayambe kudya mosaonekera chipangizo chopangidwa ndi chitsulo pansi pa utoto wopakidwapo. Dzimbirilo lingaonekere patapita nthaŵi. Mofananamo, mikhalidwe ndi zikhumbo za mtima wa munthu zingakhale zitayamba kale kuipa zisanabale zipatso zoŵaŵa kapena ngakhale kudziŵidwa ndi ena. Monga momwe tingapendere mwanzeru chipangizo kuti tione ngati chikuchita dzimbiri, moteronso kupenda mitima yathu mosamala ndi kuikonza panthaŵi yake kungasungitse umphumphu wathu wachikristu. M’mawu ena, tingathe kulandira madalitso a Mulungu ndipo tingathe kupeŵa matemberero ochokera kwa Mulungu. Ena angaganize kuti madalitso ndi matemberero otchulidwa kwa Israyeli wakale alibe tanthauzo lenileni kwa awo amene akuyang’anizana ndi dongosolo ili la zinthu. (Yoswa 8:34, 35; Mateyu 13:49, 50; 24:3) Komabe, zimenezi sizili choncho. Tingathe kupindula mokulira ndi zitsanzo zachenjezo zoloŵetsamo Israyeli, monga momwe 1 Akorinto chaputala 10 akunenera.
2. Kodi nchiyani chimene 1 Akorinto 10:5, 6 amanena ponena za zokumana nazo za Israyeli m’chipululu?
2 Mtumwi Paulo amayerekezera Aisrayeli okhala pansi pa Mose ndi Akristu okhala pansi pa Kristu. (1 Akorinto 10:1-4) Ngakhale kuti anthu a Israyeli mwina akadaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, “ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nawo; pakuti anamwazika m’chipululu.” Chotero Paulo anauza Akristu anzake kuti: “Koma zinthu izi zinachitika, zikhale [zitsanzo kwa ife, NW], kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.” (1 Akorinto 10:5, 6) Zilakolako zimaleredwa mumtima, chotero tifunikira kumvera zitsanzo zimene Paulo akutchula.
Chenjezo pa Kupembedza Mafano
3. Kodi ndi motani mmene Aisrayeli anachimwira mogwiritsira ntchito mwana wa ng’ombe wa golide?
3 Chenjezo loyamba la Paulo nlakuti: ‘Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kuseŵera.’ (1 Akorinto 10:7) Chitsanzo chimenechi cha chenjezo nchija cha Aisrayeli obwerera ku njira za ku Igupto ndi kupanga fano la mwana wa ng’ombe. (Eksodo, chaputala 32) Wophunzira Stefano anasonyeza vuto lake lalikulu pamene anati: “Amene [Mose, wotumidwa ndi Mulungu] makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera mmbuyo mumtima mwawo ku Aigupto, nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa m’Aigupto, sitidziŵa chomwe chamgwera. Ndipo anapanga mwana wa ng’ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja awo.” (Machitidwe 7:39-41) Onani kuti Aisrayeli opulupudzawo anasunga “mumtima mwawo” zikhumbo zoipa zimene zinawachititsa kupembedza mafano. “Anapanga mwana wa ng’ombe . . . nabwera nayo nsembe kwa fanolo.” Ndiponso, ‘anasekera ndi ntchito za manja awo.’ Panali nyimbo za mingole, kuimba, kuvina, kudya, ndi kumwa. Mwachionekere, kupembedza fanoko kunali kokola munthu ndi kosangalatsa.
4, 5. Kodi tiyenera kupeŵa machitidwe opembedza mafano otani?
4 Igupto wophiphiritsira—dziko la Satana—kwakukulukulu amalambira zosangulutsa. (1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 11:8) Amalambira anthu a m’seŵero, oimba, ndi akatswiri a zamaseŵero, ndiponso kuvina kwawo, nyimbo zawo, ndi malingaliro awo a kusanguluka ndi nthaŵi zosangalatsa. Ambiri ayesedwa kudziloŵetsa m’kusanguluka pamene akupitiriza kunena kuti amalambira Yehova. Pamene Mkristu adzudzulidwa chifukwa cha cholakwa china, kaŵirikaŵiri mkhalidwe wauzimu wake wofooka umadziŵidwa kuchokera m’kumwa zakumwa zaukali, kuvina, ndi kusangalala mwa njira ina kumene kuli konga kupembedza mafano. (Eksodo 32:5, 6, 17, 18) Kusangulutsa kwina nkwabwino ndi kosangalatsa. Komabe, nyimbo za dziko zalerolino zochuluka, kuvina, mafilimu, ndi mavidiyo zimaperekedwa kuti ziipitse zikhumbo zathupi.
5 Akristu oona samagonjera pa kupembedza mafano. (2 Akorinto 6:16; 1 Yohane 5:21) Aliyense wa ife asamaletu kuti asakhale womwerekera pa zosangulutsa zamafano ndi kukhala pangozi ya kumwerekera pa kusangalala m’njira za dziko. Ngati tigonjera ku zisonkhezero zadziko, zikhumbo zovulaza ndi mikhalidwe zingakhazikike mosazindikirika m’maganizo ndi mumtima. Ngati zimenezi siziwongoleredwa, potsirizira pake zingatichititse ‘kumwazika m’chipululu’ cha dongosolo la Satana.
6. Kodi ndi mchitidwe wotsimikizirika wotani umene tingafunikire kutsatira ponena za kusanguluka?
6 Mofanana ndi Mose panthaŵi ya chochitika cha mwana wa ng’ombe wagolidi, kwenikweni “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akunena kuti: “Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine.” Kuchitapo kanthu motsimikizira kusonyeza kuti taima mochirimika kaamba ka kulambira koona kungakhale kopulumutsa moyo. Fuko la Mose la Levi linachitapo kanthu mofulumira kuchotsa zisonkhezero zoipa. (Mateyu 24:45-47; Eksodo 32:26-28) Chotero, pamenepa, pendani mosamala kusankha kwanu zosangulutsa, nyimbo, mavidiyo, ndi zina zotero. Ngati zili zoipitsa makhalidwe m’njira ina, imani kumbali ya Yehova. Ndi kudalira pa Mulungu mwapemphero, sinthani kusankha kwanu kwa zosangulutsa ndi nyimbo, ndipo wonongani zinthu zovulaza mwauzimu, monga momwe Mose anawonongera mwana wa ng’ombe.—Eksodo 32:20; Deuteronomo 9:21.
7. Kodi tingatetezere motani mtima wophiphiritsira?
7 Kodi tingaletse motani dzimbiri la mumtima? Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi kulola choonadi chake kuloŵa m’maganizo mwathu ndi mumtima. (Aroma 12:1, 2) Zoonadi, tiyenera kufika pa misonkhano yachikristu mokhazikika. (Ahebri 10:24, 25) Kufika pa misonkhano mwamphwayi kungayerekezeredwe ndi kupaka utoto pamalo adzimbiri. Zimenezi zingatichititse kukhala okondwa kwakanthaŵi, koma sizimathetsa vuto lake lalikulu. M’malo mwake, mwa kukonzekera pasadakhale, kusinkhasinkha, ndi kukhala ndi phande mokangalika m’misonkhano, tingathe kuchotsa mwamphamvu dzimbiri limene lingakhalepo mkatikati mwa mtima wathu wophiphiritsira. Zimenezi zidzatithandiza kumamatira Mawu a Mulungu ndipo zidzatilimbitsa kuti tipirire mayeso a chikhulupiriro ndi kukhala “angwiro ndi opanda chirema.”—Yakobo 1:3, 4; Miyambo 15:28.
Chenjezo pa Dama
8-10. (a) Kodi ndi chitsanzo cha chenjezo chotani chimene chikutchulidwa pa 1 Akorinto 10:8? (b) Kodi mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 5:27, 28 angagwiritsiridwe ntchito bwanji mopindulitsa?
8 M’chitsanzo chotsatira cha Paulo, timalangizidwa kuti: “Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.”a (1 Akorinto 10:8) Mtumwi Paulo anali kunena za nthaŵiyo pamene Aisrayeli anagwadira milungu yonyenga ndipo ‘anachita chigololo ndi ana aakazi a Moabu.’ (Numeri 25:1-9) Chigololo nchakupha! Kulola malingaliro ndi zikhumbo zachigololo zili zosalamuliridwa nkofanana ndi ‘kuchita dzimbiri’ kwa mtima. Yesu anati: “Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.”—Mateyu 5:27, 28.
9 Chosonyeza umboni wa zotulukapo za “kuyang’ana mkazi kumkhumba” ndicho kaganizidwe koluluzika ka angelo osamvera Chigumula cha m’tsiku la Nowa chisanafike. (Genesis 6:1, 2) Kumbukiraninso kuti, chimodzi cha zochitika zomvetsa chisoni koposa cha moyo wa Mfumu Davide chinayambitsidwa ndi kupitiriza kuyang’anitsitsa mkazi mosayenera. (2 Samueli 11:1-4) Mosiyana ndi zimenezo, munthu wolungama wokwatirayo Yobu ‘anapangana ndi maso ake, potero sanapenyetsetse namwali,’ motero akumapeŵa chigololo ndi kukhala wosunga umphumphu. (Yobu 31:1-3, 6-11) Maso angafanizidwe ndi mazenera a mtima. Ndipo zinthu zambiri zoipa zimatuluka mumtima woipa.—Marko 7:20-23.
10 Ngati titsatira mawu a Yesu, sitidzalekerera malingaliro olakwa mwa kuona zithunzi zaumaliseche kapena kusunga malingaliro achisembwere kulinga kwa Mkristu mnzathu, wantchito mnzathu, kapena wina aliyense. Dzimbiri silimachoka pa chitsulo mwa kungolipukuta. Chotero, musangokankhira pambali malingaliro ndi zikhoterero zachisembwere monga ngati kuti zili zosanukha kanthu. Tengani njira zamphamvu za kuchotsa zikhoterero zachisembwere mwa inu. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:29, 30.) Paulo akulimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.” Inde, “ukudza mkwiyo wa Mulungu” pa zinthu zonga chigololo, monga chisonyezero cha temberero lake. Chotero tifunikira ‘kufetsa’ ziŵalo za thupi lathu pa zinthu zimenezi.—Akolose 3:5, 6.
Chenjezo pa Kudandaula Kopandukira
11, 12. (a) Kodi ndi chenjezo lotani limene likuperekedwa pa 1 Akorinto 10:9, ndipo anali kusonyeza za chochitika chiti? (b) Kodi chenjezo la Paulo liyenera kutiyambukira motani?
11 Kenako Paulo akuchenjeza kuti: “Kapena tisayese [Yehova, NW], monga ena a iwo anayesa, nawonongeka ndi njoka zija.” (1 Akorinto 10:9) Pamene anali paulendo m’chipululu pafupi ndi malire a Edomu, Aisrayeli “ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Aigupto kuti tifere m’chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nawo mkate wachabe uwu,” mana amene anapatsidwa mozizwitsa. (Numeri 21:4, 5) Tangoganizani! Aisrayeliwo ‘anatsutsana ndi Mulungu,’ akumatcha zopereka za Mulungu kukhala zachabe!
12 Mwa kudandaula kwawo, Aisrayeli anali kuyesa kuleza mtima kwa Yehova. Sanalekerere pakuwalanga, pakuti Yehova anatumiza njoka zaululu pakati pawo, ndipo ambiri anafa njokazo zitawaluma. Anthu atalapa ndipo Mose atawatetezera, mliriwo unaleka. (Numeri 21:6-9) Ndithudi chochitika chimenechi chiyenera kukhala chenjezo kwa ife kuti tisasonyeze mzimu wopanduka, wa kudandaula, makamaka motsutsana ndi Mulungu ndi makonzedwe ake ateokrase.
Chenjezo pa Kung’ung’udza
13. Kodi 1 Akorinto 10:10 amachenjeza za chiyani, ndipo Paulo anali kulingalira za chipanduko chiti?
13 Potchula za chitsanzo chake chotsiriza chophatikizapo Aisrayeli m’chipululu, Paulo akulemba kuti: “Kapena [musang’ung’udze, NW], monga ena a iwo [anang’ung’udza, NW], nawonongeka ndi woonongayo.” (1 Akorinto 10:10) Chipanduko chinabuka pamene Kora, Datani, Abiramu, ndi ogwirizana nawo awo anachita zinthu motsutsana ndi teokrase ndi kunyoza ulamuliro wa Mose ndi Aroni. (Numeri 16:1-3) Opandukawo atawonongedwa, Aisrayeli anayamba kung’ung’udza. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti anayamba kulingalira kuti kuwonongedwa kwa opandukawo kunali kosalungama. Numeri 16:41 amati: “Mmaŵa mwake khamu lonse la ana a Israyeli [linang’ung’udza, NW] pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.” Chifukwa cha kupezera kwawo chifukwa ndi mmene chiweruzo chinaperekedwera pa chochitikacho, Aisrayeli 14,700 anafa ndi mliri wotumizidwa ndi Mulungu.—Numeri 16:49.
14, 15. (a) Kodi “anthu osapembedza” amene anakwaŵira mumpingo anachita tchimo lina lotani? (b) Kodi tingaphunzirenji m’chochitika cha Kora?
14 M’zaka za zana loyamba C.E., “anthu osapembedza” amene anakwaŵira mumpingo wachikristu anakhaladi aphunzitsi onyenga ndiponso ong’ung’udza. Anthu ameneŵa “[a]napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero,” amuna odzozedwa amene panthaŵiyo anaikiziridwa uyang’aniro wauzimu pampingo. Ponena za ampatuko osapembedzawo, wophunzira Yuda ananenanso kuti: “Amenewo ndiwo [ong’ung’udza, odandaula, NW], akuyenda monga mwa zilakolako zawo.” (Yuda 3, 4, 8, 16) Lerolino, anthu ena amakhala ong’ung’udza chifukwa chakuti amalola mkhalidwe wa dzimbiri lauzimu kukula mumtima mwawo. Iwo kaŵirikaŵiri amasumika maganizo pa kupanda ungwiro kwa awo okhala m’malo a uyang’aniro mumpingo ndi kuyamba kung’ung’udza motsutsana nawo. Kung’ung’udza ndi kudandaula kwawo kungakuledi kufikira pa kusuliza zofalitsa za “kapolo wokhulupirika.”
15 Kufunsa mafunso oona mtima onena za nkhani ya m’Malemba kuli koyenera. Komano bwanji ngati tiyamba kukulitsa mkhalidwe wotsutsa umene umaoneka m’makambitsirano osuliza ochitika pakati pa mabwenzi athu apafupi? Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zidzafika pati? Kodi sikuli bwino kwambiri kuleka kung’ung’udza ndi kupempherera nzeru modzichepetsa?’ (Yakobo 1:5-8; Yuda 17-21) Kora ndi omchirikiza ake, amene anapandukira ulamuliro wa Mose ndi Aroni, mwina anakhulupiriradi kuti lingaliro lawo linali lovomerezeka kwakuti sanapende zolinga zawo. Komabe, iwo analakwa kotheratu. Ndimo mmene zinalilinso kwa Aisrayeli amene anang’ung’udza ponena za kuwonongedwa kwa Kora ndi opanduka ena. Nkwanzeru chotani nanga kulola zitsanzo zimenezo kutisonkhezera kupenda zolinga zathu, kusiya kung’ung’udza kapena kudandaula, ndi kulola Yehova kutiyeretsa!—Salmo 17:1-3.
Phunzirani, Ndipo Pezani Madalitso
16. Kodi mfundo yaikulu ya chilimbikitso cha pa 1 Akorinto 10:11, 12 njotani?
16 Paulo, mouziridwa ndi Mulungu, akumaliza mpambo wa mauthenga achenjezo ndi chilimbikitso ichi: “Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife. Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:11, 12) Tisaone mwawambatu kaimidwe kathu mumpingo wachikristu.
17. Kodi tiyenera kuchitanji ngati tizindikira za cholinga china chosayenera mumtima mwathu?
17 Monga momwe chitsulo chilili chokhoza kuchita dzimbiri, mofananamo mbadwa zochimwafe za Adamu tili ndi choloŵa cha kukhoterera pa zoipa. (Genesis 8:21; Aroma 5:12) Chifukwa chake, sitiyenera kulefuka ngati tizindikira za cholinga china chosayenera mumtima mwathu. M’malo mwake, tiyeni tichitepo kanthu mwamphamvu. Pamene chitsulo chiikidwa pamalo a mpweya wachinyontho kapena pamalo okhala ndi zinthu zowononga chitsulo, dzimbiri lake limawonjezereka mofulumira. Tifunikira kupeŵa “mpweya” wa dziko la Satana, ndi zosangulutsa zake zonyansa, chisembwere chake chowanda, ndi chikhoterero chake chotsutsa cha maganizo.—Aefeso 2:1, 2.
18. Kodi Yehova wachitanji pankhani ya ndingaliro zoipa za anthu?
18 Yehova wapatsa anthu njira yoletsera ndingaliro zoipa zimene tapatsidwa mwa choloŵa. Anapereka Mwana wake wobadwa yekha kotero kuti awo okhulupirira mwa iye akakhale nawo moyo wosatha. (Yohane 3:16) Ngati titsatira mapazi a Yesu mosamalitsa ndi kusonyeza umunthu wonga wa Kristu, tidzakhala dalitso kwa ena. (1 Petro 2:21) Tidzalandiranso, osati matemberero, koma madalitso a Mulungu.
19. Kodi tingapindule motani mwa kulingalira zitsanzo za m’Malemba?
19 Ngakhale kuti ife lero tikhoza kuchimwa monga momwe anachitira Aisrayeli akale, tili ndi Mawu a Mulungu olembedwa achikwanekwane otitsogoza. M’masamba ake timaphunziramo za zochita za Yehova ndi anthu ndiponso mikhalidwe yake yosonyezedwa mwa Yesu, “chinyezimiro cha ulemerero wa [Mulungu, NW], ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe Chake.” (Ahebri 1:1-3; Yohane 14:9, 10) Kupyolera mwa pemphero ndi phunziro lakhama la Malemba, tingathe kukhala ndi “mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) Pamene tiyang’anizana ndi mayesero ndi ziyeso zina za chikhulupiriro chathu, tingapindule mwa kulingalira zitsanzo za m’Malemba ndipo makamaka chitsanzo chabwino koposa cha Yesu Kristu. Ngati titero, sitidzalandira matembero a Mulungu. M’malo mwake, tidzalandira chiyanjo cha Yehova lerolino ndi madalitso ake kosatha.
[Mawu a M’munsi]
Kodi Mungayankhe Bwanji?
◻ Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu wa Paulo wa kusakhala opembedza mafano?
◻ Kodi tingachitenji pomvera chenjezo la mtumwiyo pa dama?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kung’ung’udza ndi kudandaula?
◻ Kodi tingalandire motani madalitso a Mulungu, osati matemberero?
[Chithunzi patsamba 18]
Ngati tikufuna madalitso a Mulungu, tiyenera kupeŵa kupembedza mafano
[Zithunzi patsamba 20]
Tiyeni tichitepo kanthu motsimikizirika kuchotsa zikhumbo zosayenera m’mitima mwathu, monga momwedi dzimbiri limafunikira kuchotsedwa