Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Ngati MKristu akudwala kapena ali paulendo kotero kuti ali wosakhoza kufika paphwando la Chikumbutso, kodi angachite phwandolo mwezi umodzi pambuyo pake?
Mu Israyeli wakale Paskha anali kutchitidwa chaka chirichonse pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, wotchedwa Nisan (kapena, Abib). Koma tikupeza makonzedwe apadera olembedwa pa Numeri 9:10, 11 akuti: ‘Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma adzichitira Yehova Paskha. Mwezi wachiŵiri [wotchedwa Iyyar, kapena Ziv], tsiku lake lakhumi ndi chinayi, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi woŵaŵa.’
Tawonani kuti chochitikachi sichinapereke masiku aŵiri osiyana a Paskha (Nisan 14 kapena Ziv 14), kuti Mwisrayeli aliyense kapena banja akakhala waufulu kusankha, modalira pa zomkomera. Makonzedwe achakudya cha Paskha m’mwezi wachiŵiri anali ndi polekezera. Anali apadera kaamba ka Mwisrayeli amene mwamwambo anali wodetsedwa pa Nisan 14 kapena amene anali pamtunda wautali kuchokera kumalo ozoloŵereka ochitirako phwandolo.
Cholembedwa chimodzi chokha cha kugwiritsiridwa ntchito mofala kwa kakonzedweka chinali nthaŵi pamene Mfumu Hezekiya wokhulupirika anayambiranso kusungidwa kwa Phwando la Mikate Yopanda Chotupitsa. Panalibe nthaŵi yakukonzekera mwezi woyamba (popeza ansembewo sanali okonzekera ndiponso anthu sanasonkhane), chotero linachitidwa pa tsiku la 14 lamwezi wachiŵiri.—2 Mbiri 29:17; 30:1-5.
Kusiyapo zochitika zapadera zotero, Ayuda anasunga Paskha padeti limene Mulungu anasankha. (Eksodo 12:17-20, 41, 42; Levitiko 23:5) Yesu ndi ophunzira ake anachita phwandolo monga momwe Chilamulo chinanenera, sanachitire deti limenelo modzifunira. Luka akusimba kuti: ‘Tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paskha. Ndipo iye [Yesu] anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife Paskha, kuti tidye.’—Luka 22:7, 8.
Panthaŵi imeneyo Yesu anayambitsa phwando la chaka ndi chaka limene Akristu amalidziŵa monga Mgonero wa Ambuye. Phindu lakuti Akristu afikepo silingathe kugogomezeredwa mopambanitsa. Ichi chiri chochitika chofunikadi koposa m’chaka kwa Mboni za Yehova. Mawu a Yesu amasonyeza chifukwa chake; iye anati: ‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’ (Luka 22:19) Chotero, aliyense wa Mboni za Yehova ayenera kulinganiza miyezi ingapo pasadakhale kusunga deti laphwandolo kukhala lopanda zochitika zina zirizonse. Mgonero wa Ambuye udzachitidwa pa Lachiŵiri, April 6, 1993, pambuyo pakuloŵa kwadzuŵa kumaloko.
M’zochitika za kamodzikamodzi mkhalidwe wosawonedweratu, monga ngati kudwala kapena zopinga zaulendo, zingathe kulepheretsa Mkristu kufikapo monga momwe iye analinganizira. Kodi zikatero chingachitidwe nchiyani?
Mkati mwa phwando mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira zimaperekedwa, ndipo awo amene ali odzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu ndi osankhidwira moyo kumwamba amadya. (Mateyu 26:26-29; Luka 22:28-30) Ngati munthu amene wakhala alikudya chaka chirichonse wabindikiritsidwa ndi matenda chaka chino panyumba kapena m’chipatala, akulu ampingo wam’malowo adzachita makonzedwe akuti mmodzi wa iwo apititse mkate ndi vinyo kwa wodwalayo, kukakambitsirana naye malemba a Baibulo oyenerera ankhaniyo, ndi kupereka zizindikirozo. Ngati Mkristu wodzozedwa ali kutali ndi mpingo wakwawo, ayenera kulinganiza kufika pampingo m’dera limene iye adzakhala ali padeti limenelo.
Chotero, kukakhala m’mikhalidwe yakamodzikamodzi kwambiri kuti Mkristu wodzozedwa akafunikira kuchita phwando la Mgonero wa Ambuye masiku 30 pambuyo pake (mwezi weniweni umodzi), mogwirizana ndi lamulo la pa Numeri 9:10, 11 ndi chitsanzo cha pa 2 Mbiri 30:1-3, 15.
Awo amene ali gulu la “nkhosa zina” za Yesu, okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso, sakulamulidwa kudya mkate ndi kumwa vinyo. (Yohane 10:16) Kuli kofunika kufika pa phwando lachaka ndi chaka, koma iwo samadya zizindikirozo. Chotero ngati mmodzi wa iwo adwala kapena ali paulendo ndipo chotero sali pampingo uliwonse madzulowo, iye akakhoza kuŵerenga yekha malemba oyenerera (kuphatikizapo cholembedwa cha Yesu cha kuyambitsa phwandolo) ndi kupempherera dalitso la Yehova pa chochitika cha padziko lonse lapansicho. Koma m’chochitikachi, palibe kufunikira kulikonse kwa kuchita makonzedwe owonjezereka amsonkhano kapena nkhani ya Baibulo yapadera mwezi umodzi pambuyo pake.