Lingaliro la Baibulo
Kodi Kuba kwa wosauka Nkololeka?
“Umphaŵi ndiwo mdani wamkulu wa chimwemwe cha anthu; umawonongadi ufulu ndipo umachititsa kuti mikhalidwe ina yabwino ikhale yosatheka kuisonyeza, ndipo ina kukhala yovuta kwambiri.”—Samuel Johnson, wolemba mabuku wa m’zaka za zana la 18.
KATSWIRI wina pa zaboma Magnus Aurelius Cassiodorus anati: “Umphaŵi ndiwo mayi wa upandu.” Malingaliro ameneŵa amasonyeza zonena kuti maupandu ena amangochitika mwachibadwa chifukwa cha kusauka. Ambiri lerolino amavomereza zimenezo, makamaka pamene upanduwo uli wa kuba.
Lingaliro lakuti kuba kwa wosauka nkololeka nlofala kwambiri. Talingalirani nthanthi ina yotchuka yachingelezi ya m’zaka za zana la 14 yonena za Robin Hood, mpandu wina wa m’nthano amene ankabera anthu olemera ndi kumagaŵira osauka mapindu omwe ankapeza. Kwa zaka mazana ambiri anayesedwa ngwazi.
Kunena zoona, anthu ambiri lerolino akukumana ndi mavuto aakulu azachuma. Posachedwapa World Bank inapereka lipoti lakuti pali anthu 1,300, 000 000 amene amadya zochepera dola imodzi patsiku. Pa kufufuza kwina, 70 peresenti ya Afilipino anati amadziŵerengera pakati pa anthu osauka. M’Brazil, 20 peresenti ya anthu olemera kopambana amapeza ndalama zoŵirikiza nthaŵi 32 kuposa 20 peresenti ya anthu osauka kopambana. Mikhalidwe yotere ikhoza kukhumudwitsa anthu ena moti nkufika pamlingo wa kugwiritsira ntchito njira iliyonse, ngakhale kuba kumene, kungoti apeze zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.
Baibulo limatsutsiratu kuba. Lachisanu ndi chitatu pa Malamulo Khumi limati: “Usabe.” (Eksodo 20:15) Komabe, alipo ambiri okhulupirira Baibulo amene amati kuba si mlandu ngati wakubayo waba chifukwa cha umphaŵi womvetsa chisoni.
Zimenezi zimabutsa mafunso ofunika kwambiri: Kodi kuba kwa wosauka sikulakwadi? Kodi munthu angachitenji pamene ali m’mavuto aakulu kwenikweni a zachuma? Bwanji ngati ali ndi ana odwala kapena anjala ofunika kuwasamalira? Kodi Yehova Mulungu amalola kuba m’mikhalidwe imeneyi, makamaka ngati zinthuzo zabedwa kwa aja amene sangavutike ndi kubedwa kwa zinthuzo?
Kodi Mulungu Amati Chiyani?
Pakuti Yesu anaonetsa umunthu wa Atate wake, chitsanzo chake chingatithandize kumvetsa lingaliro la Mulungu. (Yohane 12:49) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anali wachifundo kwambiri pochita ndi anthu osauka. Baibulo limati “poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni.” (Mateyu 9:36) Komabe, iye sanalole kuba kulikonse kaya mikhalidwe ikhale yotani. Mofananamo, ngakhale kuti Mulungu amadera nkhaŵa osauka, samaona kusaukako kukhala chilolezo choti munthu abe. Pa Yesaya 61:8, Baibulo limatiuza kuti Mulungu ‘amada chifwamba ndi choipa.’ Ndipo mtumwi Paulo anasonyeza poyera kuti mbala sizidzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Choncho sitinasiidwe m’malere ponena za lingaliro la Mulungu.—1 Akorinto 6:10.
Komabe, Miyambo 6:30 imati “anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala.” Kodi mawuŵa amalola kuba? Kutalitali. Nkhani yake imasonyeza kuti Mulungu amalangabe mbalayo pa cholakwa chakecho. Vesi lotsatira limati: “Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kaŵiri; Idzapereka chuma chonse cha m’nyumba yake.”—Miyambo 6:31.
Ngakhale kuti mbala yakuba chifukwa cha njala singakhale ndi mlandu wofanana ndi munthu wakuba chifukwa cha dyera kapena wongofuna kuvutitsa mnzake, awo ofuna chiyanjo cha Mulungu sayenera kupezeka ndi mlandu wa kuba wa mtundu uliwonse. Ngakhale pamene wina wasauka kwadzaoneni, kuba kumanyozetsa Mulungu. Miyambo 30:8, 9 amanena motere: “Mundidyetse zakudya zondiyenera, . . . kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.” Inde, wakuba amatonza dzina la Mulungu. Chifukwa chakuti kuba ndi mchitidwe wopanda chikondi, kubera wolemera kaya wosauka ndi tchimo ndithu. Kwa awo amene amakonda Mulungu ndi mnansi wawo, kuba sikololeka konse.—Mateyu 22:39; Aroma 13:9, 10.
Lingaliro lakuti munthu wosauka ali ndi ufulu wa kuba si lanzeru. Kuteroko kungafanane ndi kunena kuti munthu wa pampikisano waliŵiro wosalimba kwambiri ali ndi ufulu wa kugwiritsira ntchito mankhwala oletsedwa kuti apambane. Ngakhale ngati angapambane, iye wagwiritsira ntchito chinyengo. Ena adzaona kuti iye wawatengera chipambano chawo mwa njira yobera. Chimodzimodzi ndi mbala. Amatenga zinthu za ena mwa kuba. Kusauka kwakeko sikumchotsera mlandu wakuba.
Mbala iliyonse yofuna chiyanjo cha Mulungu iyenera kulapa ndi kusiya njira yake. Baibulo limalangiza kuti: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.” (Aefeso 4:28) Amene kumbuyoku anali mbala ndipo tsopano alapadi angakhale nacho chitsimikizo chakuti Yehova adzawakhululukira.—Ezekieli 33:14-16.
Kodi Osauka Angachitenji?
Baibulo limalonjeza kuti: “Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.” (Miyambo 10:3) Mulungu samathandiza amene amaswa dala lamulo lake kuti akhutiritse zokhumba zawo. Koma amamvera chifundo amene amamumvera moona mtima, ndipo amadalitsa khama lawo pamene amayesa kupeza zosoŵa pamoyo wawo.—Salmo 37:25.
Anthu mamiliyoni ambiri apeza kuti pamene atsatira makhalidwe aumulungu, zinthu zimawayendera bwino pamoyo wawo. Mwachitsanzo, kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo wa kukhala wakhama ndi kupeŵa machitachita oipa, monga ngati juga, uchidakwa, kusuta, ndi mankhwala osokoneza bongo, kwawathandiza kupeza zambiri zofunika pamoyo wawo. (Agalatiya 5:19-21) Zimenezi zimafuna kuti asonyeze chikhulupiriro, ndipo awo amene atero aona kuti “Yehova ndiye wabwino” ndi kuti amathandizadi amene amamdalira.—Salmo 34:8.
[Mawu a Chithunzi patsamba 20]
Robin Hood: General Research Division/The New York Public Library/Astor, Lenox and Tilden Foundations