Nyimbo 219
Mpando Waufumu Wakumwamba wa Yehova
1. Inu Yehova, ndinu M’lungu.
Ulemerero Mbuye, Pampandowo.
Utawaleza ukuŵala.
Inu ndinu Mulungu Wamtendere.
2. Akulu ovala zoyera,
Mafumu ndi ansembe. Ngokongola!
Zamoyo zinayi Zifu’la:
Nzeru mphamvu chikondi—Zitamanda.
3. Mphenzi mabingu mutulutsa.
Onse amamatire Chowonadi.
Nyanja inena za chiyero.
Tiyeretsedwetu ndi Mawu anu.
4. Masomphenyawa titamanu,
Ndinu wamphamvuyonse, Woyeradi.
Yesu Mpulumutsi ndi Mfumu.
Mwa ‘ye tikufikani Ndi ulemu.