Nyimbo 166
Wonani Khamu la Yehova!
1. Wonani khamulo,
La Yehovayo,
Lilengeza ’fumu
Wa Kristu Yesu.
Lipita mtsogolo,
Molimba mtima;
Lodalira M’lungu,
Lopanda mantha.
Lidalira M’lungu,
Potsata Kristu,
Lilalikirabe:
“Alamulira.”
2. Atumiki a Ya
Afuna “nkhosa”
Ziri mu Babulo
Ndipo zilira.
Ayesayesabe
Kuzimasula;
Aziitanira
Kumisonkhano.
Zitamasulidwa,
Ziphunzitsidwa
Kuzindikiratu
Zinthu zowona.
3. Tawonani ‘khamu
Lalikululo’,
Ndi ‘otsalirawo,’
Gulu lamphamvu.
Liri lochenjera,
Monga njokazo,
Pansi pa chizunzo,
Lipilirabe.
Limalemekeza
Yehova M’lungu;
Kulambira kwawo
kuwonjezeka.