Nyimbo 224
“Senzani Goli Langa”
1. Inu otopetsedwa,
Ndi kupsinjika konse,
Yesu akuitana:
‘Idzanitu kwa ine.’
2. ‘Ine ndiri wofatsa,
Sindirinso wadziko.
Phunzirani kwa ine,
Mudzapeŵa muviwo.’
3. ‘Katundu ngwopepuka,
Ndi golilo nlofeŵa.
Ndipumulitsa mtima
Kwa onse olungama.’
4. Mukhaletu owona.
Adzakulimbitsani;
Muli m’goli limodzi,
Potumikira M’lungu.