Kodi Muli ndi Oda Yokhazikika ya Magazini?
1 Popeza kuti tsopano tili m’makonzedwe a chopereka chaufulu ndi motani mmene magazini aziyendera pampingo? Sipazikhala kuti woyambirira kufika pakauntala ya magazini ndiye amene azitenga magazini moyambirira. Timalangizidwa ‘kuchita zonse moyenera ndi molongosoka.’ (1 Akor. 14:40) Motero, kodi tiyenera kutsatira njira iti kuti pasamakhale chisokonezo kapena kukhumudwitsana? Chabwino, kumbukirani mphatika ya mutu wakuti “Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa,” yopezeka mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1995. Inatiuza ‘kukhala ndi oda yoikika ya magazini,’ ikumati: “Lembetsani oda yokuyenerani kwa mbale wosamalira magazini ya unyinji wodziŵika wa makope a magazini alionse. M’njira imeneyi, inu ndi banja lanu mudzakhala mukulandira magazini okwanira mokhazikika.” Kodi mwachita zimenezi?
2 Magazini akafika mu mpingo kodi azigaŵidwa motani? Wosamalira magazini adzapereka kwa wofalitsa aliyense chiŵerengero cha magazini amene iye anaoda. Akulu ayenera kudziŵitsa ofalitsa kuti sayenera kufuna magazini oposa amene anaoda popeza zimenezi zidzapangitsa kuti wina magazini am’pereŵere. Ndithudi, ngati m’kupita kwa nthaŵi wina angafune kuwonjezera kapena kuchepetsa chiŵerengero cha magazini amene amalandira angauze wosamalira magazini kuti asinthe oda yakeyo. Ndiyeno, wosamalira magazini adzasintha pa oda ya mpingo yopita ku Sosaite. Dziŵani kuti pamatenga miyezi itatu kuti kusintha kumeneku kutheke. Ngati mungachoke pampingopo kwa nthaŵi yaitali, muuzeni wosamalira magazini ngati mukufuna kuti magazini anuwo aziwapereka kwa munthu wina mpaka inu mutadzabwera.
3 Sosaite ikufuna kuona wofalitsa aliyense wodziŵa kuŵerenga ndiponso ana ake odziŵa kuŵerenga ali ndi kope lawolawo la Nsanja ya Olonda. Mungakonze zooda kope limodzi la magazini ya Galamukani! la banja lanu. China chimene muyenera kuŵerengera ndi magazini amene inu ndi banja lanu mudzafuna mu utumiki wakumunda. Mwanjira imeneyi, akulu sadzafunikira kungolota chiŵerengero cha magazini oodera mpingo komano adzaphatikiza pamodzi maoda a anthu onse kuti akhale ndi nambala yolondola. Bwanji osalembetsa oda yokhazikika ya magazini? Wosamalira magazini adzalemba maoda onseŵa ndi kuphatikiza onse pamodzi. Ayenera kuoda ena ongowonjezera a anthu osonyeza chidwi amene alibe oda yokhazikika. Izi zidzapangitsa kuti aliyense azikhala ndi chiŵerengero cha magazini chimene amafuna nthaŵi zonse popanda kuopa kuti wina wake atenga magazini onse iwo osatengako kanthu.