Nyimbo 145
Khalani Woleza Mtima
1. N’kuleza mtima kotani
nanga Yehova asonyeza!
Nkana avutika apilira,
Samatopatu konse.
Anapilira ndi Israyeli,
Ndi mtundu wa’nthu onse.
Chotero nkhosa zonse zapeza
Kuleza mtima kwake.
2. Yehova Mulungu wamuyaya
Aleza mtima nafe,
Ndithudi okhulukidwa ife
Tisonyeze mkhalidwe.
Timafuna chipatso cha mzimu
Kutithandiza m’munda.
Kuti tisagonje ku choipa,
Tikhalebe ofatsa.
3. Kuleza mtima kutithandiza
Kusungabe umodzi
Mumpingotu ndiponso mubanja
M’lungutu akondwere!
Chikondi cha M’lungu chithandiza
Kuti tileze mtima.
Tikufuna kuti tipilire
Kufikira ungwiro.