Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/01 tsamba 4
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 4/01 tsamba 4

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Si mwayi wake! Monga Mboni za Yehova, ndife amwayi chifukwa chakuti tadziŵa Yehova, Mulungu yekha woona ndi wamoyo, Mlengi wa chilengedwe chonse, komanso chifukwa tatenga dzina lake ndiponso timam’tumikira. Palibenso madalitso oposa ameneŵa!—Yes. 43:12; Aheb. 8:11.

Tikuyembekeza kupulumuka komanso tili ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu kuti enanso alambire Yehova nayembekezenso kupulumuka. (Mat. 24:14; Aroma 10:13, 14; 1 Ates. 5:8) Timasangalalanso kuti tili m’gulu la ubale wapadziko lonse la olambira amene amakondana ndi kuthandizana mwachangu. Zonsezitu n’zabwino!

N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti: “Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: . . . Loŵani ku zipata zake ndi chiyamiko, ndi ku mabwalo ake ndi chilemekezo: M’yamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimamka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.” (Sal. 100:2-5) Kutumikira Yehova mokondwera kumagwirizana kwambiri ndi kukhala naye paubale wolimba. Amatilola kukhala naye paubale umenewo ndipo ndi mwayi wathu kuti tiulimbitse. Tikakhala ndi ubale umenewu, timadziŵa kuti Yehova nthaŵi zonse ali wokonzeka kutithandiza ndi kutilimbitsa nthaŵi za mavuto. Timakhulupirira kuti adzapereka mphamvu ndi malangizo auzimu zofunika pothana ndi mavuto a masiku otsiriza a dongosolo la zinthu lino. Mosasamala kanthu za mavuto amene timakumana nawo, timasangalala ndi utumiki wathu, ndipo tsiku lililonse timayamika Yehova chifukwa ‘amatisamalira ife,’ monga momwe Mawu ake amanenera.—1 Pet. 5:7.

Chaka chatha, Yehova anatidalitsadi kwambiri. Pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu,” tinasangalala kwambiri kukhala pamodzi ndi namtindi wa anthu amene ali ndi chikhulupiriro chapadera ngati chathu, kuimba ndi kudyera limodzi pagome lauzimu la Yehova. Pa Maphunziro a Buku a Mpingo, tinasangalala kwambiri kuphunzira pamodzi buku la Samalani Ulosi wa Danieli! lolimbitsa chikhulupiriro chathu. Komanso, tinasangalala zedi kulandira Gawo 1 la buku latsopano la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse! ‘Chikho chathu chisefuka.’—Sal. 23:5.

N’zosangalatsa kudziŵa kuti ifeyo abale ndi alongo auzimu mamiliyoni, tikutumikira Yehova mogwirizana! N’zolimbikitsatu kwambiri kuona ziŵerengero zapamwamba zatsopano za mu utumiki wakumunda! Tikusangalala kuti tinali ndi anthu ankhaninkhani pa Chikumbutso cha imfa ya Ambuye wathu ndipo anafika mosasamala kanthu za zovuta za dzikoli. Tikayang’ana munda wa dziko lonse, n’zoonekeratu kuti ntchito yotuta n’njaikuludi. (Luka 10:2) Chaka chatha mlungu uliwonse pa avareji ophunzira Baibulo 5,555 anapita patsogolo mpaka ubatizo wa m’madzi, kusonyeza kudzipatulira kwawo. Ngakhale ntchito yotuta n’njaikulu m’madera ena a dziko lapansi kuposa ena, tonse tikusangalala ndi zimene Yehova akuchita. Tili ndi umboni woonekeratu wakuti akudalitsa ntchito ya atumiki ake onse.

Chosangalatsa chinanso ndi kumangidwa kwa Nyumba za Ufumu zatsopano! Tili osangalala kwambiri kuona abale ndi alongo athu m’mayiko omwe akutukuka akuchirikiza ndi mtima wonse ntchitoyi. Magulu Omanga Nyumba za Ufumu ophunzitsidwa bwino amanga kale Nyumba za Ufumu zambiri. Abale ameneŵa amapita ku mipingo yosiyanasiyana m’dziko lawo kukatsogolera ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Popeza kuti pakufunikabe Nyumba za Ufumu zambiri, tikufuna antchito odzifunira m’mayiko amene akutukuka kuti athandize ntchito yofunikayi. Ngati muli m’dziko lotere, kodi mungadzipereke? Si mmene abale ndi alongo athu okondedwa amayamikirira kukhala ndi Nyumba ya Ufumu yawoyawo yolambiriramo! Ndipo amathokoza kwambiri abale onse padziko lapansi chifukwa cha ndalama zogwirira ntchitoyi!

Tikusangalalanso kumva milandu imene yatiyendera bwino. Komabe, m’madera ambiri muli anthu olamulira amene akufuna kuthetsa kulambira Yehova. Polimbana ndi zimenezi, timakhulupirira kuti, Yehova akafuna kuthandiza sasamala kuti adani alipo angati kapena kuti atumiki ake akuoneka osatetezeka motani. (2 Mbiri 14:11) Tikukuthokozani abale ndi alongo nonse amene mukupitiriza kuima nji pa kulambira koona.

Pitirizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndi kudalira kwambiri utsogoleri wa Yehova pamene mosangalala mukukwaniritsa maudindo anu achikristu. (Miy. 3:5, 6 ) Musataye mtima, kaya adani achite zotani. Kumbukirani mmene Elisa analimbikitsira mnyamata wake wamantha uja. “Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” (2 Maf. 6:15-17) Lerolino, magulu ankhondo a Yehova akumwamba ndi okonzeka kuteteza zinthu za kulambira koyera monga zinalili masiku a Elisa. Tili ndi chidaliro poyembekeza za m’tsogolo. Zonse zili m’manja mwa Yehova. Anthu sangalimbane naye. Wakhazika Mwana wake pampando ndipo wam’patsa ulamuliro wonse. “Odala onse akum’khulupirira Iye.”—Sal. 2:1-6, 12.

Kumbukirani kuti inu abale ndi alongo nonse timakukondani ndipo timakuganizirani kwambiri. Pemphero lathu lapansi pa mtima n’lakuti nonse ‘muime amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.’—Akol. 4:12, NW.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena