Mwambo Wapadera M’Malaŵi
1 Loŵeruka, pa May 19, namtindi wa abale athu akwathu konkuno pafupifupi 2,000 anasonkhana pamodzi ndi alendo a m’mayiko ambiri ku likulu la Mboni za Yehova ku Lilongwe. Panali alendo ochokera ku Belgium, Benin, Botswana, Britain, Canada, Denmark, Democratic Republic of Congo, Ethiopia, France, Germany, Kenya, Mozambique, Namibia, Nigeria, South Africa, Spain, Sweden, Tanzania, United States, Zambia ndi Zimbabwe. Kodi kunali chiyani? Kunalitu mwambo wopatulira kwa Yehova nthambi yatsopano imene ili pafupi ndi Mtsinje wa Lingadzi. Anamanga shedi yaikulu kwambiri ya bulugamu, nsungwi ndiponso udzu, kuti anthu onse amene anabwera pa mwambowu asapse ndi dzuŵa. Anamanganso pulatifomu yokongola ya udzu ya mamangidwe a kwathu kuno pomwe pankachitikira pulogalamu yolimbikitsayi. Monga mukudziŵa, chifukwa cha kuchepa kwa malo, amene anaitanidwa anali abale ndi alongo okhawo amene atha zaka 40 kapena kuposerapo atabatizidwa.
2 Amene analipo pamwambowu anamva mbiri yachidule ya ntchito ya m’dziko lino ndiponso anamvetsera mwachidwi mbiri ya momwe ntchito yomanga nthambiyi yayendera mwachangu. Ntchito yomanga yeniyeni inayamba mu February 1998 mpaka October 2000 basi. Mboni zogwira ntchito modzifunira za m’mayiko ambiri zinagwira ntchito pamodzi ndi abale awo a kwathu kuno, zimene zinachititsa anthu amene ankaona kapena kumva zomwe zinali kuchitika kunena zambiri. Anakamba nkhani yopatulira nthambi ndi Mbale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira ndipo mutu wankhani unali wakuti “Kondwerani ndi Zimene Yehova Akupanga.” Mbale Sebastien Johnson wa ku nthambi ya ku Congo Kinshasa, amene anabwera pa nthambi ya Malaŵi monga woyang’anira woyendera nthambi, anakamba nkhani yamutu wakuti “Kodi Mumayamikira Kutumikira Yehova?”
3 Tsiku lotsatira, Lamlungu, pa May 20, khamu la anthu linasonkhana ku Civo Stadium ku Lilongwe kukamvetsera pulogalamu yapadera imene inakambidwa pamsonkhano wa pa May 19. Anthu miyandamiyanda ochokera m’madera onse a dziko lino ndiponso alendo a m’mayiko amene tawatchula aja amene anabwera kumwambo wopatulirawu analinso komweko. Anthu anasangalala kumva malipoti a ntchito ya Yehova m’mayiko ena mwa amenewo, monga anachitira pa May 19. Mbale Johnson anakamba nkhani inanso yamutu wakuti “Mtima Wanu Uzikhala pa Zinthu Zofunika Kwambiri.” Nayenso Mbale Pierce anakamba nkhani ina.
4 Onse amene analipo masiku aŵiri apadera ameneŵa ku Lilongwe anabwerera kwawo ali osangalala kwabasi ndiponso anachita chidwi ndi ubale wapadziko lonse. (1 Pet. 5:9) Anabwerera kwawo ali “osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira” anthu ake.—1 Maf. 8:66.