Ŵerengani ndi Ana Anu
Malinga ndi kunena kwa magazini ina ya ku Brazil yotchedwa Veja, ana a makolo okonda kuŵerenga kwambiri nawonso amayamba kukonda kwambiri mabuku kuposa ana amene makolo awo sawapatsa chitsanzo chakuŵerenga chimenechi m’nyumba. Katswiri wina pankhani yakaleredwe ka ana, Martha Hoppe, anati: “Kuŵerengera pamodzi ndi ana kumakulitsa ubwenzi pakati pa makolo ndi ana awo ndipo anawo amamvetsa bwino zimene mabukuwo akunena.”
Kuŵerengera ana anu mofuula kumakupatsaninso mpata woyankha mafunso. Mukhoza kumakambirana za zithunzi zilizonse zimene zikusonyezedwa m’nkhaniyo. Hoppe anati: “Mwana akamamvetsetsa zimene mabuku amanena, amachita nawo chidwi kwambiri moti ngati akufuna kudziŵa kanthu kena, amakafufuza m’mabuku.”
Makolo ambiri a Mboni za Yehova amakonda kuŵerenga ndi ana awo. Amaŵerenga mabuku ngati lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, ndi lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.a Mabuku ngati ameneŵa amathandiza ana kuŵerenga bwino ndiponso amawapangitsa kukonda buku lofala kwambiri padziko lonse—Baibulo Loyera. Choncho, ngati muli kholo, asonyezeni ana anu chitsanzo chabwino mwa kuŵerenga mwakhama Mawu a Mulungu. (Yoswa 1:7, 8) Mulimonse mmene zingakhalire, musalephere kuwaŵerengera!
[Mawu a M’munsi]
a Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.