Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/03 tsamba 1
  • Anatiikiza Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anatiikiza Uthenga Wabwino
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Choyamba N’chiyani M’moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 5/03 tsamba 1

Anatiikiza Uthenga Wabwino

1 Ndife amwayi kwambiri chifukwa choti anatiikiza uthenga wabwino wa Mulungu! (1 Ates. 2:4) Ngakhale kuti anthu ena sangafune kumva uthenga wamphamvuwu, anthu oona mitima amakopeka nawo monga mmene anthu amachitira akamva kafungo kabwino. (2 Akor. 2:14-16) Anthu amene amamvetsera ndi kulabadira uthenga wabwino adzapulumuka. (Aroma 1:16) Kodi tichite nawo chiyani uthenga wabwino umene anatiikizawu?

2 Yesu ndi Atumwi: Yesu anaika ntchito yolengeza uthenga wabwino patsogolo pa zonse. (Luka 4:18, 43) Ngakhale panthaŵi yomwe anali atatopa ndiponso anali ndi njala, iye ankauza ena uthenga wabwino chifukwa chokonda anthu ndiponso chifukwa ankaona kuti uthengawo ndi wofunika. (Marko 6:30-34) Kudzera m’zonena komanso zochita zake, iye anawasonyeza bwino ophunzira ake kufunika kwa ntchito yolalikira za Ufumu.—Mat. 28:18-20; Marko 13:10.

3 Potsanzira Yesu, atumwi analimbikira kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu. Ngakhale panthaŵi yomwe anawamenya ndi kuwalamula kuti asiye kulalikira, iwo “sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira” uthenga wabwino. (Mac. 5:40-42) Mtumwi Paulo anagwira ntchito imeneyi mwakhama kwambiri. (1 Akor. 15:9, 10; Akol. 1:29) Iye anayerekezera mwayi wolalikira uthenga wabwino ndi kukhala ndi ngongole ndi anthu, ndipo anali wokonzeka kuvutika kuti abweze ngongoleyo.—Mac. 20:24; Aroma 1:14-16.

4 Mwayi Wathu Masiku Ano: Kuona kuti ntchito yopatulika yomwe anatiikizayi ndi yofunika kudzatipangitsa kufufuza njira zimene tingafutukulire ntchito yathu yolalikira. (Aroma 15:16) Edward amene ankayenda panjinga ya anthu olumala, ankakhala pa khomo la hotela ina n’kumafotokozera alendo okhala pahotelapo za chikhulupiriro chake. Komabe, pofuna kuti achite zambiri iye anakonzetsa malo m’galimoto ya bokosi bode kuti aziikamo njinga yake ndipo pogwiritsira ntchito galimoto imeneyi anachita upainiya kwa zaka zambiri komanso anayenda makilomita ambiri. Mofanana ndi Edward, anthu ambiri masiku ano asintha zina ndi zina pa moyo wawo n’cholinga choti achite zochuluka pofalitsa uthenga wabwino.

5 Mwa kutsanzira Yesu ndiponso atumwi, tiyeni nthaŵi zonse tiziika ntchito yolalikira patsogolo pa zonse m’moyo wathu. Tikatero, timasonyeza kuti timakonda anthu komanso timasonyeza kuti uthenga wabwino womwe anatiikizawu ndi wofunika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena