Lipoti Labwino Limalimbikitsa
Paulo ndi Barnaba atauza Akristu ena oyambirira kuti anthu ambiri amene sanali Ayuda atembenuka, “[a]nakondweretsa kwambiri abale onse.” (Mac. 15:3) Ifenso m’Malawi muno tachita zomwezo ndi Lipoti la Utumiki Wakumunda la February, tikaganiza kuti aka n’koyamba kukhala ndi anthu oposa 55,000 amene akuchita nawo utumiki wakumunda. N’zochititsa chidwi kuti mwezi umenewu wokha tinagaŵira mabuku 22,166, mabulosha 61,163 ndi magazini 253,741. Manambala ameneŵa ndi apamwamba kwambiri amene sitinakhale nawo ndi kale lonse m’Malawi muno. Mosakayikira kuchita bwino kumeneku pankhani yogaŵira zofalitsa zathu kwatithandiza kukhala ndi nambala yapamwamba ya maphunziro a Baibulo okwana 50,115, amene sitinayambe takhala nawo m’mwezi umodzi. Aka n’koyamba kuti tipitirire pa 50,000! Kukhala ndi Nyumba za Ufumu zatsopano kwathandizanso; pamene timafika kumapeto kwa mwezi wa February, n’kuti nyumba zokwana 613 zitamangidwa.
Zotsatira zabwino zimenezi zikusonyeza kuti tili mu nthaŵi yomwe anthu akuwonjezeka kwambiri m’Malawi muno. Pamene tikupitiriza kuphunzira mwakhama ndi anthu achidwi tingayembekezere kuona ofalitsa ambiri akuchita nawo ntchito yotuta polemekeza Mwini zotuta. (Mat. 9:37, 38) Abale ndi alongo, pitirizani kulalikira ndi kuphunzitsa.—Mat. 24:14; 28:19, 20.