Nyimbo 55
Kuyenda ndi Yehova Masiku Onse
(Mika 6:8)
1. Timayenda ndi Yehova,
Masiku alionse.
Kukoma mtima kwakeko
Wapereka kwa anthu!
Pokhala ndi mwa kusankha
Kuyenda ndi Mulungu,
Tiyamba n’kudzipereka
Kuimira Mulungu.
2. Kuyendabe ndi Atate
Ndiko njira yanzeru.
Tazingidwa ndi adani
Angatilande mphotho.
Pali Satana n’ziwanda
Ndi misampha yathupi
Ndi chuma chadziko lino;
Zingakole mapazi!
3. M’lungu wapatsa thandizo
Kupyolera mwa mzimu,
Kupyola mwampingo wake,
Ndi mwa mapempherowo.
Poyendabe ndi Yehova,
Tichite choyenera.
Tikhaletu ndi chikondi
Ndipo odzichepetsa.