Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/04 tsamba 8
  • Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kuthamanga Makaniwo Mwachipiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chipiriro—Nchofunika kwa Akristu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 2/04 tsamba 8

Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera

1 Ambuye wathu ananeneratu kuti ophunzira ake adzakumana ndi masautso. (Mat. 24:9) Kodi ziyeso tiziziona bwanji? Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira masautso? Msonkhano wadera wa chaka chautumiki cha 2004 udzayankha mafunso ameneŵa. Mutu wake ndi woti “Kondwerani M’chiyembekezo, Pirirani M’masautso.”—Aroma 12:12.

2 Nkhani Zosiyirana Ziŵiri: Nkhani yosiyirana yoyamba ya mutu wakuti “Balani Zipatso Mopirira,” idzafotokoza njira zimene timabalira zipatso. Ofalitsa angapo adzafunsidwa mafunso kuti anene mmene amachitira polalikira ndi pophunzitsa posonyeza kuti nthaŵi yatsala pang’ono. Makolo makamaka adzafunika kumvetsera mwachidwi nkhani yakuti “Tikamalangizidwa ndi Yehova,” imene idzafotokoze mmene makolo angakambiranire zinthu ndi ana awo. Wokamba nkhani yomaliza mu nkhani yosiyirana imeneyi adzafotokoza zimene tiyenera kuchita kuti tipeŵe kukopeka ndi dziko, zimene zingatipangitse kukhala osabala zipatso.—Marko 4:19.

3 “Thamangani Mopirira pa Mpikisanowo” ndiwo mutu wa nkhani yosiyirana yachiŵiri. Nkhani imeneyi idzafotokoza momveka bwino mmene moyo wathu ulili ngati mpikisano. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuthamanga momvera malamulo ake? Kodi tingataye bwanji cholemetsa chilichonse kuti tisaleme pa mpikisano wa moyo? Malangizo a m’Malemba apanthaŵi yake amene adzaperekedwe adzatithandiza tonsefe kupitiriza kuthamanga mopirira.

4 Kupirira Kumakondweretsa Mulungu: Nkhani zimene oyang’anira oyendayenda adzakambe zidzalimbitsa chikhulupiriro cha anthu amene adzamvetsere mwachidwi ndi kugwiritsa ntchito malangizo ake. Imodzi mwa nkhani zimene woyang’anira chigawo adzakambe ili ndi mutu wakuti “Kupirira Kumachititsa Kuti Tikhale Ovomerezeka kwa Mulungu.” Nkhani ya onse idzayankha mafunso akuti: Kodi mitundu iyenera kudalira dzina la ndani, ndipo kodi pakufunika chiyani kuti ichite zimenezi? Nkhani yomaliza yoti “Ngati Mupirira Mudzapeza Miyoyo Yanu,” idzafotokoza chimene chinathandiza Yesu kupirira popanda kukwiya pamene anthu amam’chitira zinthu zosalungama.

5 Musaiŵale kudzabweretsa buku lanu la Sukulu ya Utumiki ndi Nsanja ya Olonda ya mlungu umenewo. Muzidzalemba notsi kuti zidzakuthandizeni kumvetsera mwachidwi komanso kuti mudzazigwiritse ntchito m’tsogolo. Padzakhala kubwereramo kwa pulogalamuyi ku mpingo m’tsogolo muno.

6 Ndi Yehova mwiniwake amene wakonza phwando lauzimu limeneli. Bwerani! Dzadyeni! Mitima yathu idzasangalala ngati tidzabwera kudzapindula ndi pulogalamu yonseyo.—Yes. 65:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena