-
ZilengezoUtumiki wa Ufumu—2004 | May
-
-
Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu May: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, omwe ena mwa iwo angakhale amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kugaŵira buku la Lambirani Mulungu. Tichite zotheka kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba, makamaka ngati ena anamaliza kale kuphunzira buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. June: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Pogwiritsa ntchito buloshali, yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Mabulosha alionse amene mpingo uli nawo.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa June 1 kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Zopereka za m’macheke zizilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi ya nthambi ndi Watch Tower Bible and Tract Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3. Macheke opita ku mpingo wanu azilembedwa kuti ndalamazo apatse mpingowo.
◼ Kuyambira ndi mabuku amene titumize mu July, mafomu a mpingo amene amatumizidwa chaka ndi chaka akhala akutumizidwa ku mipingo mafomuwo akakhalapo. Malangizo ofotokoza za kugaŵa mafomuŵa tidzawasonyeza pa mpambo wolongedzera mabuku. Ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mtumiki wa mabuku ayenera kuonetsetsa kuti mpingo uliwonse walandira mafomu ake akangofika kumene.
-
-
Kodi Mudzapezekapo?Utumiki wa Ufumu—2004 | May
-
-
Kodi Mudzapezekapo?
1 Munthu wina amene wakhala Mboni kwa nthaŵi yaitali anati: “Ngati muphonya tsiku loyamba la msonkhano wachigawo, ndiye kuti mwaphonya zinthu zambiri zedi!” Chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti tsiku loyamba n’limene limakhala chiyambi cha phwando lalikulu lauzimu limene gulu la Yehova latikonzera. (Yes. 25:6) Kupezekapo kwathu kuyambira pachiyambi kumasonyeza kuti timavomereza mawu a wamasalmo akuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, tiyeni ku nyumba ya Yehova.”—Sal. 122:1.
2 Komabe, chaka chatha m’malo ena a Msonkhano Wachigawo wa “Patsani Mulungu Ulemerero,” chiŵerengero cha anthu patsiku Lachisanu chinali chochepa kwambiri poyerekezera ndi chiŵerengero cha tsiku Loŵeruka ndi Lamlungu. Zimenezi zikutanthauza kuti abale ambiri anaphonya mbali ya msonkhano imene inali ndi nkhani zofunika kwambiri zokhudza kupatsa Mulungu ulemerero. Komanso anadzimana mayanjano abwino ndi okhulupirira anzawo.
3 Musalole Ntchito Yakuthupi Kukulepheretsani: Kuopa kuchotsedwa ntchito chingakhale chifukwa chimene ena analepherera kupezeka pamsonkhano tsiku Lachisanu. Komabe, Mboni zambiri zaona kuti mabwana awo savuta pankhani imeneyi ngati apempheratu tchuthi nthaŵi ikadalipo. Bwana wina anachita chidwi kwambiri ndi mlongo wina amene anali mpainiya chifukwa cha chizoloŵezi chake chopezeka pamisonkhano yonse ya mpingo ndiponso yaikulu moti bwana wakeyo anakakhala nawo tsiku lathunthu pamsonkhano umene mlongoyu anapita!
4 Simuyenera kuganiza kuti abwana anu sangalole kukupatsani tchuthi, kapena kuganiza kuti kuphonya tsiku limodzi kulibe kanthu. Ndi chidaliro chonse, konzekerani kuwaonetsa mwaluso abwana anu kuchokera m’Malemba chifukwa chake kupezeka pamsonkhano kuli mbali yofunika kwambiri pa kulambira kwanu. (Aheb. 10:24, 25) Ndiyeno dalirani malonjezo a Yehova, pozindikira kuti zilizonse zimene mufuna zakuthupi zidzapatsidwa kwa inu ngati muika zinthu zauzimu pamalo oyamba m’moyo wanu.—Mat. 6:33; Aheb. 13:5, 6.
5 Chofunika kwambiri ndicho kuyamikira “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:10, 11, NW; Sal. 27:4) Izi zimatipangitsa kukonzekera kuti tipindule mokwanira ndi makonzedwe ofunika a Yehova ameneŵa. Yambani kukonzekera lero, ndipo tsimikizani kuti mudzapezekepo masiku onse atatu!
-
-
Kugaŵira Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi WalusoUtumiki wa Ufumu—2004 | May
-
-
Kugaŵira Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
◼ “Kodi mukuganiza kuti dziko likanakhala labwinopo anthu akanakhala kuti amatsatira mawu aŵa? [Ŵerengani Mateyu 7:12a. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Buku ili lili ndi zinthu zambiri zimene tingaphunzire kwa mphunzitsi waluso woposa onse amene anakhalako.” Sonyezani zithunzi ndi mawu ofotokoza zithunzizo pa mutu 17.
◼ “Makolo ambiri masiku ano amayesetsa kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zofunika? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 22:6.] Onani kuti makolo akulimbikitsidwa kuyamba kuphunzitsa ana awo ali aang’ono. Buku ili lakonzedwa kuti liwathandize kuchita zimenezo.” Sonyezani zithunzi ndi mawu ofotokoza zithunzizo pa mutu 15, 18, kapena 32.
◼ “Nthaŵi zambiri makolo amadabwa ndi mafunso amene ana awo amafunsa. Ena mwa mafunsowo amakhala ovuta kuyankha, si choncho kodi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani 2 Timoteo 3:14, 15.] Amayi a Timoteo ndi agogo ake akazi anam’phunzitsa zimene Malemba amanena kuyambira ali khanda. Buku ili lingathandize makolo kuchita zomwezo kwa ana awo masiku ano.” Sonyezani zithunzi zingapo ndi mawu ofotokoza zithunzi pa mutu 11 ndi 12 kapena 34 mpaka 36.
-