Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/04 tsamba 4
  • ‘Lemekezani Yehova ndi Chuma Chanu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Lemekezani Yehova ndi Chuma Chanu’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 12/04 tsamba 4

‘Lemekezani Yehova ndi Chuma Chanu’

1 Mawu amenewa akunena thandizo limene timapereka pa ntchito yolalikira ya padziko lonse. (Miy. 3:9) Kupatulapo kuchita nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa mwachindunji, timalemekezanso Yehova pogwiritsa ntchito mwanzeru chuma chathu. Mwachitsanzo, mu Israyeli wakale ankati pakafunika ndalama za ntchito yapadera, monga zomangira chihema ndiponso kachisi, anali kungopereka chilengezo ndipo anthu anali kupereka mowolowa manja mwakuti nthawi zina anali kupereka zochuluka mpaka zina ‘kutsala.’ Timakumbukiranso kuti Yesu ndi ophunzira ake anali kusunga thumba kapena bokosi la ndalama mmene anali kutengamo ndalama zothandizira osauka ndiponso kugulira zofunika zina.—Eks. 36:5-7

2 Masiku anonso, Mboni za Yehova zimatengerabe zitsanzo zimenezi za anthu akale amene anagwira ntchito molimbika ndiponso kupereka mowolowa manja. N’chifukwa chake mpingo uliwonse uli ndi mabokosi a zopereka, amene kawirikawiri amakhala kumbuyo m’Nyumba za Ufumu ndipo amakhala pamalo oonekera. Mabokosi a zopereka ayeneranso kukhalapo pa malo osiyanasiyana a phunziro la buku. Ndalama zopezeka pa Nyumba ya Ufumu ndi m’maphunziro a buku zimagwiritsidwa ntchito kusamalira Nyumba ya Ufumu kapena kupititsira patsogolo zinthu za Ufumu mogwirizana ndi mmene mpingo unganenere. Kodi mpingo wanu uli nawo mabokosi a zopereka amene wina aliyense akhoza kupitako ndi kupereka zilizonse zimene akufuna popanda kukakamizika?—2 Maf. 12:9, 10; Luka 21:1.

3 Kuwonjezera pamenepa, palinso ndalama za Sosaite za ntchito ya padziko lonse zimene mpingo umasamalira kudzera mwa mkulu kapena mtumiki wotumikira wosankhidwa ndi bungwe la akulu. N’zodandaulitsa kuti mipingo ina imalephera kusunga bwinobwino mafaelo ake. N’chifukwa chake mfundo zimene zili m’mafunso ndi mayankho otsatirawa zikhala zothandiza kwambiri.

Msonkhano uliwonse ukatha, abale awiri ayenera kutsegula bokosi la zopereka ndi kuwerenga ndalama zimene zili mmenemo. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

Njira imeneyi imapereka chitsimikizo kwa onse kuti ndalama zimene akupereka zikusamalidwa bwino. Tiyenera kukhala ndi nkhawa yonga imene mtumwi Paulo anali nayo pamene anali kusamalira zopereka zaufulu zimene mipingo inapereka kuthandiza abale a ku Yudeya. Taonani zimene zalembedwa pa 2 Akorinto 8:19-21. Mu vesi 19 mtumwi Paulo analankhula za Tito amene anamusankha kuti apite naye limodzi “m’chisomo ichi,” kapena kuti popereka mphatso zachifundo. N’chifukwa chiyani anachita zinthu mwanjira imeneyi? Paulo akuyankha mu vesi 20 ndi 21 mwa kusonyeza kuti zimathandiza kuti abale asakayikiridwe popanda maziko ngati ndalama zasowa.

Kodi tiyenera kuchita nawo chiyani malisiti amene timalemba tikamaliza kuwerenga ndalama?

Lisiti limodzi losainidwa ndi abale onse awiri liyenera kuperekedwa kwa mlembi, ndipo lisiti lina liyenera kuikidwa pamodzi ndi ndalama kuti mtumiki wa maakaunti akaliike m’faelo. Zimenezi ziyenera kuchitidwa ponse pawiri, potenga zopereka za pa Nyumba ya Ufumu ndi za kumalo a Maphunziro a Buku a Mpingo.

Kodi n’zololeka kwa aliyense kukongola ndalama za mpingo?

Ndalama zoperekedwa ndi za mpingo wonse. Palibe munthu amene payekha angalamule mmene ndalamazi ziyenera kugwiritsidwira ntchito. Ngakhale kuti bungwe la akulu limasankha kulipirira zinthu zimene mpingo umafunikira nthawi ndi nthawi, koma pakafunika kulipirira zinthu zina zapadera, akulu amatengera nkhani imeneyi ku mpingo wonse kuti uvomereze. “Kukongola” ndalama zimenezi ngakhale pakagwa zovuta ndi kuba.—Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1994, masamba 19 ndi 20.

4 Ndi mwayi wamtengo wapatali kuthandiza nawo kulipira zosowa za mpingo ndiponso kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu. Komabe, sitifuna ngakhale m’pang’ono pomwe kuchita ngati tikupemphetsa ndalama moti abale n’kuona ngati tikuwakakamiza, koma zimene tikufuna n’zoti adziwe mmene mpingo umachitira zinthu ndiponso mwayi umene ali nawo pa nkhani imeneyi. Abale alinso ndi mwayi wothandiza nawo pa ntchito yosamalira woyang’anira dera ndi woyang’anira chigawo mwa kuwapatsa malo ogona ndi zakudya nthawi zonse. Zonsezi zili mwayi wa utumiki ndipo zimangofunika mzimu wofunitsitsa. Ndiyetu tiyeni titenge nawo mbali popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu m’gawo lathu mwa zopereka zathu zaufulu ndiponso kuonetsetsa kuti zolembedwa za maakaunti a mpingo zikusungidwa bwino. Tikatero tidzalemekeza Yehova ndi chuma chathu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena