Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/05 tsamba 6
  • Kuphunzira Bulosha la Dikirani!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzira Bulosha la Dikirani!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Mlungu wa May 23
  • Mlungu wa May 30
  • Mlungu wa June 6
  • Mlungu wa June 13
  • Mlungu wa June 20
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 4/05 tsamba 6

Kuphunzira Bulosha la Dikirani!

Kuyambira mlungu wa May 23 mpaka June 20, 2005, mipingo padziko lonse idzayamba kuphunzira bulosha la Dikirani! pa Phunziro la Buku la Mpingo. Gwiritsani ntchito mafunso otsatirawa pokonzekera ndi pochititsa msonkhano umenewu. Paphunziroli, muziwerenga nkhaniyo, ndipo muziwerenga malemba osagwidwa mawu ngati nthawi ilipo.

Mlungu wa May 23

◼ Tsamba 3 ndi 4: Mwa zochitika zimene azindandalika apazi, kodi ndi zochitika ziti zimene zakhudza moyo wanu kwambiri? N’chiyani chikukusonyezani kuti zochitika zimenezi si zochitika wamba?

◼ Tsamba 5: Kodi n’chifukwa chiyani mukukhulupirira kuti Mulungu amatiganiziradi? Kodi n’chiyani chimene chingasonyeze kuti za Mulungu zimatikhudza limodzinso ndi zimene akuchita?

◼ Tsamba 6 mpaka 8: Kodi Mateyu 24:1-8, 14 amati chiyani za tanthauzo la zimene zikuchitika m’dzikoli panopa? Malingana ndi mmene 2 Timoteo 3:1-5 akusonyezera, kodi panopa tikukhala m’nthawi zotani? Kodi anowa ndi masiku otsiriza a chiyani? N’chifukwa chiyani mukukhulupirira kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu? Kodi Ufumu umene timalalikira ndi chiyani?

◼ Tsamba 9 ndi 10: Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuganiza mosamala tikamasankha zochita tsiku ndi tsiku ndiponso zinthu zofunika kwambiri m’moyo? (Aroma 2:6; Agal. 6:7) Mukamawerenga mafunso amene ali patsamba 10, mumakumbukira malemba ati amene ayenera kukutsogolerani pa zochita zanu?

Mlungu wa May 30

◼ Tsamba 11: Kodi n’chifukwa chiyani aliyense payekha afunika kuwaganizira mafunso amene afunsidwa patsamba limeneli? (1 Akor. 10:12; Aef. 6:10-18) Kodi mayankho athu pa mafunso amenewa akusonyeza chiyani za mmene timaonera malangizo a Yesu amene ali pa Mateyu 24:44?

◼ Tsamba 12 mpaka 14: Kodi “nthawi ya chiweruziro” yotchulidwa pa Chivumbulutso 14:6,7 ndi itiyo? Kodi ‘kuopa Mulungu ndi kum’patsa ulemerero’ kumatanthauza chiyani? Kodi Babulo Wamkulu n’chiyani, ndipo n’chiyani chidzamuchitikire? Kodi tikufunika kuchitanji panopa ngati tili mu Babulo Wamkulu, kapenanso ngati tinachokamo kale? Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe zikuphatikizidwa m’nthawi ya chiweruzo yonenedweratuyo? Kodi kusadziwa kwathu ‘tsiku ndi nthawi’ ya chiweruzo cha Mulungu chimene ananeneratu kumatichititsa chiyani? (Mat. 25:13)

◼ Tsamba 15: Kodi nkhani ya ulamuliro tingaifotokoze bwanji, ndipo kodi imatikhudza bwanji aliyense payekha?

◼ Tsamba 16 mpaka 19: Kodi “miyamba yatsopano” ndi “dziko latsopano” n’chiyani? (2 Pet. 3:13) Kodi ndani akulonjeza zinthu zimenezi? Kodi miyamba yatsopano ndi dziko latsopano zidzabweretsa kusintha kotani? Kodi ifeyo aliyense payekha tidzapindula nazo zinthu zimenezi?

Mlungu wa June 6

◼ Tsamba 20 ndi 21: Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani kwa otsatira ake a m’zaka 100 zoyambirira lokhudza kuthawa? (Luka 21:20, 21) Kodi kuthawa kumeneko kunali kotheka panthawi iti? N’chifukwa chiyani anafunika kuthawa mofulumira popanda kuzengereza? (Mat. 24:16-18, 21) Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri samvera machenjezo? Kodi anthu masauzande ku China ndi ku Philippines anapindula bwanji chifukwa chomvera machenjezo odalirika? N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kumvera chenjezo la Baibulo la kutha kwa dongosolo la zinthu lilipoli? Popeza nthawi yatha, kodi tili ndi udindo wanji? (Miy. 24:11, 12)

◼ Tsamba 22 ndi 23: Ku Australia mu 1974 ndi ku Colombia mu 1985, n’chifukwa chiyani anthu anakana kumvera machenjezo onena za tsoka limene linali kudzachitika, ndipo zotsatira zake zinali zotani? Kodi mukanakhala inu, mukuganiza kuti mukanatani mutamva machenjezo amenewa, ndipo mukanachita zimenezo chifukwa chiyani? Kodi n’chiyani chingasonyeze kuti tikanamvera chenjezo m’tsiku la Nowa? N’chifukwa chiyani anthu anafuna kukhala mu Sodomu wakale ndi malo ozungulira? Kodi tingapindule bwanji poganizira mozama zimene zinachitika mu Sodomu?

Mlungu wa June 13

◼ Tsamba 24 mpaka 27: Gwiritsani ntchito “Mafunso Ogwiritsa Ntchito Pophunzira” amene ali patsamba 27.

Mlungu wa June 20

◼ Tsamba 28 mpaka 31: Gwiritsani ntchito “Mafunso Ogwiritsa Ntchito Pophunzira” amene ali patsamba 31.

Kuphunzira bulosha limeneli kudzatithandiza kukhala ‘odikira’ ndi okonzekeratu. Tiyeni tionetsetse kuti utumiki wathu nthawi zonse ukusonyeza kuti uthenga umene angelo akulalikira wakuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake,” ndi wofulumira kwambiri.—Mat. 24:42, 44; Chiv. 14:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena