Kuimba Zitamando Ndi Mbali Yofunika ya Kulambira Kwathu
1. (a) N’chifukwa chiyani kuimba kuli kofunika pa kulambira kwathu? (b) Kodi ena asonyeza motani kuti salemekeza mbali imeneyi?
1 Kulemekeza Yehova mwa kuimba nyimbo zomutamanda, ngati mmene Yesu ndi atumwi ake anachitira, ndi mbali yofunika pa kulambira kwathu. (Marko 14:26) Kuimba kumatipatsa mwayi wosonyeza mmene timaonera Mlengi wathu. (Sal. 149:1, 3) Komabe, abale ndi alongo ena asonyeza kuti salemekeza mbali yofunika imeneyi ya kulambira kwathu. Kodi asonyeza motani zimenezi? Mwa kufika mochedwa pamisonkhano yampingo ndi misonkhano ikuluikulu popanda zifukwa zenizeni. Amafika pamisonkhanoyi pambuyo pa nyimbo ndi pemphero loyamba. Ena asonyeza kuti salemekeza mbali imeneyi chifukwa choti saimirira ndipo saikirapo mtima n’komwe kuti aimbe bwino nyimbo za Ufumu, pamene angathe kutero.
2. (a) Kodi Mawu a Mulungu amatilamula zotani pankhani yomutamanda kudzera m’nyimbo? (b) Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wasonyeza motani kufunika kwa kuimba monga mbali ya kulambira kwathu?
2 M’Mawu a Mulungu muli malo ambiri otilamula kuti timuimbire zitamando. Mwachitsanzo, pa Yesaya 42:10 timamvapo kuti: “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.” (Onaninso Salmo 96:1; 98:1.) Mogwirizana ndi zimenezi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anakonza zoti tikasonkhana, pamisonkhano yampingo, yadera, ndi yachigawo, tiziimba nyimbo za Ufumu.—Mat. 24:45.
3. Kodi ndi malangizo ati amene angatithandize kuti tiziimba bwino? (Onaninso bokosi patsamba 6.)
3 Tonse Tingathe Kuimba Bwino: Mfumu Davide inali yodziwa kuimba. Taonani malangizo oyenerera omwe inapereka. Inati: ‘[Yesetsani, NW] kuimba mwaluso momveketsa mawu.’ (Sal. 33:3) Pankhaniyi, palibenso china chimene Yehova amafuna kwa atumiki ake onse, koposa kuti ‘tiyesetse.’ Achikulire ena amachita manyazi kuimba pamisonkhano. Komatu ngakhale amatero, kuimba ndi mbali ya kulambira kwathu, ngati mmene zilili ndi utumiki wa kumunda. (Aef. 5:19) Timayesetsa kuti tilemekeze Yehova mu utumiki wa kumunda. Kodi sitingathenso kumulemekeza mwa kukweza mawu athu, kaya ndi osalala kapena ayi, n’kuimba mochokera pansi pa mtima nyimbo zomutamanda?—Aheb. 13:15.
4. Kodi mipingo ingachite chiyani kuti iziimba nyimbo motsatira matepi?
4 Abale athu padziko lonse amayamikira abale ndi alongo a ku Africa kuno chifukwa chakuti timaimba bwino kwambiri nyimbo za Ufumu popanda zida zoimbira. Komabe m’pofunikanso kuti tiphunzire kuimba motsatira malimba amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anakonza. Ngakhale kuti si mipingo yonse imene ili ndi magetsi kapena zipangizo zokuzira mawu, ena aitanitsa nyimbo za Ufumu zoti azigwiritsa ntchito pa misonkhano ya mpingo wawo. Mbale amabweretsa wailesi yakaseti yoyendera mabatire, n’cholinga chothandiza mpingo kuti uimbe motsatira matepi.
5. Kodi ana athu angapindule bwanji akaphunzira kuimba nyimbo za Ufumu mosangalala ndi mochokera pansi pa mtima?
5 N’kopindulitsa Kwambiri: Kuimba mokweza, mochokera pansi pa mtima, n’kopindulitsa kwambiri. Mwa kuimba, aliyense amachita nawo mbali yaikulu pa kulambira. Nthawi zambiri, makolo omwe alimbikitsa ana awo kuti aziimba nyimbo za Ufumu mosangalala, mochokera pansi pa mtima ndiponso mozindikira zomwe akuchita, aona kuti kuimba koteroko kumawathandiza anawo kukula mwauzimu. Kodi mumachita zimenezi m’banja mwanu? Pamisonkhano yampingo ndi pamisonkhano ikuluikulu anthu omwe aima nafe pafupi amalimbikitsidwa kuimba mokweza akamva kuti ifeyo sitikuimba mwamanyazi. Ifeyo ‘tikamayesetsa,’ nawonso mpingo wonse umapindula, chifukwa chakuti mwachibadwa ena amakweza mawu akamva anzawo akutero.
6. Kodi kuimba mochokera pansi pa mtima kumapereka motani umboni wabwino?
6 Anthu amene abwera koyamba pamisonkhano yathu, komanso odutsa m’njira pafupi ndi Nyumba za Ufumu zathu ndiponso anthu okhala moyandikana ndi nyumbazi, amachita chidwi ndi kaimbidwe kathu kabwino. Nthawi ina m’mbuyomu, Nsanja ya Olonda inafotokozapo nkhani iyi: ‘Mkazi wina . . . anapita [yekha] kwa nthawi yoyamba ku Nyumba ya Ufumu . . . ndipo anakhalako misonkhano yonse iwiri. Pamene mpingo unkaimba . . . [nyimbo yakuti] “Yang’ananibe Maso Anu Pamphotho!,” iye anachita chidwi kwambiri ndi mawu [a nyimboyi] ndiponso mmene anaimbidwira moti anaona kuti amenewa ndiwo malo amene ankafuna kukhalako. Pambuyo pake anafikira mmodzi wa Mboni zomwe zinalipo ndi kupempha phunziro la Baibulo, ndipo anapita patsogolo nakhala mboni yachikristu ya Yehova.’
7. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamanyalanyaze kuimba nyimbo za Ufumu?
7 Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kumva anthu akuimba, makamaka akamaimba nyimbo zomutamanda ndi kumuyamikira. Motero sitiyenera kunyalanyaza kuimba nyimbo za Ufumu pamisonkhano yathu yosiyanasiyana. Pamisonkhano yathu yambiri, pamakhala mipata yocheperapo yoti omvera afotokoze maganizo ndi kuyamikira kwawo. Koma tonsefe tingafotokoze mmene timaonera ubwino wa Yehova mwa kuimba nawo nyimbo za Ufumu mochokera pansi pa mtima. Kunena zoona, ngati timayamikira kwambiri ubwino ndi kukoma mtima kwa Yehova, tidzaimba ndi mtima wonse nyimbo zomutamanda. Chofunika kwambiri n’chakuti tikamaimba bwino, Yehova, yemwe anayambitsa nyimbo ndi kuimba, ndiponso ndi woyenerera kutamandidwa kudzera mu nyimbo kuposa wina aliyense, adzatamandidwa koposa.
[Bokosi patsamba 6]
Nazi zina mwa mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti muziimba bwino:
◼ Konzekerani kuti muzifika pamisonkhano nthawi yoyambira misonkhanoyo isanakwane.
◼ Ngati mungathe, imirirani poimba nyimbo. Mwina mwaona kuti chithunzi chomwe chili kumapeto kwa mabuku athu a nyimbo a zikuto zolimba chili ndi oimba a pakachisi ophunzitsidwa bwino kuimba, omwe aimirira poimba bwino za kumtima kwawo ndi kutamanda Mulungu.
◼ Pampingo ndiponso kunyumba, phunzirani kuimba nyimbo zomwe zakonzedwa kuti ziimbidwe pa misonkhano ya mlungu ndi mlungu ndiponso ikuluikulu, mwa kugwiritsa ntchito matepi ngati n’zotheka.
◼ Popeza kuti mawu a nyimbo zathu za Ufumu n’ngatanthauzo kwambiri, tifunika tiziika maganizo athu pamawuwo tikamaimba. Ngati tikugwiritsa ntchito matepi a nyimbo za Ufumu pamisonkhano ya mpingo, m’pofunika kukweza tepiyo kuti onse omwe akuimba azimva bwinobwino.
◼ Munthu amene akutchula nambala ya nyimbo yoti iimbidwe, ayenera kutchulanso mutu ndi Lemba lotsogolera nyimboyo, ndipo mwinanso angafotokoze mmene ikugwirizanirana ndi nkhani yomwe iphunziridwe kapena yomwe yaphunziridwa pamsonkhanopo, m’malo mongotchula nambala chabe.