Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/06 tsamba 4
  • Kodi Mumachititsa Phunziro la Baibulo la Banja Nthawi Zonse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumachititsa Phunziro la Baibulo la Banja Nthawi Zonse?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 8/06 tsamba 4

Kodi Mumachititsa Phunziro la Baibulo la Banja Nthawi Zonse?

1 Makolo onse omwe anadzipereka kutumikira Yehova, amafuna kuti ana awonso adzafike pofuna kupereka moyo wawo kwa Yehova ndi kukhala Mboni zobatizidwa. Makolo otere amafuna kudziwa kuti ana awo ali n’chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu, umene uli “moyo weniweniwo,” ngati mmenenso iwo amayembekezera.—1 Tim. 6:19.

2 Potuma ophunzira ake kuti “phunzitsani anthu a mitundu yonse,” Kristu Yesu sanapatulepo ana. (Mat. 28:19, 20) Tonse tikudziwa kuti Yesu ankakonda ana ndipo anali kuwadera nkhawa moti anachita kuuza ophunzira ake kuti am’bweretsere anawo. Ophunzira a Yesu anachita chidwi kwambiri ndi nkhaniyi moti anailemba m’mabuku atatu a Mauthenga Abwino.—Mat. 19:13-15; Marko 10:13-16; Luka 18:15-17.

3 Ngati makolo akuderadi nkhawa tsogolo la ana awo, afunika kuyesetsa kuchita chilichonse chomwe angathe kuthandiza anawo kuti akhale ophunzira a Kristu Yesu. Izi zikuphatikizapo kuwaphunzitsa Baibulo mlungu ndi mlungu, pogwiritsa ntchito zofalitsa zosiyanasiyana za kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, makamaka zimene analembera ana. N’zoona kuti akulu ndi atumiki othandiza amafunikira kuphunzira ndi akazi awo komanso ana awo nthawi zonse, chifukwa chakuti amafunika kuchita zimenezi pokwaniritsa udindo wawo. Komabe aliyense amene ali mutu wabanja ndipo amafunadi kusamalira bwino banja lake afunikiranso kuchita chimodzimodzi ndi banja lake. (1 Tim. 3:4, 5, 12) Mwa kuchititsa phunziro la Baibulo la banja nthawi zonse, makolo achikristu angadzakhale ndi mwayi woona kuti ‘ana awo akuyendabe m’choonadi.’—3 Yoh. 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena