Nyimbo 22
Kulabadira Uthenga wa Yuda
(Yuda 21)
1. Timalimbikitsidwa
Ndi Mawu a Yuda.
Analembera ife
Kutitu tisagwe.
Uphungu wake wabwino
Utilimbikitsedi.
Udzatigalamutsa ndithu (mudzikoli).
2. Machenjezo amphamvu
Asonya choipa.
Satana ngwochenjera
Koma timdziŵadi.
Angatitayitse mphotho;
Mwamawudi onyenga,
Amayesa kutivulaza (tisamale)!
3. Mochenjera oipa
Angatinyengedi.
Tikusankha Mulungu,
Tisasocheretu.
Kutigalamutsa, mawu
A Yuda ngothandiza!
Choncho tidzapeŵa mpatuko (titerodi).
4. Inde, timenye nkhondo
Yachikhulupiro.
Chifundo, chikondi ndi
Mtendere zikule.
Kwa Yehova M’lungu wathu,
Mwa Yesu Mfumu yathu,
Tonse tipereke ulemu (kwa Yehova).