Nyimbo 161
Pempherani kwa Yehova Tsiku ndi Tsiku
1. Pempherani kwa Yehova Wathu.
Ndimwaŵi kukhala ndi dzinalo.
Tiri ndi ufulu wolankhula;
Ndiye Tate yemwe tingapemphe.
M’pempherebe kwa M’lungu.
2. Pempheranitu tsiku ndi tsiku,
Kumapempha chikhululukiro.
M’zonse timampempha chithandizo;
Amateteza sitidzawopa.
M’pempherebe kwa M’lungu.
3. Pempheranitu ngati zavuta.
Tingampatsetu mitima yathu,
Kumuuza nkhaŵa zathu zonse;
Iri tsono ndidalitso lathu.
M’pempherebe kwa M’lungu.
4. Pempheranitu m’kumathokoza.
Mtamandeni ndi kum’yamikira.
Lankhulani ndi Yehova mo’na,
Natidzawona ubwino wake.
M’pempherebe kwa M’lungu.