“Nthawi Zonse Mawu Anu Azikhala . . . Okoleretsa ndi Mchere”
1. Kodi ‘kukoleretsa mawu athu ndi mchere’ kumatanthauza chiyani?
1 “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoleretsa ndi mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akol. 4:6) Kukoleretsa mawu athu ndi mchere kumatanthauza kusankha mawu oyenera ndi kunena zinthu m’njira yosakhumudwitsa anthu ena. Kuchita zimenezi pamene tili mu utumiki n’kofunika kwambiri.
2. Kodi n’chiyani chinathandiza kuti Yesu athe kulalikira mayi wachisamariya?
2 Chitsanzo cha Yesu: Nthawi ina akupuma pafupi ndi chitsime, Yesu analankhula ndi mayi wachisamariya amene anabwera kudzatunga madzi. Ali m’kati molankhulana, mayiyo anatchula kangapo zinthu zosonyeza kuti Ayuda ndi Asamariya anali pa udani kwa zaka zambiri. Mayiyo anafotokozanso kuti ankakhulupirira kuti Asamariya ndi mbadwa za Yakobo, ngakhale kuti Ayuda ankati Asamariya ndi mbadwa za anthu akunja. M’malo moyamba kutsutsana naye, Yesu analankhula zinthu zabwino zokhazokha. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu athe kulalikira zinthu zimene zinapindulitsa mayiyo ndi anthu ena a mumzinda wake.—Yoh. 4:7-15, 39.
3. Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha Yesu pamene tili mu utumiki?
3 Tikamalalikira tizikumbukira kuti cholinga chathu ndi ‘kulengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino.’ (Aroma 10:15) Tifunika kuuza eninyumba zinthu zosangalatsa ndi zolimbikitsa zochokera m’Baibulo, m’malo mooneka ngati tikufuna kutsutsa zinthu zimene iwo amakhulupirira. Ngati atchula mfundo ina yolakwika, tisathamangire kuwatsutsa. Pazinthu zimene anenazo, kodi pali mfundo ina imene tingagwirizane nayo kapena tingagwiritse ntchito powayamikira mochokera pansi pamtima? Mwinamwake pofuna kuwerenga nawo lemba tinganene kuti, “Kodi munayamba mwaganizapo za mfundo iyi?”
4. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati mwininyumba akutichitira mwano?
4 Nanga bwanji ngati mwininyumba akulankhula nafe mwamwano kapena akuchita kuonekeratu kuti akungofuna kutsutsana nafe? Tiyenera kupitiriza kukhala odekha ndi ofatsa ngakhalenso mu zolankhula zathu. (2 Tim. 2:24, 25) Ngati munthuyo alibe chidwi ndi uthenga wa Ufumu, ndi bwino kupeza njira yabwino yochokera panyumba pakepo.—Mat. 7:6; 10:11-14.
5. Kodi ndi zinthu zotani zimene zinachitikira mlongo wina chifukwa cholankhula mofatsa?
5 Pamakhala Zotsatira Zabwino: Mlongo wina anayesa kulalikira mayi wina woyandikana naye nyumba, koma mayiyo anakwiya kwambiri ndi kuyamba kum’tukwana. Mlongoyo analankhula mokoma mtima kuti: “Pepani kuti ndakukhumudwitsani. Tsalani bwino.” Patatha milungu iwiri, mayi uja anakagogoda pakhomo pa mlongoyo. Anam’pepesa ndipo anayamba kumvetsera zimene mlongoyo ankafuna kumuuza. Mayankhidwe ofatsa nthawi zambiri amakhaladi ndi zotsatira zabwino.—Miy. 15:1; 25:15.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kulankhula mawu okoleretsa tikakhala mu utumiki?
6 Yesetsani kulankhula mawu okoleretsa polengeza uthenga wabwino. Ngakhale ngati mwininyumba sakufuna kumvetsera, mwina angadzafune kumvetsera ulendo wina Mboni za Yehova zikadzafikanso panyumba pake.