Nyimbo 85
Yehova Ndiye Pothaŵirapo Pathu
1. Yehova pothaŵira,
Tidalira iye.
Mthunzi wakewo ndiwo;
Pobisala pathu.
Adzakupulumutsani
Kuchokera kumiliri.
Yehova ndiye linga,
Kwa olungama onse.
2. Nkana zikwi zidzagwa,
Pafupi ndi iwe,
Zikwi khumi kumanja;
Sudzavulazidwa.
Sudzagwedera ndi mantha,
Monga kuti nkuvulala.
Udzawona ndi maso,
Pokhala m’mapikomo.
3. Mliri sudzakugwera,
Ngakhaletu tsoka.
Mwa angelo Mulungu
Adzatchinjiriza.
Sudzawopa konse mkango;
Udzapondereza njoka.
Sudzakhumudwa konse
Potumikira M’lungu.
4. Ka’mba ka chidaliro;
Tamani Yehova.
Podziŵitsa ubwino,
Tipeŵa chitonzo.
Tidzipereke kwa M’lungu;
Adzatipulumutsatu.
Yehova pothaŵira,
Dzina lake ndi linga.